Republic of Zambia
MINISTRY OF EDUCATION
PRIMARY EDUCATION
LITERACY AND LANGUAGE
M’CINYANJA
BUKU LOTHANDIZILA MPHUNZITSI
GILEDI 1: TEMU 3
Developed by the Curriculum Development Centre
Lusaka
April 2025
1
UMWINI
Umwini wonse ndi wotetezedwa. Osalembanso bukuli kapena zigawo zake mnjila ina iliyonse
popanda cilolezo cocokela kwa eni ake a Curriculum Development Center.
© Curriculum Development Center
Linasindikizidwa koyamba m’Cinyanja
mu 2025 ndi a Curriculum Development Center.
First Published 2025 by
Zambia Educational Publishing House
Light Industrial Area
Chishango Road
P. O. Box 32708
Lusaka, Zambia
Printed by:
Zambia Educational Publishing House (ZEPH)
2
MASOMPHENYA
Maphunzilo ophindulitsa moyo wonse wamunthu, omwe apezeka mosabvuta, opelekedwa
mopanda tsankho, ndiponso othandiza popeleka zotsowa zonse zopindulitsa munthu molingana
ndi m’mene maphunzilo amaiko ena alili.
3
ALEMBI
Ms. Rabecca Tembo Head of Department, Nyamphande Boarding, Lusangazi
Joshua Zulu Lecturer, Chalimbana University, Chongwe
Belita Sakala Lecturer, Chipata college of Education, Chipata
Elizabeth Banda Mngoza Primary, Petauke
Jonathan Ngoma Kabvuma Primary School, Nyimba
Thomas Zulu Masomphenya Primary School, Lusangazi
Mary Phiri Kanjala Primary, Chipata
4
Zamkatimu
UMWINI ......................................................................................................................................................................... 2
MASOMPHENYA ............................................................................................................................................................ 3
ALEMBI .......................................................................................................................................................................... 4
Zamkatimu ..................................................................................................................................................................... 5
MAU OYAMBA ............................................................................................................................................................... 6
CIYAMIKO....................................................................................................................................................................... 7
LAMBULO....................................................................................................................................................................... 8
MOGWILITSILA NCHITO BUKULI .................................................................................................................................... 9
MATANTHAUZO A MAU .............................................................................................................................................. 10
CAPAMUTU 1: KULONGOSOLA MALO ......................................................................................................................... 13
CAPAMUTU 2: KUFOTOKOZA MAONEKEDWE A ZINTHU ............................................................................................ 41
CAPAMUTU 3: SEWELO ............................................................................................................................................... 69
CAPAMUTU 4 : KUKAMBA ZILAPI .............................................................................................................................. 101
CAPAMUTU 5 KUMVETSELA NDI KULANKHULA ........................................................................................................ 139
CAPAMUTU 6: KULOWEZA MAU OPINDA LILIME ...................................................................................................... 173
BIBLIOGRAPHY ........................................................................................................................................................... 207
5
MAU OYAMBA
Kubwela kwa maphunziro opindulitsa opatsa maluso ochedwa Competence Based Curriculum
(CBC) kwabweletsanso msintho pa kaphunzilidwe katsopano komanso kothandiza.
Maphunzilowa atsopano ali ndi zophunzitsila zomwe zimapangitsa aphunzi kukhala ndi maluso
amakono. Kusinthaku kuonetsanso ciyambi cotukula maphunzilo komanso kufunikila kwake.
Buku lophunzitsila Cinyanja geledi 1 yapangidwa mogwilizana ndi mfundo za amaphunzilo
omwe akufuna kulumikiza maphunzilo ndi umoyo watsiku ndi tsiku. Maluso onse omwe
apelekedwa mbuku yoonetsa ndondomeko yonse yamaphunzilo ya 2023 (Curriculum
framework) ndi wogwilizana ndi bukuli.
Colinga ca bukuli ndikuthandiza aphunzitsi a maphunzilo giledi 1 (primary Education) kucilikiza
maphunzilo atsopano a CBC Pamene mabuku ololedwa akali osowekela. Bukuli likuonetsa
kudzipeleka kosasunthika kwa cigawo ca zamaphunzilo kuti nchito ya aphunzitsi ikhale
yapafupi, pakupatsa ndondomeko ya uphungu, ntchito zoyeselela ndi mayeso ogwilizana ndi
zolinga za CBC. Komabe, aphunzitsi alimbikitsidwa kuonjezele zida zophunzitsila kupyolela
mkafuku-fuku kao kuti athane ndi zotsowekela zilizonse pomwe agwilitsa nchito CBC.
Ndikhulupilila kuti aphunzitsi azagwilitsa ncito buku limeneli moyenela.
Kelvin Mambwe (PhD)
Permanent Secretary-Education Services
Ministry of Education
6
CIYAMIKO
Buku lakuwelenga ndi kulemba m’Cinyanja lapangidwa kupyolela mkugawana nzelu ndi
kugwilila nchito pamodzi ndi ena. Anthu ambili, zigawo ndi mabungwe anafunsidwa ndi
kupatsidwa mpata woti apeleke maganizo ao pa uthenga womwe unafunika kukhala mbukuli.
Mwaico ndifuna kupeleka mathokozo anga kwa anthu , zigawo ndi mabungwe omwe anapeleka
thandizo ya ndalama ndi ukaswili wao kuti buku limeneli lophunzitsila lilembedwe moyenelela.
Awa ndi aphunzitsi, aphunzitsi amasukulu apamwamba kwambili, mabungwe oimilila
ziphunzitso (subject associations), Mabungwe akunja kwa boma ndi mabungwe ogwilizana nao.
Pomaliza, ndithokozanso anyanchito a cigawo ca Curriculum Development Centre
pakusimikizila kuti nchito yolemba bukuli yamalizidwa moyenela.
Charles K. Ndakala, (Dr.)
Director Curriculum Development
Ministry of Education
7
LAMBULO
Buku lophunzitsila aphunzi a geledi 1 lapangidwa mozama kuti lithandizile aphunzitsi
kuphunzitsa maphunzilo a Cinyanja mogwilizana ndi maphunzilo osinthidwa. Bukuli lapangidwa
molingana ndi ndondomeko yobvomelezeka ya kaphunzitsidwe ka Cinyanja ya caka ca 2023.
Ndondomeko imeneyi ikufuna kuwongolela kusiyana komwe kunapangidwa cifukwa ca kusowa
kwa mabuku obvomelezeka komanso kupatsa aphunzitsi zida zophunzitsila zothandiza, zocita,
ndi mayeso yopangidwa kulingana ndi kalasi la ophunzila ndi zosowa zao.
Cigawo ca zamaphunzilo cidziwa zobvuta zomwe zimabwela cifukwa cosintha maphunzilo.
Kusankha ndondomeko yamaphunzilo opatsa ana maluso osiyana-siyana (Competence Based
Curriculum) ndi ciyambi ca kusintha kopititsa patsogolo maphunzilo ndi kufunikila kwake.
Bukuli lionetsa kudzipeleka ndi cidwi ca cigawo ca zamaphunzilo kupanga nchito ya aphunzitsi
kuti ikhale yotheka pakuwapatsa ndondomeko ya uphungu, nchito ndi mayeso omwe alunjikidwa
ndi ndondomeko ya zolinga za maphunzilo atsopano. Komabe, aphunzitsi alimbikitsidwa kuti
naonso angathe kuwonjezela pakucita kafuku-fuku wawo komanso Kupanga zida zao
zophunzitsila kuti athane ndi zotsowa zina zomwe zingabuke pogwilitsa nchito ndondomeko
yatsopanoyi.
Zocita ndi mayeso zomwe zapelekedwa zapangidwa kuti zizilimbikitsa ndi kukulitsa maluso eni-
eni anchito zamanja ndi maluso oganiza mwakuya mwa aphunzi pomwe akuwonetsa kufunikila
kwa kugonjela msintho kumalo amaphunzilo osiyana-siyana. Aphunzitsi alimbikitsidwa
kugwilitsa nchito uphungu uwu mumakalasi awo osiyana-siyana ndi kufufuza njila zina
zololedwa, zobvomelezeka pakafunika kutelo. Kusintha kumeneku ndi kofunikila pakuonetsetsa
kuti aphunzi onse, ocokela kumalo osiyana-siyana aphindula ndi maphunzilo abwino atsopano.
Ciyembekezo ndi cakuti bukuli lidzakhala cida cofunikila kwambili kwa aphunzitsi pomwe
asewenzetsa ndondomeko yamaphunzilo atsopano yochedwa Competence Based Curriculum,
kukulitsa luso lao lopatsa aphunzi cidziwitso cokwanila cokhudza cilankhulo ca Cinyanja maluso
omwe angathandize aphunzi kukhala ndi cidwi comwe cingapangitse maphunzilo kukhala
aphindu.
8
MOGWILITSILA NCHITO BUKULI
Bukuli lipeleka uthenga womwe uyenela kuphunzitsidwa mu temu laciwili la giledi 1. Bukuli
ndilogawidwa mzigawo ndipo cigawo ciliconse cili ndi maphunzilo ocokela muzigawo zina
zosiyana-siyana zomwe ndi Kumvetsela ndi Kulankhula, kuwelenga, matanthauzo a mau,
mvetso, ndi kulemba. Uthenga womwe waikidwa mbukuli siunalembedwe mumaphunzilo
(lesson plans), koma uyenela kugwilitsidwa nchito kulemba maphunzilo (lessons). Popanga
maphunzilo, muyenela kutenga uthenga kucokela kuzigawo zosiyana-siyana kupanga phunzilo
limodzi. Mwacitsanzo, Phunzilo lingakhale ndi kumvetsela ndi kulankhula, matanthauzo a mau,
kuwelenga ndi kulemba. Popanga phunzilo, muyenela kusankha mfundo zophunzitsa zomwe
muzagogomezapo m’phunzilo ndi nchito zocita aphunzi pa luso lapadela lililonse. Apa
zikutanthauza kuti phunzilo linzakhala ndi maluso apadela oposa limodzi. Koma, mphunzitsi
adzasankha kuti ndi gawo iti yomwe adzagogomezapo mphunzilo lake ndi kuipatsa nthawi
yaitali koposa ena. Moonjezela, nchito zopatsidwa pa luso lapadela siziyenela kucitidwa zonse
mu phunzilo limodzi ai. Zimenezi zingacitidwe mumaphunzilo osiyana-siyana.
NJILA YOPHUNZITSILA
Kaphunzitsidwe kayenela kulondola njila yapang-ono-pang’ono yomwe inena kuti poyamba,
mphunzitsi acite nchito yoonetsela potsatila pake, acitile nchitoyo pamodzi ndi aphunzi ndipo
pothela aphunzi acite aliyense payekha (Gradual Release Model (GRM), Moonjezela, njila
zosiyana-siyana zakaphunzitsidwe ziyenela kugwilitsidwa nchito kuti zotsowa zosiyana-siyana
za aphunzi zikwanilitsidwe.
9
MATANTHAUZO A MAU
1. Asanayambe Kulemba- Pre-writing
2. Asanayambe kuwelenga- Pre-Reading
3. Capamutu-Theme
4. Cidule - Overview
5. Cigawo- Component / section
6. Lambulo-Introduction
7. Gwelo la Uthenga- Reference
8. Kayendetsedwe ka maso ndi katsegulidwe ka buku powelenga ndi
polemba-Directionality
9. Kudziwa za Zolembedwa-Concept of Print
10. Kuganiza mwakuya- Critical Thinking
11. Kusanthula maganizo Mwakuya- Analytical Thinking
12. Mgwilizano-Collaboration
13. Kukambitsilana- Communication
14. Kudziwa kugwilitsa nchito zinthu za kompyuta- Digital Literacy
15. Kupanga Zatsopano ndi kuonjezela pa zakale- Creativity and Innovation
16. Zokhuza mwini komanso ena- Emotional intelligence
17. Zamalonda- Entrepreneurship
18. Kuthetsa bvuto-Problem Solving
19. Kukambilana-Discussion
10
20. Kulemba cimodzi- cimodzi- Manuscript Form
21. Mau acikoka –Hook
22. Kulemba mokhotesa-Cursive Form
23. Kumvetsela ndi Kulankhula- Listening and Speaking
24. Kuzindikila Mvekelo- Phonological Awareness
25. Kuzindikila ubale wa lembo ndi Mvekelo- Phonemic awareness
26. Luso lapadela - Specific Competence
27. Luso Lonse-General Competence
28. Luso loyembekezeleka-Expected Standard
29. Malembedwe- Handwriting
30. Masilabe-Syllables
31. Chati yamasilabe- Syllabic Chart
32. Mau ofunika kwambili- Key terms
33. Mayeso-Assessment Activities
34. Mutu- Topic
35. Mutu waung’ono- Sub-Topic
36. Kasungidwe ka nyama- Animal farming
37. Mvekelo za zinthu zosiyana-siyana-Sounds made by different objects
38. Mwacidule- Summary
39. Nchito- Learning activities
40. Ocita Sewelo- Characters
11
41. Zinthu Zophunzilila ndi Zophunzisila- Teaching and Learning Materials
42. Zindikilani- Note
43. Zocita-Exercise
44 Ciyambi
45 Mau ofunikila kudziwa
46 Nchito
47 mwacidule
12
CAPAMUTU 1: KULONGOSOLA MAONEKEDWE A MALO
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa kulongosola malo osiyana-siyana. Kulongosola malo
kudzathandiza aphunzi kutukula luso la kumvetsela ndi kulankhula, kuzindikila matanthuzo a
mau omwe adzagwilitsa nchito m’maphunzilo ena.
CAPAMUTU 1: KUMVETSELA NDI KULANKHULA
Mutu: Kulongosola Maonekedwe
Mutu Waung’ono: Malo
Luso Lapadela: Kulongosola Malo.
Mau Ofunikila Kudziwa: Kulongosola, malo, kuzindikila
Mfundo Zophunzitsa:
● Kufotokoza za malo
● Kulongosola mbali za malo
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Mabuku, machati ndi zina
Nchito A: Apeleke mau omwe amagwilitsidwa nchito polongosola malo (Kukula,
kucepa, utali wa pansi ndi utali wa m’mwamba)
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kalongosoledwe ka mbali za malo.
● Onetsani zizindikilo za mbali za malo (mapili, mitengo, mitsinje, miseu)
● Fotokozani pamodzi ndi aphunzi za ukulu kapena kucepa kwa malo.
● Uzani aphunzi afotokoze za utali kapena ufupi wa malo.
II. Aphunzi:
13
● Aphunzile mbali za malo.
● Aphunzile zizindikilo za mbali za malo (mapili, mitengo, mitsinje, miseu)
● Amvetsele za ukulu kapena kucepa kwa malo.
● Amvetsele za utali kapena ufupi wa malo
● Alongosole zizindikilo za malo a kwao pakujambula.
Muyeso Woyembekezeleka: Mau olongosolela malo apelekedwa moyenela.
Nchito B: Kulongotsola malo kugwilitsa nchito mau azindikilidwa.
I. Mphunzitsi:
● Apeleke citsanzo cakalongosoledwe ka malo pogwilitsa nchito mau ozindikilidwa
polongosola malo mwakujambula.
● Gwilitsani nchito ndi aphunzi mau azindikilidwa polongosola malo a kunyumba kwao
mwa kujambula.
● Auze aphunzi kuti agwilitse nchito mau azindikilidwa polongosola malo a kusukulu kwao
mwa kujambula.
II. Aphunzi:
● Amvetsele bwino pomwe aphunzitsi akupeleka citsanzo cakalongosoledwe ka malo.
● Alongosole malo a kunyumba kwa pogwilitsa nchito mau azindikilidwa.
● Alongosole malo a ku sukulu kwao pogwilitsa nchito mau azindikilidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Mau azindikilidwa agwilitsidwa nchito moyenela polongosola
malo.
Nchito C: Kucita masewela olongosolela malo monga ukazitape ndi ndine yani.
I. Mphunzitsi:
14
● Phunzisani aphunzi kaseweledwe ka masewela aukazitape ndi ndine yani polongosola
mbali za malo.
● Ikani aphunzi m'magulu ndi kusewela nao masewela aukazitape ndi ndine yani
olongosolela mbali za malo.
● Funsni aphunzi kucita masewela aukazitape ndi ndine yani polongosola malo a
kunyumba ndi kusululu kwao m'magulu ao.
II. Aphunzi:
● Amvetsetse pomwe aphunzi akuphunsitsa maseweledwe a masewela aukazitape ndi
ndine yani polongosola mbali za malo.
● Asewele masewela aukazitape ndi ndine yani olongosolela mbali za malo.
● Acita masewela aukazitape ndi ndine yani polongosola malo a kunyumba ndi kusululu
kwao m'magulu ao.
● .
Muyeso Woyembekezeleka: Masewela olongotsola maonekedwe azinthu yaseweledwa
moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kulongosola malo pogwilitsa nchito mau
ozindikilidwa
KUWELENGA
MUTU 1: KUZINDIKILA MASILABE
Mutu Waung’ono 1: Kuzindikila masilabe opangidwa ndi gw-_, mf-_, ms-_, _oo-.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse masilbe amvekelo amalemba ophatikizana imodzi-
imodzi kufikila onse owonetsedwa pa mwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa
mophunzitsila masilabe gwa, gwe, gwi, gwo, gwu.
15
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa masilabe kucokela ku mau okambidwa, kusewela
masewela akuwelenga masilabe omwe ali mu mau pakuomba m’manja, ndi masewela akupanga
mau pa kusintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau atsopano.
Luso Lapadela: Kuzindikila ndi kusintha masilabe.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: zipangizo zogwilika.
Mau Ofunikila Kudziwa: masilabe, vawelo, mvekelo.
Mfundo zophunzitsa:
● Kuzindikila masilabe m’mau okambidwa.
● Kusewela masewela owelenga masilabe.
● Kusewela masewela opanga mau okambidwa kugwilitsa nchito masila.
● Kusewela masewela opanga mau posinthanisa ndi kucotsa masilabe.
Kumbukilani kuphunzitsa mamvekelo onse awa: (/gw/, /mf/, /ms/, /oo/).
Nchito A: Kuzindikila masilabe m’mau okambidwa
I. Mphunzitsi:
● Phunzitsani aphunzi kazindikilidwe ka masilabe m'mau.
● Zindikilani pamodzi ndi aphunzi kazindikilidwe ka masilabe m’mau opangidwa
Citsanzo: gwila = gwi ndi la
● Uzani aphunzi kuti azindikile masilabe m’mau okambidwa.
Gwada Gwa/wa, Gwapo gwa/po, Gwada gwada,
II. Aphunzi:
● Aphunzile kuzindikila masilabe.
16
● Aphunzitsi azindikile masilabe m’mau okambidwa pamodzi ndi aphunzi.
● Azindikile masilabe m’mau okambidwa.
Muyeso Woyembekeleka: Aphunzi azindikila masilabe m’mau okambidwa moyenela.
Nchito B: kusewela masewela akuwelenga masilabe
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi kaseweledwe ka masewela owelenga mau.
● Welengani mau omwe ali ndi masilabe gwa, gwe, gwi, gwo, gwu pamodzi ndi
aphinzi.
● Ikani aphunzi m'magulu ndipo muwauze kuti awelenge mau opatsidwa omwe ali
ndi masilabe gwa, gwe, gwi, gwo, gwu.
II. Aphunzi:
● Amvetsele pomwe aphunzitsi akuphunzitsa kawelengedwe ka mau.
● Awelenge mau omwe ali ndi masilabe gwa, gwe, gwi, gwo, gwu pamodzi ndi
aphunzitsi.
Citsanzo: Gwelo, gwaila, gwada, gwendeza
● Awelenge mau opatsidwa m'magulu ao.
Muyeso Woyembekezeleka: Masewela owelenga masilabe poomba m’manja acitidwa moyenela.
Nchito C: Kupanga mau okambidwa kugwilitsa nchito masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi kapangidwe ka mau pogwilitsa nchto masilabe opangidwa ndi
mvekelo /gw/.
● Pangani mau okambidwa pogwilitsa nchito masilabe ali ndi mvekelo /gw/ pamodzi
ndi aphunzi.
Citsanzo: Gwa/da = gwada, Gwi/la = gwila, Gwe/tsa = gwetsa
● Ikani aphunzi m'magulu ndipo muwauze kuti apange mau okambidwa pogwilitsa
nchito masilabe opangidwa ndi mvekelo /gw/
II. Aphunzi:
17
● Amvetsetse pomwe citsanzo cikupelekedwa.
● Apange mau pamodzi ndi aphunzitsi.
● Apange mau m'magulu ao omwe ali ndi masilabe opangidwa ndi mvekelo /gw/.
Muyeso Wombekezeleka: Mau okambidwa apangidwa moyenela pogwilitsa nchito masilabe.
Nchito D: kusewela masewela akusintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau
atsopano.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi mosinthila ndi mocotsela masilabe popanga mau ena.
● Yetselelani pamodzi ndi aphunzi kusinthanitsa ndi kucotsa masilabe m’mau
● Uzani aphunzi kuti akhale awili-awili ndipo asewele masewela opanga mau
atsopano posintha ndi pocotsa masilabe.
Citsanzo
KUSINTHA
1. Gwila = sinthani gwi, ikamponi gwe ndi kupanga Gwela
2. Gwadula = sinthani gwa ikani gwe kupanga gwedula
KUCOTSA
1. Gwilila = lila
2. Anagwada = gwada
● Uzani aphunzi kuti asinthe ndi kucotsa masilabe m’mau opatsidwa aliyense
payekha.
II. Aphunzi:
● Amvetsele bwino masinthidwe ndi macotsedwe amasilabe.
● Apange mau pamodzi ndi aphunzi posintha ndi pocotsa mvekelo monga mcitsanzo
cili pamwambapa.
● Asinthe ndi kucotsa masilabe m'mau opatsidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: kusintha ndi kucotsa masilabe kwacitika moyenela.
18
MUTU 2: Kupanga Masilebe.
Mutu Waung’ono 1: Masilabe.
Ciyambi: mutu uyu udzaona pakulumikiza malemba ndi mavawelo kupanga masilabe.
Luso Lapadela: kulumikiza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe
Mau Ofunikila Kudziwa: Makonsonanti, masilabe, mavawelo.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: mafulashi khadi, , silabiki chati
Mfundo Zophunzitsa:
● kupanga masilabe
● kulumikiza makonsonanti ndi mavawelo
Nchito A: Kupanga masilabe pa kulumikiza makonsonanti ndi mavawelo
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi kasakanizidwe kamakonsonanti ndi mavawelo popanga masilabe.
● Pangani masilabe ndi aphunzi kugwilitsa nchito makonsonanti ndi mavawelo kupanga
masilabe.
● Uzani aphunzi kuti apange makonsonanti ndi mavawelo pogwilitsa nchito mvekelo /gw/.
II. Aphunzi:
● Aonelele masakanizidwe a masilabe ndi mavelo pogwilitsa nchito makonsonanti ndi
mavawelo pogwilitsa nchito mvekelo /gw-/.
● Apange masilabe ndi aphunzitsi kugwilitsa nchito makonsonanti ndi mavawelo.
● Apange masilabe kulingana ndi makonsonanti omwe apatsidwa.
Zocita:
Aphunzi apange masilabe kugwilitsa nchito makonsonanti ndi mavawelo apatsidwa.
19
Gw/a, Gw/e, Gw/i, Gw/o, Gw/u
Muyeso Woyembekezedleka: Kusakaniza kwa makonsonanti ndi mavawelo kwacitidwa moyenela.
Nchito B : Kuwelenga chati yamasilabe.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani chati ya masilabe kwa aphunzi.
● Sonyezani kuwelenga masilabe ali pa chati.
● Uzani aphunzi awelenge masilabe.
● Thandizilani aphunzi kuwelenga m’magulu masilabe ali pa chati.
II. Aphunzi:
● Aone chati ya masilabe.
● Amvetsele kuwelenga masilabe ali pa chati.
● Awelenge masilabe.
● Awelenge m’magulu masilabe ali pa chati.
Zocita
1. Lembani masilabe osowa mwa awa.
gwa gwe ….. gwo gwu.
2. Welengani masilabe ali pa 1
Muyeso Woyembekezeleka: Chati ya masilabe yawelengedwa moyenela.
Nchito C : Kusankha masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Sankhani masilabe kucokela pa makhadi ya malembo.
20
● Udzani aphunzi kuti asankhe masilabe kucokela pa makhadi ya malembo
Citsanzo:
Gwila, gwa, bwela, gwada, gwe, gula, gwi, nzelu, gwu, mwana, gwo.
Yankho : gwa gwe gwi gwo gwu
II. Aphunzi:
● Aonelele masankhidwe a masilabe pakati pa malembo pakati pa malembo, mau ndi
masilabe.
● Asankhe masilabe pakati pa mau.
Zocita:
1. Sankhani masilabe kucokela pa malembo, masilabe ndi mau.
gwa, mwano, gwelo, gwada, gwe, gwila, gwo, bwela, gwu, gwi
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe asankhidwa moyenela.
Nchito D : Kusintha Masilabe
I. Mphunzitsi:
● Achule mau monga gwila
● Sonyezani kasinthidwe kamasilabe mu mau.
Citsanzo:
Gwila– khala– sinthani ‘gwi’ ikani ‘kha’ kupanga khala.
II. Aphunzi:
● Aone ndi kumvetsela kasinthidwe ka masilabe m’mau.
● apange mau atsopano pa kusintha masilabe m’magulu ao.
gwetsa – tsitsa— sinthani ‘gwe’ ikani ‘tsi’ kupanga ‘tsitsa’
21
gwelo — bwalo —- sinthani ‘gwe’ ikani ‘bwa’ kupanga bwalo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kusintha masilabe m’mau ndikupanga mau atsopano kwacitika
moyenela.
Nchito E: Kulumikidza malembo ophatikizana koma omveke mosiyana amakonsonanti
ndi mavawelo kupanga masilabe.
I. Mphunzitsi:
● pelekani citsanzo ca makonsonanti omwe sali ndi mvekelo imodzi kupanga masilabe
polumikiza ndi mavawelo.
Citsanzo:
a e i o u
gwa gwe gwi gwo gwu
II. Aphunzi:
● Aone citsanzo ca makonsonanti amwe sali ndi mvekelo imodzi
● Amvetsele molumikizila makonsonanti omwe sali ndi mvekelo imodzi ndi mavawelo
kupanga masilabe.
● m’magulu ao apange masilabe polumikiza makonsonanti omwe sali ndi mvekelo imodzi
ndi mavawelo kupanga masilabe.
Muyeso Woyembekezeleka: Malembo ophatikizana koma omveka mosiyana amakonsonanti
ndi mavawelo alumikizidwa ndi kupanga masilabe moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kupanga masilabe kucokela ku makonsonanti ndi
mavawelo, kuwelenga masilabe pa chati la masilabe, kusankha masilabe ndi kusintha malembo.
22
B. KUWELENGA
MUTU 1: Kupanga Mau ndi gwa, gwe, gwi, gwo , gwu
Mutu Waung’ono 2: Mau
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa kulumikidza masilabe kupanga mau, kusintha ndi kucotsa
masilabe kupanga mau atsopano, kuzindikila masilabe mu mau ndi kuwelenga masilabe.
Luso Lapadela 1: Aphunzi apange mau osiyana-siyana polumikidza masilabe.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Silabiki chati, mafulashi khadi
Mau Ofunikila Kudziwa: Makonsonanti, mavawelo, masilabe, kulumikidza
Mfundo Zophunzitsa:
● Kulumikidza masilabe kupanga mau
● Kusinthanitsa ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano ndi aphunzi
● Kupenda masilabe m'mau.
Nchito A Kulumikaza masilabe popanga mau
Mphunzitsi:
● Onettsani aphunzi mapangidwe a mau kugwilitsa nchito masilabe.
● Pangani ndi aphunzi mau kugwilitsa nchito masilabe.
● Uzani aphunzi kuti apange mau pogwilitsa nchito masilabe m’magulu ao.
Aphunzi:
● Aphunzile mapangidwe a mau.
23
● Apange masilabe ndi aphunzi
● Apange mau kugwilitsa nchito masilabe m’magulu ao.
1. Gwe/sa gwesa
2. Gwa/za gwaza
3. Gwa/po gwapo
Muyeso Wombekeleka: Masilabe aphatikizidwa kupanga mau moyenela
Nchito B: Kucotsa ndi kuika masilabe ena m’mau
I. Mphunzitsi:
● Onetsani kacotsedwe ndi kaikidwe ka masilabe m'mau.
● Ccotsani ndi kuika masilabe pamodzi ndi aphunzi
● Uzani aphunzi kuti acotse ndi kuika masilabe ali ndi mvekelo /gw/ m'magulu ao.
1. Gwawa gwada
2. Gwapo gwape
3. Kugwila gwila
II. Aphunzi:
● Aonelele mocotsela ndi kuika masilabe kupanga mau ena
● Apange mau ena pamodzi ndi mphunzitsi
● Apange mau ena pocotsa masilabe ena
Muyeso Woyembekezeleka: Nchito zopanga mau zakwanitsidwa moyenela
Nchito C: Kuzindikile masilabe m’mau.
I. Mphunzitsi:
● Onetsni aphunzi mazindikilidwe a masilabe m'mau.
● Citani nchito ndi aphunzi ya kuzindikila masilabe m’mau.
24
● Uzani aphunzi kuti azindikile masilabe onenedwa m’mau poika kamzele munsi mwa
silabe m'magulu ao.
II. Aphunzi:
● Aphunzile mozindikilila masilabe m'mau.
● Azindikile masilabe m’mau ndi aphunzitsi ndiponso okha.
Citsanzo
Gwa/mpo/ni, gwe/ lo, gwe/nde/ za
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe azindikilidwa moyenela.
Nchito D: Kuwelenga masilabe
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi kazindikilidwe ka masilabe m'mau.
● Welengani masilabe m’mau ndi aphunzi.
● Uzani aphunzi kuti azindikile nambala ya masilabe m’mau opatsidwa.
II. Aphunzi :
● Amvetsele bwino pomwe aphunzitsi akuphunzitsa kazindikilidwe ka mau.
● Awelenge ndi aphunzitsi masilabe ali m’mau.
● Azindikile nambala ya masiabe m’mau.
1. Gwadani 3
2. Gwamula 3
3. Gwaza 2
Muyeso Woyembekezeleka: Aphunzi azindikila namabala ya masilabe m’mau osiyana-siyana
moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kulumikidza masilabe kupanga mau, kusintha ndi
kucotsa masilabe kupanga mau atsopano, kuzindikila masilabe mu mau ndi kuwelenga masilabe.
25
Luso Lapadela 2: Kuwelenga mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau koyenela.
Nchito: Kuwelenga mau
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kuwelenga mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau koyenela
powelenga mau pa bolodi ndi pogwilitsa nchito timabuku ta nthano.
● Welengani ndi aphunzi mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau komveka bwino.
● Ikani aphunzi awili-awili ndi kuwauza kuti awelenge mau mofulumila ndi kachulidwe ka
mau koyenela monga m'citsanzo ca mphunzitsi.
II Aphunzi:
● Amvetsele bwino pomwe citsanzo cili kupelekedwaa.
● Awelenge mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau koyenela.
● Akhale m'magulu ndi kuwelenga mau monga m'citsanzo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga mau mofulumila ndi kuchulila mau komveka bwino
kwacitika moyenela.
Luso Lapadela 3: Kuwelenga ndime mokweza ndi kachulidwe ka mau koyenela.
Nchito A: Kuwelenga ndi kumvetsa ziganizo
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kuwelenga ndime mofulumila ndi kuonetsa kayankhidwe ka
mafunso kucokela ku ndime yowelengedwa.
● Welengani ndime pamodzi ndi aphunzi.
● Funsani aphunzi mafunso kucokela mu ndime yowelengedwa.
26
II Aphunzi:
● Amvetsele bwino pomwe aphunzitsi akuwelenga.
● Awelenge ndi kuyankha mafunso kucokela ku ndime yowelengedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga ndime mofulumila, kuimvetsetsa ndi kuyankha
mafunso kucokela m’ndimeyo kwacitika moyenela.
Nchito B: Kuwelenga ndime kucoka pa ziganizo ziwili (2) kufika pa ziganizo
zisanu (5) (kuwelenga kwa gulu, kubwelezela zomwe wina wawelenga kale, kuwelenga
awili-awili).
I Mphunzitsi:
● Welengani ndime mokweza pomwe aphunzi akumvetsela modekha.
● Welengani Pamodzi ndi aphunzi (Choral Reading).
● Uzani aphunzi kuti azibwelezela zomwe mphunzitsi akuwelenga (Echo Reading).
● Uzani aphunzi kuti awelenge awili-awili (Paired Reading).
II. Aphunzi:
● Amvetsele modekha pomwe aphunzitsi akuwelenga.
● Awelenge pamodzi ndi mphunzitsi,
● Abwelezele zomwe mphunzitsi akuwelenga.
● Awelenge awili-awili.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga ndime yokwanila mizela iwili kufika pa isanu
kwacitika moyenela
Nchito C: Kuzindikila zolembedwa zili ndi mvekelo zosiyana-siyana ndi zolumikidzana.
27
I. Mphunzitsi
● Pelekani mabuku omwe ali ndi nkhani zosiyana-siyana
● Onetsani mowelengela nkhani
● Welengani nkhani ndi aphunzi
● Uzani aphunzi kuti awelenge nkhani.
II. Aphunzi
● Alandile mabuku ali ndi nkhani zowelenga.
● Aonelele mowelengela
● Awelenge nkhani aliyense payekha.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga mokuwa ndime yomwe ili masilabe osiyana-siyana
kwacitidwa moyenela
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kuwelenga masilabe, mau ndi nkhani momveka
ndi kaculidwe ka mau koyenela.
MVETSO
MUTU 1: MVETSO YA KUMVETSELA
Mutu Waung’ono 1: Ganizo Leni-Leni.
Ciyambi: Mutu uyu udzayangana pa kuzindikila ndi kutulutsa ganizo leni-leni pa zomwe
amva.
Luso Lapadela: Azindikile ndi kupeleka maganizo leni-leni kulingana ndi zomwe zamva.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Makhadi a ziganizo, mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: Maganizo, mvetselo.
28
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuphunzitsa m’mene aphunzi angapelekele maganizo ao pa zomwe amva kapena
kuwelenga.
● Kuwelenga nkhani kwa aphunzi ndi kuwafunsa mafunso mwakulankhula cabe.
Kuuza aphunzi kuti apeleke cigamulo kulingana ndi zomwe amva.
Nchito A: Kuzindikila ndi kupeleka ganizo leni-leni pa zomwe amva
I. Mphunzintsi:
● Uzani aphunzi kuti amvetsele ku nkhani yapamtima yomwe izakambidwa kapena
kuwelengwedwa.
● Citani nchito ndi aphunzi ya kulingalila nkhani yakambidwa.
● Funsani aphunzi kuti apeleke maganizo ao kulingana ndi zomwe azamva.
II. Aphunzi:
● Amvetsele bwino ku nkhani zokambidwa kapena zowelengedwa.
● Acitate nchito ya kulingalila nkhani yakambidwa.
● Apeleke maganizo ao kulingana ndi zomwe azamva.
Muyeso Woyembekezeka: Ganizo leni-leni lazindikilidwa ndi kupelekedwa moyenela.
Nchito B: Kufupikitsa uthenga.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi yosavuta
● Yeselelani kufupikisa uthenga wa nkhani yawelengedwa pamozi ndi aphunzi.
● Uzani aphunzi kuti afotokoze nkhani zomwe amva mwakutengamo cabe mfundo zeni-
zeni.
II. Aphunzi:
29
● Amvetsele nkhani yapafupi
● Aye tselele kufupukitsa nkhani ya welengedwa.
● Afotokoze nkhani zomwe amva mwakutengamo cabe mfundo zeni-zeni.
Muyeso Woyembekezeleka: Nkhani yafupikitsidwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kufupikitsa maganizo kulingana ndi zomwe
aphunzi amva.
D. MVETSO
MUTU 1: Kumvetsela
Mutu Waung’ono 2: Zazoona ndi Malingalilo Cabe.
Ciyambi: Mutu uyu uzayangana pakuzindikila malingalilo cabe kucokela mnkhani
yazoona.
Luso Lapadela: Kusiyanitsa pakati pa zazoona ndi malingalilo cabe.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Makhadi a ziganizo, mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: Maganizo, malingalilo, kuzindikila, kusiyanitsa.
Mfundo zophunzitsa:
● Kuphunzitsa m’mene aphunzi angazindikilile maganizo cabe pa nkhani zazoona zomwe
amva.
● Kuwelenga nkhani kwa aphunzi ndi kuwafunsa mafunso mwakulankhula cabe.
● Kuuza aphunzi kuti apeleke maganizo ao kulingana ndi zomwe amva
Nchito A: Kuzindikila lingalilo mnkhani.
30
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi yapafupi
● Yeselelani ndi aphunzi kuzindikile lingalilo cabe.
● Uzani aphunzi kuti azindikila ligalilo/ganizo mnkhani yokambidwa kapena
yowelengedwa.
II. Aphunzi:
● Amvesele nkhani yawelengedwa ndi aphunzi
● Ayeselele kuzindikila lingalilo.
● Amvetsele bwino ku nkhani ndipo azindikilo lingalilo cabe ili mnkhaniyo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuzindikila lingalilo mnkhani kwacitidwa moyenela.
Nchito B: Kuzindikila zoona za nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi
● Yetsanni kuzindikila cazoona mnkhaniyi pamodzi ndi aphunzi
● Uzani aphunzi kuti azindikila cazoona mnkhani yokambidwa kapena yowelengedwa.
II. Aphunzi:
● Amvetsele nkhani kwa aphunzitsi
● Ayetselele kuzindikila cazoona mnkhaniyi pamodzi ndi aphunzi
● Azindikile cazoona mnkhani yokambidwa kapena yowelengedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Cazoona casiyanitsidwa ku ganizo cabe moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kusiyanitsa cazoona ku malingalilo cabe.
31
MUTU 2: MVETSO YA KUWELENGA
Mutu Waung’ono 2: Zoona za nkhani
Ciyambi: Mutu uyu udzayangana pa kupeleka uthenga kulingana ndi zomwe zamveka
mnkhani yawelengedwa.
Luso Zapadela: Kupeleka uthenga omveka bwino kucokela nkhani.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: makhadi a ziganizo, mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: uthenga, kupeleka, kufotokoza.
Mfundo zophunzitsa:
● Phunzitsani m’mene aphunzi angapelekele uthenga omvekka kucokela ku nkhani
yowelengedwa.
● Yetselelani ndi aphunzi kupeleka uthanga.
● Fotokozani kuti popeleka uthenga umatenga cabe mitu yeni-yeni a nkhaniyo.
Nchito A: Kufotokoza zomwe zawelengedwa.
I. Mphunzitsi :
● Welengani nkhani ndipo muwauze aphunzi kuti amvetsele modekha pamene
mukuwelenga nkhaniyo.
● Uzani aphunzi kuti naonso awelengeko nkhaniyo m’modzi-m’modzi, m’magulu ang’ono-
ang’ono ndiponso kalasi yonse.
● Uzeni aphunzi kuti afotokoze zomwe amva mnkhani.
II. Aphunzi :
32
● Amvetsele modekha pamene nkhani ikuwelengedwa.
● Awelenge nkhani mm'magulu ang'ono-ang'ono ndiponso kalasi yonse.
● Afotokoze zomwe amvamo mnkhani.
Nkhani
Gwendezani ndi Batizani anali kutsutsana kuti gwada sindiwo.
Amai ao atamva zakutsutsana, anaganiza zophika ndiwo za gwada kuti athese mkangano.
Tsikulo Gwendezani ndi Batizani onse anadya nsima ya gwada.
Muyeso Woyembekezeleka: Zomwe zawelengedwa zafotokozeddwa moyenela.
Nchito B: Kuyankha Mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa.
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti muzawawelengela nkhani ndipo azafunika kumvetsa cifukwa
muzawafunsa mafunso
● Uzani aphunzi kuti ayankhe mafunso kucokela ku zomwe zawelengdwa mnkhani.
II. Aphinzi:
● Amvetsele ku nkhani
● Ayankhe mafunso kulingana ndi zomwe awelenga.
Mafunso
1. Kodi Batizani anali kukangana ndiyani?
2. Anali kukangana cifukwa ca ciyani?
3. Amai ao anacita ciani kuti athese mkangano?
4. Kodi unakakhala iwe, unakacita ciyani kuti uthetse mkangano?
Muyeso Woyembekezeleka: Mafunso ayankhidwa moyenela.
33
Nchito C: Kufotokoza molondola momwe zinacitika mnkhani.
I. Mphunzitsi:
● Fotokozani cimodzi mwa zithu zomwe zinacitika mnkhani
● Uzani aphunzi kuti afotokoze zimene zawelengedwa mnkhani ili pa nchito A.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku zofotokozedwa
● Afotokoze molondola momwe zinthu zinacitikila mnkhani yomwe awelenga.
Muyeso Woyembekezeleka: Nkhani yafotokozedwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuyangana pakuwelenga nkhani, kuyankha mafunso ndi kufotokoza
zomwe zawelengedwa.
B. KULEMBA.
MUTU 1: MALEMBEDWE
Mutu Waung’ono 1: Malembedwe Okhazikika
Ciyambi: Mutu uyu uzayangana pa malembedwe okhazikika ndi kuzindikila pipata
m'mau.
Luso Lapadela: Kulemba mau m’malembedwe okhazikika.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Silabiki chati, mafulashi khadi, makhadi a
ziganizo, mabuku.
34
Mau Ofunikila Kudziwa: Kulemba, kukhazikika, lembo, malembedwe.
Mfundo Zophunzitsa:
● Uzani aphunzi kuti malembedwe ali ndi malamulo omwe afunika kulondoledwa
polemba.
● Fotokozani za lamulo lamicila yopita kumwamba komanso micila obwela pansi
mumalembedwe
Nchito A: Kujambula mau m’malembedwe okhazikika.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca malembedwe a mau polondola malembedwe okhazikika ndiponso
polemekeza micila opita kumwamba komanso pansi.
● Citani cimodzi-modzi ndi mvekelo zina.
II. Aphunzi:
● Aonelele ku citsanzo copelekedwa
● Alembe mau molondola bwino zomwe aphunzitsidwa pakalembedwe ka malembo.
Zocita:
1. Nkhono.
2. Nkhumba.
3. Nkhani
Muyeso Woyembekezeleka: Mau alembedwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuyangana pakalembedwe ka mau kokhazikika.
35
MUTU 1: Malembedwe
Mutu Waung’ono 2: Mipata a mau.
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa malembedwe okhazikika.
Luso lapadela: Kusiya mipata m’mau.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Fulashi khadi, makhadi a ziganizo, mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: Kulemba, kukhazikika, lembo, mipata.
Mfundo zophunzitsila:
● Uzani aphunzi kuti malembedwe abwino aziganizo ayenela kukhala ndi mipata pakati
opa mau.
● Fotokozaninso za lamulo lamicila yopita kumwamba komanso micila obwela pansi
mumalembedwe.
Nchito A: Kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca malembedwe a ziganizo pozindikila ndi kusiya mipata pakati pa
mau.
● Citani cimodzi-modzi ndi mvekelo zina.
II. Aphunzi :
● Alembe ziganizo ndi kulemekeza kusiya mipata pakati pa mau.
Zocita:
1. Nkhono ipezeka kumtunda ndi m’madzi.
2. Nkhumba ndi nyama yoweta.
36
Muyeso Woyembekezeleka: malembedwe okhazikika alembedwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa malembedwe okhazikika ndi kuzindikila mipata
ya mau m'ziganizo.
Mutu 2: Cimangilizo
Mutu Waung’ono 1: Zopumila
Lambulo: Mutu uyu uzaona pa kuzindikila zomupila, kulemba ziganizo zathunthu ndi
kupanga nkhani yapafupi.
Luso lapadela: Kugwilitsa nchito zopumila zeni-zeni. (Malemba akulu-akulu, copumila kothela
kwa liu)
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Chati ya ziganizo, buku la nkhani.
Mau Ofunikila Kudziwa: Zopumula, cimangilizo. Nkhani,
Mfundo zophunzitsa:
● Kuphunzitsa zopumila.
● Kuphunzitsa ziganizo.
● Kuphunzitsa nkhani yapafupi.
Nchito A: Kuzindikila lembo lalikulu ndi copumila cacikulu
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti ciganizo cimayamba ndi lembo lalikulu ndipo cimatha ndi copumila.
● Patsani citsanzo caciganizo comwe cili ndi lemba lalikulu ndi copumila.
37
● Patsani aphunzi ziganizo zolembedwa moyenela ndipo muwauze kuti azindikile lemba
laikulu ndi copumila polemba kamzele munsi mwake.
●
II. Aphunzi:
● Avetsetse pomwe aphunzitsi akufotokoza za lemba loyamba ndi copumula.
● Aone citsanzo ca ciganizo ca lembo lalikulu ndi copumula.
● Azindikile lembo lalikulu ndi copumila polemba kamzele munsi mwake.
Citsanzo
1. Atate atyola msale.
2. Mfumu yagwidwa ndi cisoni.
Muyeso Woyembekezeleka: Lembo lalikulu ndi copumila cazindikilidwa moyenela.
Nchito B: Kuika lembo lalikulu ndi zopumila m’ziganizo.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi kaikidwe ka lembo lalikulu ndi zopumila m'ziganizo.
● Patsani aphunzi ziganizo zomwe zilibe malembo aakulu ndi zopumila ndipo
muwauze kuti aikemo.
II. Aphunzi:
● Aonetsetse kaikidwa ka lembo lalikulu ndi copumila.
● Aike malembo aakulu ndi zopumila mziganizo.
Citsanzo
1. atate agwila mfuko
2. ana akudya magwawa
Muyeso Woyembekezeleka: Ziganizo zaikidwa zopumila moyenela.
Mutu Waung’ono 2: Ziganizo
38
Lambulo: Mutu waung'ono uyu uzaona pakulemba ziganizo zathunthu.
Luso Lapadela: Kulemba ziganizo zathunthu.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Chati ya ziganizo, mafulashi khadi aziganizo
Mau Ofunikila Kudziwa: ziganizo, zathunthu
Mfundo zophunzitsa:
● Kuphunzitsa kulemba ziganizo zathunthu.
Nchito: Kulemba ziganizo zathunthu
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi malembedwe aziganizo zathunrhu.
● Funsani aphunzi kuti alembe ziganizo zathunthu m'magulu ao.
II. Aphunzi:
● Aone malembedwe aziganizo zathunthu.
● M'magulu ao, alembe ziganizo zathunthu.
Muyeso Woyembekezeleka: Ziganizo zathunthu zalembedwa moyenela.
Mutu Waung’ono 3: Nkhani yosavuta
Ciyambi: Mutu waung'ono uyu uzaona pakutsilizitsa ziganizo za nkhani ndi kupanga
nkhani yasabvuta.
Luso Lapadela: Kulemba nkhani yosabvuta
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Chati ya nkhani, buku la nkhani.
39
Mau Ofunikila Kudziwa: yosabvuta, kupanga,,
Mfundo zophunzitsa:
● Kuphunzitsa kasilizidwe ka ziganizo za nkhani.
● Kuphunzitsa kapangidwe ka nkhani yosabvuta.
Nchito A: Kusilizitsa ziganizo za nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Aonetse katsilizidwe ka ziganizo za nkhani.
Citsanzo:
Dzulo amai anapita kumunda.
Popita ananyamula…………………
Atafika kumunda……………………
● Aonetsenso kapangidwe ka nkhani yosabvuta.
● Auze aphunzi kuti apange nkhani yosabvuta m'magulu ao.
II. Aphunzi:
● Aone katsilizidwe ka ziganizo za nkhani
● Aonenso kapangidwe ka nkhani yosabvuta
● Apange nkhani yosabvuta m'magulu ao.
Muyeso Woyembekezeleka: Nkhani yapafupi yapangidwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kuzindikila zomupila, kulemba ziganizo zathunthu
ndi kupanga nkhani yapafupi.
40
CAPAMUTU 2: KUFOTOKOZA MAONEKEDWE A
ZINTHU
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa kufotokoza za maonekedwe a zinthu, mau ogwilitsa
nchito pakufotokoza za zinthu zochulidwa, kuzindikila mvekelo, ubale wa lembo ndi mvekelo,
masilabe, mau, kuwelenga mofulumila, matanthauzo a mau, mvetso, malembedwe ndi
cimangilizo.
CIGAWO: KUMVETSELA NDI KULANKHULA
MUTU: Kufotokoza Za Maonekedwe
Mutu Waung’ono: Zinthu
Luso Lapadela: Fotokozani maonekedwe a zinthu.
Mau Ofunika Kudziwa: Maonekedwe, kufotokoza, zinthu.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Chati yoonetsa zinthu zosiyana-siyana, zinthu zooneka
komanso zogwilika ndi manja.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuphunzitsa kulemba mau omwe agwilitsidwa nchito pofotokoza za zinthu.
● Kuphunzitsa kugwilitsa nchito mau ozindikilidwa kuti afotokoze za zinthu.
Nchito A: Kulemba mau omwe agwilitsidwa nchito pofotokoza za zinthu.
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti alembe mau omwe amagwilitsidwa nchito pofotokoza za
maonekedwe a zinthu (cacikulu, cacifupi, cacing’ono, cacitali).
41
● Afunse aphunzi kuti achulenso utoto wa zinthuzo (fiira, dwambe, yela, cikasu, mtambo).
Citsanzo:
Mnyamata wa mtali.
Nyumba yofiila.
II. Aphunzi:
● Alembe mau omwe amagwilitsidwa nchito pofotokoza za maonekedwe a zinthu.
● Achulenso utoto wa zinthu zomwe zilikufotokozedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Mau ogwilitsidwa nchito pofotokoza maonekedwe a zinthu achulidwa
moyenela.
Nchito B: Kugwilitsa nchito mau azindikilidwa kufotokoza za maonekedwe a
zinthu.
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti azindikile mau ogwilitsa nchito pofotokoza za maonekedwe a zinthu
mu sukulu lao komanso kunyumba.
● Auze aphunzi kuti afotokoze maonekedwe a zinthu za mu sukulu monga;
Kalasi, bolodi, desiki, buku
● Uzani aphunzi kuti afotokozenso maonekedwe a zinthu za ku nyumba monga;
Nyumba yao, ziweto, mipando ndi zina zotele.
II. Aphunzi:
● Azindikile mau ogwilitsa nchito pofotokoza za maonekedwe a zinthu.
● Afotokoze maonekedwe a zinthu za mu sukulu lao .
● Afotokozenso maonekedwe a zinthu za kunyumba kwao.
Muyeso Woyembekezeleka: Mau ozindikilidwa adwilitsidwa nchito moyenela pofotokoza za
zinthu.
42
Nchito C: Kusewela masewela ofotokoza zinthu.
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti asewele masewela ofotokoza za maonekedwe a zinthu zosiyana-
siyana.
II. Aphunzi:
● Asewele masewela ofotokoza za maonekedwe a zinthu zosiyana-siyana ( masewela
monga; I spy, who am I? ).
Muyeso Woyembekezeleka: Masewela ofotokoza maonekedwe a zinthu aseweledwa
moyenela.
Mwacidule: Aphunzi aphunzila kufotokoza maonekedwe a zinthu zosiyana-siyana.
CIGAWO: KUWELENGA
MUTU: KUZINDIKILA MASILABE
Mutu Waung’ono 1: Kuzindikila masilabe opangidwa ndi; ii-, uu-, ng- , bv-
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse masilabe amvekelo imodzi mpaka onse owonetsedwa pa
mwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila masilabe bva, bve, bvi, bvo, bvu.
Ciyambi: Cigawoci cizaona pa kuzindikila masilabe mu mau okambidwa. Mau awa
azathandiza aphunzi kuzindikila kuti mau ali ndi masilabe, ndipo azazindikila mvekelo pa silabe
lililonse.
Luso lapadela: Kuzindikila ndi kusintha masilabe.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Fulashi khadi, silabiki chati.
43
Mau Ofunika Kudziwa: Masilabe, mvekelo, vawelo.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuzindikila masilabe mu mau okambidwa.
● Kusewela masewela owelenga masilabe.
● Kusewela masewela opanga mau.
Nchito A: Kuzindikila masilabe m’mau olankhulidwa.
I. Mphunzitsi:
● Alankhule mau ndi kuuza aphunzi masilabe omwe alimo.
● Anene mau ndi kufunsa aphunzi kuzindikila masilabe alimo.
Citsanzo:
1. Ng'o/mbe ng'o/mbe
2. Bvuula bvu/u/la
II. Aphunzi:
● Amvetsele mau olankhulidwa.
● Azindikile masilabe m’mau olankhulidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe m’mau olankhulidwa azindikilidwa moyenela.
Nchito B: Kusewela masewela akuwelenga masilabe poomba m'manja.
I. Mphunzitsi:
● Aonetse aphunzi kacitidwe ka masewela akuwelenga masilabe poomba m’manja.
Auze aphunzi kuti acite masewela akuwelenga masilabe poomba m’manja.
II Aphunzi:
44
● Aonelele kacitidwe ka masewela akuwelenga masilabe poomba m’manja.
● Asewele masewela akuwelenga masilabe poomba m’manja.
Muyeso Woyembekezeleka: Masewela owelenga masilabe aseweledwa moyenela.
Nchito C: Kupanga mau olankhulidwa pogwilitsa nchito masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Phunzitsani kapangidwe ka mau pogwilitsa nchito masilabe.
● Uzaze aphunzi kuti apanga mau olankhulidwa pogwilitsa nchito masilabe m’magulu
ao.
II. Aphunzi:
● Aone kapangidwe ka mau olankhulidwa pogwilitsa nchito masilabe.
● Apange mau olankhulidwa m’magulu ao pogwilitsa nchito masilabe.
Muyeso Woyembekezeleka: Mau olankhulidwa apangidwa moyenela pogwilitsa nchito
masilabe.
Nchito D: Kusewela masewela opanga mau (Kusinthanitsa ndi kucotsa masilabe)
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi masewela akupanga mau pa kusinthanitsa ndi kucotsa masilabe.
● Ikani aphunzi m’magulu kuti acite masewela akupanga mau pa kusinthanitsa ndi
kucotsa masilabe kupanga mau atsopano.
II. Aphunzi:
● Aone masewela a kapangidwe ka mau pa kusinthanitsa ndi kucotsa masilabe.
● Acite masewela a kupanga mau pa kusinthanitsa ndi kucotsa masilabe kupanga mau
atsopano.
45
Zitsanzo:
Kusinthanitsa
i. Ng'ona bvina.
ii. Ng’ambe ng’ombe.
Kucotsa
i. Ng’ambako mbako
ii. Mabvuto bvuto
Muyeso Woyembekezeleka: Masewela opanga mau aseweledwa moyenela.
Mwacidule: Aphunzi a zindikila masilabe ndi kucita masewela akuomba m’manja.
Acitanso masewela opanga mau kugwilitsa nchito masilabe kucokela ku mau okambidwa.
MUTU 2: Kulumikiza Makonsonanti ndi Mavawelo
Mutu waung’ono 1: Masilabe
Lambulo: Mutu waung’ono uyu uzaona pa kupanga masilabe kucokela ku makonsonanti
ndi mavawelo.
Luso Lapadela: Kulumikiza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
Mau Ofunikila Kudziwa:
● Makonsonanti, mavawelo, masilabe, kulumikiza.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuphunzitsa kulumiza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
46
● Kuwelenga silabiki chati .
● Kusankha masilabe mu mau.
● Kucotsa malembo mu mau ndi kupanga mau atsopano.
Nchito A: Kulumikiza makonsonant ndi avawelo kupanga masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Sonyezani molumikizila makonsonanti ndi mavawelo popanga masilabe.
Citsanzo: b/ii bii, ph/ ii phii, f /ii fii.
● Ikani aphunzi m’magulu apange masilabe pogwilitsa nchito vawelo ‘ii’ ndi mvekelo /s/,
/b/, /bv/, /f/.
● Uzani aphunzi kuti awelenge masilabe yomwe apanga monga awa; sii, bii, bvii,fii.
II. Aphunzi:
● Alumikize makosonanti ndi mavawelo
● M’magulu apange masilabe pogwilitsa nchito mvekelo /bv/ ndi mavawelo.
● Awelenge masilabe omwe apangidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe apangidwa moyenela kucokela ku makonsonanti ndi
mavawelo
Nchito B: Kuwelenga chati ya masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Asonyeze aphunzi kawelengedwe ka chati ya masilabe.
● Akumbutse aphunzi njila zosiyana-siyana zowelengelamo chati ya masilabe
monga; kucokela kudzanja la manzele kupita ku dzanja la manja ndi kucokela
kumwamba kutsikila pansi.
47
● Awelenge chati ya masilabe m'magulu ao.
II. Aphunzi:
● Aonelele kawelengedwe ka chati ya masilabe.
● Akumbukile mawelengedwe ocokela kudzanja la manzele kupita ku dzanja la
manja ndi kucokela kumwamba kutsikila pansi.
● M’magulu ao awelenge silabiki chati m’njila zosiyana-siyana monga;
1. Kucokela kudzanja la manzele kupita kudzanja la manja.
2. Kucokela kumwamba kutsikila pansi.
3. Kuwelenga mwa zigi-zagi komanso mosakaniza.
Muyeso Woyembekezeleka: Silabiki chati yawelengedwa moyenela.
Nchito C: Kusankha masilabe
I. Mphunzitsi:
● Asonyeze mosankhila masilabe kucokela m'mau.
● Afunse aphunzi kuti akhale awili-awili ndipo asankhe masilabe kucokela
m'mau opelekedwa.
Citsanzo: bvuula, bviika
II. Aphunzi:
● Aphunzile mosankhila masilabe kucokela ku mau.
● Akhale awili-awili ndipo asankhe masilabe kucokela ku mau opatsidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe asankhidwa moyenela.
Nchito D: Kusintha masilabe
I. Mphunzitsi:
48
● Auze aphunzi kuti awelenge mau opelekedwa.
● Aonetse mosinthanitsila malembo.
Citsanzo: Bvina bvika ‘
● Auze aphunzi kuti asinthanitse lembe zocita posinthanitsa malembo.
II. Aphunzi:
● Awelenge mau opelekedwa.
● Aphunzile mosinthanitsila malembo kupanga mau atsopano.
● Alembe zocita posinthanitsa malembo.
Muyeso Woyembekezeleka: Malembo asinthanitsidwa moyenela.
Nchito E: Kulumikiza makonsonanti a mvekelo zosiyana ndi mavawelo popanga masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Aonetse aphunzi molumikizila makonsonanti a mvekelo zosiyana ndi
mavawelo kupanga masilabe.
Citsanzo:
-bv/a bva
-bv/i bvi.
● Afunse aphunzi kukhala awili-awili kuti ayeselele kulumikiza
makonsonanti a mvekelo zosiyana ndi mavawelo kupanga masilabe.
II. Aphunzi:
● Aone molumikizila makonsonanti a mvekelo zosiyana popanga masilabe.
● Akhale awili-awili kuti ayeselele kulumikiza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
Muyeso Woyembekezeleka: Makonsonanti a mvekelo zosiyana-siyana ndi mavawelo
alumikizidwa moyenela.
Mutu waung’ono 2: Mau
49
Lambulo: Mutu uyu uzaona pakulumikiza masilabi kupanga mau, kusintha ndi kucotsa
masilabe kupanga mau atsopano, kuzindikila masilabe mu mau ndi kuwelenga masilabe.
Luso lapadela: Kulumikiza masilabe popange mau.
Zipangizo zophunzila ndi zophunzilila: Silabiki chati, mafulashikhadi.
Mau ofunika kudziwa: Makonsonanti, mavawelo, masilabe, kulumikiza.
Mfundo zophunzitsa:
● Kulumikiza masilabe kupanga mau
● Kusinthanitsa ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano
● Kudzindikila masibe mu mau
● Kupenda silabe mu mau
Nchito A: Kulumikiza masilabe kupanga mau
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi mapangidwe a mau kugwilitsa nchito masilabe.
Zitsanzo: Bi/i bii
Bvi/ni/ki/la bvinikila
● Funsani aphunzi kuti apange mau kugwilitsa nchito masilabe opatsidwa m'magulu ao.
● Uzani aphunzi kuti azindikile nambala ya masilabe m’mau opatsidwa.
Zitsanzo:
1. Bii 2
2. Bviika 3
3. Bvindikila 4
50
II. Aphunzi:
● Aphunzi aone kapangidwe ka mau pogwilitsa nchito masilabe.
● Apanga mau kugwilitsa nchito masilabe.
● Azindikile nambala ya masilabe m'mau.
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe alumikizidwa moyenela kupanga mau.
Nchito B: Kusintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau atsopano.
I. Mphunzitsi:
● Aphunzitse kasinthidwe ka masilabe kupanga mau.
Kusintha masilabe kupanga mau
● Bvika bvina (cotsani /bvi/ ikani /bvu/)
● Aonetsa aphunzi kapangidwe ka mau pocotsela masilabe.
Kucotsa masilabe kupanga mau.
ii. Kubviika bviika (cotsani silabe / ku/)
● Ikani aphunzi m’magulu kuti apanga mau pa kusintha ndi kucotsa masilabe.
II. Aphunzi:
● Aphunzile kasinthidwe ka masilabe kupanga mau.
● Aonelele kapangidwe ka mau pa kusintha masilabe.
● M’magulu ao apanga mau atsopano pa kusintha ndi kucotsa masilabe.
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe asinthanitsidwa moyela.
Nchito C: Kuzindikila masilabe m'mau.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani zithunzi kwa aphunzi.
● Funsani aphunzi kuti afotokoze zomwe aona pa zithunzi monga;
51
- mnyamata a kubvika nyumba,
- mai aku bviika zobvala.
● Uzani aphunzi kuti azindikile masilabe m'mau omwe apelekedwa.
- kubvika
- bviika
II. Aphunzi:
● Aone zithunzi zomwe zapelekedwa.
● Afotokoze zomwe aona pa zithunzi.
● Azindikile masilabe mu mau omwe apelekedwa.
-kubvika ku/bvi/ka
-bviika bvi/i/ka
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe mu mau azindikilidwa moyenela.
Nchito D: kuwelenga masilabe
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi momwe angawelengele masilabe m'mau.
● Uzani aphunzi kuti awelenge nambala ya masilabe mu mau awa:
II. Aphunzi:
● Aphunzile momwe angawelengele masilabe m'mau.
● Awelenge nambala ya masilabe mu mau opelekedwa.
Zitsanzo:
1. Bvala 2
2. Wa/bva/la 3
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga masilabe kwacitidwa moyenela.
52
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kulumikiza masilabe kupanga mau, kusintha ndi
kucotsa masilabe kupanga mau atsopano, kuzindikila masilabe mu mau ndi kuwelenga masilabe.
MUTU 3: KUWELENGA MOFULUMILA
Luso Lapadela 1: Kuwelenga mau mokuwa ndiponso molungama
Nchito : Kuwelenga mau
I. Mphunzitsi:
● Akambe mau.
● Alembe mau pa bolodi.
● Auze aphunzi kuti awelenge mau awa;
-siila, cofiila, ng’ombe, kuula, bvuta.
II. Aphunzi:
● Amvetsele mau okambidwa
● Awelenge mau mokuwa m’magulu ao.
● Awelenge mau opatsidwawo ndi machulidwe oyenela.
Zocita:
Welengani mau awa mokuwa komanso mofulumila awili-awili;
1. Bvundula
2. Bviika
Muyeso woyembekezeleka: Mau awelengedwa moyenela
Luso Lapadela: Kuwelenga nkhani mokuwa pozindikila kachulidwe ka mau
Nchito A: Kuwelenga ndi kumvetsetsa ziganizo.
53
I. Mphunzitsi:
● Onetsani chati ya ziganizo kwa aphunzi.
● Funsani aphunzi kuti awelenge ziganizo momvetsetsa m’modzi-m’modzi pa nthawi .
● Uzani aphunzi kuti alembe m’mabuku ao.
Zitsanzo:
-Malita wabvala delesi lofiila.
II. Aphunzi:
● Aone chati ya ziganizo yoonetsedwa ndi mphunzitsi.
● Awelenge ziganizo m’modzi-m’modzi pa nthawi momvetsetsa ndipo ayankhe mafunso.
● Alembe ziganizo m’mabuku ao.
Muyeso Woyembekezeleka: Ziganizo zawelengedwa ndiponso zayankhidwa moyenela.
Nchito B: Kuwelenga nkhani ya ziganizo za pakati pa ziwili ndi zisanu. (Kuwelenga kwa
gulu, kolondola mphunzitsi komanso kwa awili-awili).
I. Mphunzitsi:
● Awelenge nkhani yaifupi ili pa chati kuti aphunzi amvetsele.
● Auze aphunzi kuti ayeselele kuwelenga nkani yomwe yawelengedwa ndi mphunzitsi.
Nkhani:
Fumbani anafuna kupita ku msika. Asanapite anaganizila zotenga ng’ombe zake
ndi ngolo. Fumbani anagula ufa, malaya ofiila ndi bulangeti.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku nkhani.
54
● Ayeselele kuwelenga nkhani.
Muyeso Woyembekezeleka: Nkhani ya ziganizo zifupi-zifupi za pakati pa ziwili ndi zisanu
zawelengedwa moyenela.
Nchito C: Kuwelenga nkhani zili ndi mvekelo zosiyana-siyana komanso
zolumikizidwa.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani mabuku omwe ali ndi nkhani zosiyana-siyana.
● Uzani aphunzi kuti awelenge nkhani.
II. Aphunzi:
● Alandile mabuku ali ndi nkhani zowelenga.
● Awelenge nkhani payekha-payekha.
Muyeso Woyembekezeleka: Nkhani za mvekelo zosiyana-siyana komanso
zolumikizidwa zamvetsedwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kuwelenga masilabe ndi mau mokuwa ndiponso
mofulumila. Wayangananso pakuwelenga nkhani ya ziganizo zifupi-zifupi za pakati pa ziwili ndi
zisanu.
MATANTHAUZO A MAU
MUTU: MAINA
Mutu waung’ono: Maina Osaculukitsidwa ndi Oculukitsidwa.
55
Lambulo: Mutuyu uzaona pa kupanga maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
Kulinganiza komanso kusewela masewela a maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa.
Luso Lapadela: Kupanga maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
Mau Ofunika Kudziwa: Maina, maina oculukitsidwa, maina osaculukitsidwa.
Mfundo Zophunzitsa:
Kuphunzitsa kupanga maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
Zida Zophunzitsila Ndi Zophunzilila:
Mafulashi khadi, machati ndi zipangizo zogwilika.
Nchito A: Kupanga maina oculukitsidwa kucoka ku osaculukitsidwa
I. Mphunzitsi:
● Funsani aphunzi kuti apeleke zitsanzo za maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
● Uzani aphunzi kuti apange maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
● Auze aphunzi kuti apangenso maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
Zitsanzo:
MAINA OSACULUKITSIDWA MAINA OCULUKITSIDWA
Bvuto Mabvuto
II. Aphunzi:
● Apeleke zitsanzo za maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
● Apange maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
● Apangenso maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Maina oculukitsidwa apangidwa moyenela kucokela ku maina
osaculukitsidwa.
56
Nchito B:
Kupanga maina osaculukitsidwa kucoka ku maina oculukitsidwa.
I. Mphunzitsi:
● Afunse aphunzi kuti achule maina osaculukitsidwa.
● Auze aphunzi kuti apeleke zitsanzo za maina osaculukitsidwa kucokela kuli
oculukitsidwa.
MAINA OCULUKITSIDWA MAINA OSACULUKITSIDWA
Cobvala Zobvala
● Auze aphunzi kuti apange maina osaculukitsidwa kucokele ku maina oculukitsidwa.
II. Aphunzi:
● Achule maina osaculukitsidwa.
● Apeleke maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
● Apange maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Maina osaculukitsidwa apangidwa moyenela.
Nchito C: Kulinganiza maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa pa chati.
● Uzani aphunzi kuti aculukitse maina osaculukitsidwa.
● Funsani aphunzi kuti alinganize maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
Zitsanzo:
1. Bvuto mabvuto
57
2. Cobvala zobvala
II. Aphunzi:
● Aone maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa pa chati.
● Aculukitse maina osaculukitsidwa.
● Alinganize maina oculukitsidwa nd osaculukitsidwa.
Zocita:
Linganizani maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa
1. Bvumbwe asing’ang
2. Bvuto abvumbwe
3. Sing’anga mabvuto
Muyeso Woyembekezeleka: Maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa
alinganizidwa moyenela.
Nchito D: Kusewela masewela a maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi kaseweledwe ka masewela a maina oculukitsidwa ndi
osaculukitsidwa.
● Sewelani pamodzi ndi aphunzi masewela a maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
● Uzani aphunzi kuti asewele masewela a maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa
pogwilitsa nchito ma fulashi khadi m'magulu ao. (Plural bingo ndi plural scavenger).
II. Aphunzi:
● Aonelele kaseweledwe ka masewela a maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
● Asewele pamodzi ndi aphunzitsi masewela a maina oculukitsidwa ndi
osaculukitsidwa.
● Asewele masewela a maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa m'magulu ao.
58
Muyeso Woyembekezeleka: Masewela a maina oculukitsidwa ndi
osaculukitsidwa aseweledwa moyenela.
Mwacidule: Phunziloli laphunzitsa aphunzi kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku
maina osaculukitsidwa komanso maina oculukitsidwa kucokela ku osaculukitsidwa.
MVETSO
MUTU 1: KUMVETSELA NKHANI.
Mutu Waung’ono 1: Ganizo Leni-Leni.
Lambulo: Mutu uyu uzaona pa kumvetsela nkhani ndi kupeleka maganizo pa zomwe
zamveka pa nkhaniyo.
Luso Lapadela: Kuzindikila ndi kupeleka ganizo leni-leni la uthenga womwe iwo amva.
Mau Ofunika Kudziwa: Mvetselo, nkhani, mvetso, maganizo.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuphunzitsa m’mene aphunzi angapelekele maganizo pa nkhani yomwe amva.
● Kuwelenga nkhani kwa aphunzi ndi kuwafunsa mafunso mwakulakhula cabe.
● Kuuza aphunzi kuti apeleke maganizo kulingana ndi zomwe amva.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Makhadi a ziganizo, mabuku, mafulashi khadi.
Nchito A: Kuzindikila ndi kupeleka ganizo leni-leni la uthenga womwe amva.
I. Mphunzitsi:
● Awelenge nkhani kwa aphunzi ndi kuwafunsa mafunso mwakulakhula cabe.
● Auze aphunzi kuti apeleke maganizo ao kulingana ndi zomwe amva.
59
II. Aphunzi:
● Amvetsele khani yowelengedwa ndi aphunzitsi ndipo ayankhe mafunso.
● Apeleke maganizo ao kulinga ndi zomwe amva.
Muyeso Woyembekezeleka: Ganizo leni-leni lazindikilidwa ndipo la nenedwa moyenela.
Nchito B: Kufupikitsa Uthenga.
I. Mphunzitsi:
● Awelenge kapena afotokoze nkhani kwa aphunzi.
● Afunse aphunzi kuti anene uthenga omwe amva mnkhani.
● Auze aphunzi kuti afupikitse uthenga mwakujambula zithunzi zofotokoza uthenga omwe
amva.
II. Aphunzi:
● Aone zili pa cithunzi.
● Anene zomwe aona pa cithunzi.
● Alembe uthenga wopatsidwa mwakufupikitsa.
Muyeso Woyembekezeleka: Uthenga wafupikitsidwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kumvetsela nkhani ndi kupeleka maganizo pa
nkhani yomwe yawelengedwa komanso kufupikitsa uthenga.
Mutu waung’ono 2: Coona ndi Lingalilo.
Lambulo: Mutu uyu uzaona pa kuzindikila lingalilo ndi coonadi mnkhani.
60
Luso Lapadela: Kusiyanitsa pakati pa coona ndi lingalilo.
Mau Ofunika Kudziwa: Coona, lingalilo, kusiyanitsa.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Mabuku, makhadi.
Nchito A: Kuzindikila Lingalilo Mu Nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti mudzawawelengela nkhani ndipo ayenela kumvetsetsa
● Kambani kapena welengani nkhani kwa aphunzi ndipo muonetse mozindikilila lingalilo
cabe mnkhaniyo.
● Kambani kapena welengani nkhani zina ndipo muwauze aphunzi kuti azindikile lingalilo
cabe mnkhaniyo.
II. Aphunzi:
● Amvetsele nkhani ndipo aonelele mozindikilila lingalilo cabe m'nkhani.
● Awelenge ndi kumvetsele ku nkhani
● Azindikile lingalilo pokambilana m'magulu.
Muyeso Woyembekezeleka: Malingalilo m’nkhani yazindikilidwa moyenela.
Nchito B: Kuzindikila Coona M’nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi ndipo muonete mozindikilila zoona za nkhani.
● Pelekani mabuku a nkhani kwa aphunzi kuti awelenge m'magulu ao ndipo azindikile
coona mnkhaniyo.
II. Aphunzi:
61
● Alandile mabuku ali ndi nkhani zowelenga.
● Awelenge nkhani m'magulu ndipo azindikile coona mnkhaniyo.
Muyeso Woyembekezeleka: Coona casiyanitsidwa kulingalilo moyenela.
Mwacidule: Phunziloli linali kuona pa kuzindikila lingalilo ndi coonadi mnkhani.
MUTU 2: MVETSO YA KUWELENGA
Mutu Waung’ono: Zoona Za Nkhani
Lambulo: Mutu uyu uzana pa kupeleka uthenga wonenedwa m’nkhani yaifupi
yopatsidwa.
Luso Lapadela: Kupeleka uthenga wonenedwa m’nkhani yaifupi yopatsidwa.
Mau Ofunika Kudziwa: Uthenga, nkhani, ifupi.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuphunzitsa momwe aphunzi angapelekele uthenga wonenedwa m’nkhani.
● Momwe angafotokozele zomwe zawelengedwa.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Mabuku, makhadi aziganizo.
Nchito A: Kufotokoza Zomwe Zawelengedwa M’nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi.
● Phunzitsani aphunzi momwe angafotokozele zomwe zawelengedwa mnkhani.
● Patsani aphunzi nkhani kuti awelenge ndipo afotokoze zomwe zawelengedwa.
62
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku nkhani yowelengedwa.
● Aphunzile momwe angafotokozele zomwe zawelengedwa mnkhani.
● Awelenge ndipo afotokoze zomwe zawelengedwa mnkhani.
Muyeso Woyembekezeleka: Uthenga wawelengedwa ndipo wafotokozedwa moyenela.
Nchito B: Kuyankha Mafunso Kucokela Ku Zomwe Zawelengedwa.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi.
● Auze aphunzi kuti awelenge nkhaniyo m'magulu ao.
● Funsani aphunzi kuti ayankhe mafunso kucokela ku zomwe awelenga paokha ( Nciani?
Ndani? N’kuti? Liti? Zinacitika bwanji?).
II. Aphunzi:
● Amvetsele poimwe aphunzitsi akuwelenga.
● Awelenge nkhani m'magulu ao.
● Ayankhe mafunso kucokela ku zomwe awelenga.
Muyeso Woyembekezeleka: Mafunso ayankhidwa moyenela.
Nchito C: Kufotokoza Molunjika Momwe Zinthu Zinacitikila Mu Nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi ndipo mufotokoze molunjika momwe zinthu zinacitikila
mnkhani.
● Patsani aphunzi nkhani yina kuti awelenge m'magulu ao
● Funsani aphunzi kuti afotokoze molunjika momwe zinthu zinali kucitikila mu nkhani.
63
II. Aphunzi:
● Amvetsela pomwe aphunzitsi akuphunzitsa mawelengedwe ndi mafotokozedwe azocitika
mnkhani.
● Awelenge nkhani yopatsidwa m'magulu ao.
● Afotokoze molunjika momwe zinthu zinacitikila mnkhani.
Muyeso Woyembekezeleka: Zocitika mu nkhani zafotokozedwa molunkika bwino.
Mwacidule: Aphunzi aphunzila kuwelenga ndi kufotokoza uthenga wowelengedwa
kapena wokambidwa mnkhani.
B. KULEMBA.
MUTU: MALEMBEDWE
Mutu Waung’ono 1: Kupanga Lembo
Lambulo: Mutuyu uzaona pa kapangidwe ka lembo.
Luso Lapadula: Kulemba lembo.
Mau Ofunika Kuziwa: Malembedwa, lembo, kujambula.
Mfundo Zophunzitsa: Kuphunzitsa kapangidwe ka malembo osiyana-siyana.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Mafulashi khadi, mabuku, silabiki chati.
Nchito A: Kujambula Malembo
64
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi kalembedwa ka lembo koyenela.
● Funsani aphunzi m'modzi-m'modzi kuti ayeselele kulemba malembo opatsidwa pa bolodi
kapena padothi.
● Patsani aphinzi malembo ndipo muwauzse kuti ajambule m'mabuku ao.
II. Aphunzi:
● Aonelele kalembedwe ka lembo koyenela.
● Ayeselele kulemba malembo opatsidwa pa bolodi ndi padothi.
● Ajambule nchito malembo apatsidwa m'mabuku ao.
Muyeso Woyembekezeleka: Malembo alembedwa moyenela.
Nchito B: Kulemba Malembo
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi m’mene malembo alembedwela m’mizele.
● Funsani aphunzi kuti ayeselele kulemba malembo yalembedwa pa bolodi.
● Uzani aphunzi kuti alembe malembo paokha m’mabuku ao.
Zitsanzo:
Malembo a micila itali-itali yokwezeka…….d, b ,k ,h.
Malembo a micila yotsikila pansi………f, g, h, j
II. Aphunzi:
● Aonelele m’mene malembo alembedwela m’mizele.
● Ayeselele kulemba malembo yolembedwa pa bolodi.
● Alembe malembo paokha m’mabuku ao.
Muyeso Woyembekezeleka: Malembo alembedwa moyenela.
65
Mutu Waung’ono 2: Malembedwe okhazikika
Lambulo: mutu uyu uzayangana pa malembedwe okhazikika ndi kuzindikila pipata
m'mau.
Luso lapadela: Kulemba mau m’malembedwe okhazikika.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Silabiki chati, mafulashi khadi, makhadi a
ziganizo, mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: kulemba, kukhazikika, lembo, malembedwe.
Mfundo zophunzitsa:
● Uzani aphunzi kuti malembedwe ali ndi malamulo omwe afunika kulondoledwa
polemba.
Fotokozani za lamulo lamicila yopita kumwamba komanso micila obwela pansi mumalembedwe
Nchito: Kujambula mau m’malembedwe okhazikika.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca malembedwe a mau polondola malembedwe okhazikika ndiponso
polemekeza micila opita kumwamba komanso pansi.
● Citani cimodzi-modzi ndi mvekelo zina.
II. Aphunzi:
Alembe mau molondola bwino zomwe aphunzitsidwa pakalembedwe ka malembo.
Zocita:
1. Nkhono.
66
2. Nkhumba.
3. Nkhani
Muyeso Woyembekezeleka: Mau alembedwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pakalembedwe ka mau kokhazikika.
MUTU 1: Malembedwe
Mutu Waung’ono 3: Mipata a mau.
Lambulo: Mutu uyu uzaona pakusiya mipata m'mau.
Luso lapadela: kusiya mipata m’mau.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Fulashi khadi, makhadi a ziganizo, mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: kulemba, kukhazikika, lembo, mipata.
Mfundo zophunzitsila:
● Uzani aphunzi kuti malembedwe abwino aziganizo ayenela kukhala ndi mipata pakati
opa mau.
● Fotokozaninso za lamulo lamicila yopita kumwamba komanso micila obwela pansi
mumalembedwe.
Nchito: Kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo cakuzindikila mipata m'ziganizo zomwe zilibe mipata m'malembedwe
okhazikika.
67
● Funsani aphunzi kuti ayeselele kulemba ziganizo zopatsidwa zomwe zilibe mipata
m'magulu ao.
● Patsani aphunzi ziganizo zomwe zilibe mipata ndipo muwauza kuti azindikile mipata
paokha polemba ziganizozo m'[mabuku ao.
II. Aphunzi:
● Aone kasiyidwe ka mipata m'ziganizo zomwe zilibe mipata m'malembedwe okhazikika.
● Ayeselele kulemba ziganizo zopatsidwa zomwe zilibe mipata m'magulu ao.
● Azindikile mipata paokha polemba ziganizozo m'mabuku ao.
Muyeso Woyembekezeleka: Ziganizo zajambulidwa ndipo mipata asiyidwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa malembedwe okhazikika a lembo, mau ndi
kuzindikila mipata ya mau m'ziganizo.
MUTU 2: Cimangilizo
Mutu Waung’ono: Kujambula.
Ciyambi: mutu uyu uzayangana pakujambula zinthunzi zomwe zidzapeleka uthenga
yomangilizidwa pamodzi.
Luso lapadela: Kufotokoza malingalilo mwakujambula.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Phensulo, pepala, makileyoni.
Mau Ofunikila Kudziwa: zithunzi, uthenga, kujambula.
Mfundo zophunzitsila:
● Phunzitsani aphunzi kuti tingathe kufotokoza malingalilo pakujambula zomwe
tiganiza.
68
Nchito: Kujambula zocitika popanga nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi majambulidwe azithunzi zomwe zingapange nkhani ataziona.
● Uzani aphunzi kuti ajambule zithunzi za zocitika popanga nkhani.
● Pelekani nkhani yomwe izathandiza aphunzi kujambula zithunzi kuti apange nkhani.
NKHANI
Tsiku lina, mwana wa mfumu anapita kumstinje kukasambila.
Ali mkusambila anaona ng'ona ili kubwela kwa iye.
Anagwidwa ndi mantha kuopa kuti angadyedwe.
Mwamwai anatenga mwala ndi kupha nayo ng'ona.
II. Aphunzi:
● Aonelele majambulidwe a **zithunzi zomwe zingapange nkhani ataziona.
● Ajambule zithunzi za zocitika popanga nkhani.
● Alondole nkhani popanga zithunzi.
Muyeso Woyembekezeleka: Kujambula zinthunzi zosonyeza nkhani kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutuyu unali kuona pakujambula zinthunzi zomwe zipeleka uthenga
yomangilizidwa pamodzi.
CAPAMUTU 3: SEWELO
69
Ciyambi: Cigawo ici cizaona pa kucita sewelo zosiyana siyana kulingana ndi zocitika ku
nyumba ndi kusukulu. Cigawoci cizaonanso pa Kuwelenga, Mvetso komanso Kulemba. Izi
zidzathandiza aphunzi muumoyo wao watsiku ndi tsiku.
CIGAWO 1: KUMVETSELA NDI KULANKHULA
MUTU 1: Sewelo
Mutu Waung’ono 1: Kusewela
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa kucita sewelo. Sewelo lidzathandiza aphunzi kudziwa
mau ambili omwe adzagwilitsa nchito mphunzilo la kuwelenga ndi kulemba. Sewelo
lidzathandizanso aphunzi kuganiza mwakuya pokulankhula.
Luso Lapadela: Kutengako mbali kusewelo kugwilitsa nchito mau oyenela.
Mau Ofunika Kudziwa: Sewelo, kusewela, kumvetsela.
Mfundo Zophunzitsila:
• Kupatsa aphunzi mutu umene adzacitila sewelo.
• Kufotokoza maseweledwe a sewelo.
Zida Zophunzitsila Ndi Zophunzilila:
Mutu ofotokoza mfundo yasewelo, chati yowoonetsa mwana akulandila mphatso kucokela ku
makolo ndi mphunzitsi.
Nchito: Kucita sewelo zosiyana siyana kulingana ndi zocitika ku nyumba ndi
kusukulu.
I. Mphunzitsi :
70
• Ikani aphunzi m’magulu
• Fotokozelani aphunzi tanthauzo la sewelo.
• Apatseni mfundo yomwe azagwilitsa nchito pocita sewelo lao. (Ena acite sewelo loonetsa
zocitika kunyumba pomwe ena acite sewelo loonetsa zocitika ku sukulu)
Citsanzo
• Mwana ocita zabwino ku nyumba amakondweletsa makolo.
• Mwana ocita za bwino kusukulu akondweletsa aziphunzitsi.
II. Aphunzi:
• Akhale m'magulu.
• Amvetsele kutanthauzo la sewelo.
• Acite sewelo molingana ndi zigao zomwe apatsidwa.
Muyeso Woyembekezeleka
Masewelo acitidwa moyenela.
Mwacidule
Mutuyu unali kuona pakucita sewelo zosiyana. Aphunzi aonetsa luso la kumvetsela ndi
kulankhula pakucita sewelo.
CIGAWO 2: KUWELENGA
MUTU 1: Kuzindikila Masilabe
Mutu Waung’ono 1: Kuzindikila Masilabe opangidwa ndi; nz-, sh-, zy-, nkh- m’mau
okambidwa.
71
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa pa
mwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila masilabe nkha, nkhe, nkhi, nkho.
Ciyambi: Mutu uyu uzaona kuzindikila masilabe m'mau okambidwa, kusewela
masewela akuwelenga masilabe omwe ali m'mau pakuomba m’manja, ndi masewela akupanga
mau pa kusintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau atsopano.
Luso lapadela
Kuzindikila ndi kusewenzetsa masilabe.
Zida Zophunzitsila Ndi Zophunzilila
Zithunzi, zida zogwilika.
Mau Ofunika Kudziwa
Masilabe, vawelo, mvekelo.
Mfundo zophunzitsa:
● Kuzindikila masilabe m’mau okambidwa.
● Kusewela masewela owelenga masilabe.
● Kusewela masewela osintha ndi kucotsa silabe kupanga mau atsopano.
Nchito A: Kuzindikila masilabe m’mau okambidwa.
I. Mphunzitsi :
● Onetsani cithunzi kapena zinthu zogwilika zili ndi mau ali ndi ali ndi masilabe
opangidwa ndi /nkh/ mongan nkhuku.
● Fotokozani mazindikilidwe a masilabe mu liu monga khungu, khungwa, khasu, khoswe
● Citanzo:
nkhuku ili ndi zigawo ziwili - nkhu ndi ku( 2).
72
● Zindikilani masilabe ali mu liu khungu pamodzi ndi aphunzi.
II. Aphunzi :
● Apenye zithunzi kapena zinthu zogwilika zili ndi mau ali ndi mvekelo /nkh/ monga
nkhuku.
● Amvetsele kufotokoza mazindikilidwe a masilabe mu liu monga nkhuku.
Citanzo:
nkhuku ili ndi zigawo ziwili ( 2).
● Azindikile masilabe ali mu liu nkhuku mothandizidwa ndi Mphunzitsi.
Zocita:
Zindikilani masilabe m’mau okambidwa awa:
1. nkhuku– nkhu/ku
2. nkhuni- nkhu/ni
Muyeso Woyembekezeleka
Masilabe ali m'mau okambidwa azindikilidwa moyenela.
Nchito B: Kusewela masewela ozindikila masilabe m’mau poomba m’manja.
I. Mphunzitsi:
• Achule mau ali ndi mvekelo /nkh/.
Nkhata, nkhuni, nkhono.
● Sonyezani kuzindikila masilabe poomba m'manja.
73
● Uzani aphunzi awelenge masilabe ali m'mau poomba m'manja.
II. Aphunzi :
● Achule mau ali ndi mvekelo /nkh/.
● Amvetsetse mazindikilidwe a masilabe poomba m'manja.
● Awelenge masilabe ali m'mau poomba m'manja.
Zocita
Chulani mau ndi kupeza nambala ya masilabe poomba m'manja.
Nkhumba - kuomba kawili (2), ili ndi masilabe 2.
Nkhululu - kuomba katatu (3), ili ndi masilabe 3.
Nkhulungila - kuomba katatu (4), ili ndi masilabe 4.
Muyeso woyembekezeleka
Masewela ozindikila masilabe aseweledwa moyenela.
Nchito C: Kupanga mau okambidwa pogwilitsa nchito masilabe.
I. Mphunzitsi :
● Chulani masilabe nkha, nkhe, nkhi, nkho, nkhu ndi nda, ndo,
● Pelekani citsanzo cakapangidwe ka mau posewenzetsa masilabe.
Zitsanzo:
1. Nkha ndi nda apanga nkhanda.
2. Nkho ndi nda apanga nkhondo
● Uzani aphunzi apange mau ndi [Link] aphunzi alikupeza bvuto.
II. Aphunzi :
74
● Amvetsele kumachulidwe amasilabe nkha, nkhe, nkhi, nkho, nkhu ndi nda, ndo.
● Amvetsele ku citsanzo cakapangidwe ka mau posewenzetsa masilabe.
Zitsanzo
Nkha ndi nda apanga nkhanda.
Nkho ndi nda apanga nkhondo
Zocita
1. Nkha ndi ndo ipanga nkhando.
2. Nkhu ndi mba ipanga nkhumba
3. Nkho ndi no ipanga nkhono
Muyeso woyembekezeleka
Mau okambidwa kusewenzetsa masilabe apangidwa moyenela.
Nchito D: Kusewela masewela opanga mau pakucotsa ndi kusintha masilabe.
I. Mphunzitsi :
● Chulani mau awa ; nkhondo, nkhuni, nkhono.
● Uzani aphunzi kuti achule mau.
● Pelekani :citsanzo cakucotsa ndi kusintha masilabe.
Zitsanzo:
1. Nkhando – cotsani ndo ndi kuikapo nga liu tsopano ndi nkhanga.
I. Aphunzi:
● Amvetsele ku mau awa ochulidwa awa ; nkhondo, nkhuni, nkhono.
● Achule mau.
75
● Amvetsetse kucotsa ndi kusintha masilabe.
● Asinthe masilabe ndi kupanga mau atsopano.
Zocita
Sinthani silabe ndi kuikapo lina.
1. Nkhono – kucotsa no kuikapo silabe ko ipanga liu nkhoko.
Muyeso woyembekezeleka
Masewela opanga mau aseweledwa moyenela.
Mwacidule: Aphunzi aphunzila kuzindikila mvekelo, kucita masewela a kuomba
m’manja popanga masilabe ndi masewela opanga mau kugwilitsa nchito masilabe kucokela ku
mau okambidwa.
KUWELENGA
MUTU 2: Ubale wa lembo ndi mvekelo.
Mutu Waung’ono 1: Masilabe
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse kupanga masilabe pa kulumikidza makonsonanti
amodzi ndi mavawelo mpaka onse oonetsedwa pa mwambapa [Link] mwaonetsedwa
mophunzitsila kulumikidza makonsonanti ndi mavawelo.
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa kupanga masilabe kucokela ku makonsonanti ndi
mavawelo, kuwelenga masilabe pa chati la masilabe, kusankha masilabe ndi kusintha malembo.
Luso Lapadela
76
Kulumikidza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
Mau Ofunika Kudziwa
Makonsonanti , mavawelo, masilabe, kulumikidza.
Zipangizo Zophunzitsila Ndi Zophunzilila
Silabiki chati, mafulashi khadi.
Mfundo zophunzitsa:
● kulumikidza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
● Kuwelenga silabiki chati.
● Kusankha masilabe mu mau.
● Kucotsa malembo mu mau ndi kupanga mau atsopano.
Nchito A: Kupanga masilabe kugwilitsa nchito makonsonanti ndi mavawelo.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani chati la ma consonant ndi mavawelo.
Makansonanti: nz, sh, zy, nkh
Mavawelo: a e i o u
● Welengani, aphunzi naonso awelenge.
● Onetsani aphunzi molumikidzila makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
Nkh kulumikidza ndi a ipanga liu nkha.
II. Aphunzi:
● Apenye pa chati la ma consonant ndi mavawelo.
77
Makansonanti: nz, sh, zy, nkh
Mavawelo: a e i o u
● Awelenge makonsonanti ndi mavawelo.
● Apenyelele malumikidzidwe a makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
Nkh kulumikidza ndi a ipanga liu nkha.
nkh/a nkha
Muyeso Woyembekezeleka
Masilabe apangidwa moyenela.
Nchito B : Kuwelenga chati yamasilabe.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani chati ya masilabe kwa aphunzi.
● Sonyezani kuwelenga masilabe ali pa chati.
● Uzani aphunzi awelenge masilabe.
● Thandizilani aphunzi kuwelenga m’magulu masilabe ali pa chati.
II. Aphunzi:
● Aone chati ya masilabe.
● Amvetsele kuwelenga masilabe ali pa chati.
● Awelenge masilabe.
● Awelenge m’magulu masilabe ali pa chati.
Zocita
1. Lembani masilabe osowa mwa awa.
Nkha nkhe ___nkho nkhu
2. Welengani masilabe ali pa 1
78
Muyeso woyembekezeleka
Chati ya masilabe yawelengedwa moyenela.
Nchito C : Kusankha masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Chulani mau ali ndi masilabe awili ndi atatu
Nkhuni (2), nkhalango (3)
● Welengani mau achulidwa.
● Muuze aphunzi kuti mau ali ndi zigawo. Zigawo izi ndi masilabe. Sonyezani kusankha
masilabe m’mau tsopano.
Citsanzo
1. Nkhuni – nkhu/ni
2. Nkhalango – nkha/la/ngo
● Uzani aphunzi asankhe masilabe ndipo muwathandize kutelo.
II. Aphunzi:
• Achule mau ali ndi masilabe awili kapena atatu
Nkhuni – masilabe 2, nkhalango – masilabe 3
● Awelenge mau achulidwa.
● Amvetsele kuzofotokoza mphunzitsi kuti mau ali ndi zigawo. Zigawo izi ndi masilabe.
● Asankhe masilabe.
Zocita
1. lembani mau ali ndi masilabe atatu mwa awa;
nkhasi, nkhongono, nkhululu, nkhoko, nkhalango.
79
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe asankhidwa moyenela.
Nchito D : Kusintha masilabe
I. Mphunzitsi:
● Achule mau monga nkhuni ndi nkhoko.
● Sonyezani aphunzi kusintha lembo.
Citsanzo:
Nkhuni – sinthani lembo la n ndi kuikapo lembo la l.
Liu likhala nkhuli.
● Uzani aphunzi asinthe lembo mu mau kupanga liu latsopano m’magulu. Thandizani
aphunzi.
II. Aphunzi:
● Amvtsele kuchulidwa kwa mau.
Achule mau nkhuni ndi nkhoko.
● Amvetsetse kasinthidwe ka lembo ku citsanzo copelekedwa.
● Asinthe lembo m’mau kupanga liu latsopano m’magulu.
Zocita
Pezani mau atatu (3) ndi kusintha lembo kupanga mau atsopano.
1. Nkhoko sinthani lembo la k lili kufupi ndi kothela kuikapo n.
Liu latsopano ndi ___
2. Nkhando sinthani a kuikapo o liu latsopano ______
80
Muyeso Woyembekezeleka
Malembo asinthidwa moyenela.
Nchito E: Kulumikidza malembo ophatikizana koma omveka mosiyana
amakonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca malembo ophatikizana koma omveka mosiyana amakonsonanti
monga nkh.
● Lumikidzani makonsananti ndi mavawelo kupanga silabe.
Citsanzo
nkh ndi a ipanga silabe nkha
● Uzani aphunzi apange masilabe kugwilitsa nchito makonsonanti nkh ndi mavawelo
a e i o u. awili awili.
Zocita
Lumikidzani malembo ophatikizana koma omveka mosiyana amakonsonanti ndi mavawelo
kupanga masilabe.
a e i o u
nkh
Muyeso Woyembekezeleka
Malembo ophatikizana koma omveka mosiyana amakonsonanti ndi mavawelo alumikizidwa ndi
kupanga masilabe moyenela.
81
Cidule: Mutu uyu unali kuona pa kupanga masilabe kucokela ku makonsonanti ndi
mavawelo, kuwelenga masilabe pa chati la masilabe, kusankha masilabe ndi kusintha malembo.
B. KUWELENGA
MUTU 1: Kupanga Mau
Mutu Waung’ono 2: Mau
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa kulumikidza masilabe kupanga mau, kusintha ndi
kucotsa masilabe kupanga mau atsopano, kuzindikila masilabe mu mau ndi kuwelenga masilabe.
Luso Lapadela: Kulumikiza masilabe popanga mau.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Silabiki chati, mafulashi khadi
Mau Ofunikila Kudziwa: Makonsonanti, mavawelo, masilabe, kulumikidza
Mfundo zophunzitsa:
● Kulumikidza masilabe kupanga mau
● Kusinthanitsa ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano
● Kuzindikila masilabe m'mau
● Kuwelenga masilabe m'mau
Nchito A: Kusakaniza masilabe popanga mau
I. Mphunzitsi:
● Onetsani aphunzi mapangidwe a mau pogwilitsa nchito masilabe opangidwa ndi mvekelo
/nkh/.
82
Citsanzo:
1. Nkho/ndo nkhondo
2. Nkhe/zyo nkhezyo
● Uzani aphunzi kuti apange mau m'magulu ao pogwilitsa nchito masilabe opangidwa ndi
mvekelo /nkh/.
● Uzani aphunzi kuti apange mau paokha pogwilitsa nchito masilabe opangidwa ndi
mvekelo /nkh/
II. Aphunzi:
Aonetsetse mapangidwe a mau pogwiltsa nchito masilabe opangidwa ndi mvekelo /nkh/
● Apange mau m'magulu ao pogwilitsa nchito masilabe opangidwa ndi mvekelo /nkh/.
● Apange mau paokha pogwilitsa nchito masilabe opangidwa ndi mvekelo /nkh/
Muyeso woyembekezeleka: Masilabe asakanizidwa moyenela popanga mau.
Nchito B: Kusinthanitsa ndi kucotsela masilabe
I. Mphunzitsi
● Onetsani aphunzi kasinthidwe ndi kacotsedwe ka masilabe popanga mau ena.
● Ikani aphunzi m'magulu ndipo muwauze kuti asinthe ndi kucotsa masilabe popanga mau.
Citsanzo
Kusintha
1. Nkhawa nkhanza
Kucotsa
2. Nkholoko Loko
● Funsani aphunzi kuti apange mau posinthanitsa ndi kucotsela masilabe m'mau.
83
II. Aphunzi
● Aonelele kasinthidwe ndi kacotsedwe ka masilabe popanga mau ena.
● Asinthe ndi kucotsa masilabe popanga mau.
● Apange mau posintha ndi kucotsa masilabe m'mau.
Muyeso woyembekezeleka: kusinthanitsa ndi kucotsela masilabe kupanga mau kwacitika
moyenela
Nchito C: Kuzindikile masilabe m’mau.
I. Mphunzitsi
● Phunzitsani kazindikilidwe ka masilabe m'mau.
● Patsani aphunzi mau omwe ali ndi masilabe opangidwa ndi mvekelo /nkh/ ndipo
muwauze kuti azindikile zigao za masilabe zomwe zimveka m'mauwo.
Citsanzo
1. Nkhalango nkha/la/ngo
2. Nkhuku nkhu/ku
Uzani aphunzi kuti azindikile masilabe onenedwa m’mau poika kamzele munsi mwa silabe.
Citsanzo
1. Mankhama
2. Nkhulungo
II. Aphunzi
● Amvetsele pomwe aphunzitsi akuphunzitsa kazindikilidwe ka masilbe.
● Azindikile zigao za masilabe zomwe zimveka m'mau.
● Azindikile masilabe onenedwa m’mau poika kamzele munsi mwa silabe.
Muyeso woyembekezeleka: Masilabe azindikilidwa moyenela.
84
Nchito D: Kuwelenga masilabe
I. Mphunzitsi
● Phunzisani kawelengedwe ka masilabe m'mau.
● Uzani aphunzi kuti awelenge nambala ya masilabe m’mau opatsidwa omwe ali ndi
mvekelo /nkh/ m'magulu ao.
Citsanzo
1. Nkhondowosi 4
2. Nkhuzyeni 3
● Patsani aphunzi nchito yowelenga masilabe m'mau omwe ali ndi mvekelo /nk/ paokha.
Aphunzi
● Amvetsetse pomwe aphunzitsi akuphunzitsa kawelengedwe ka masilabe m'mau.
● Awelenge nambala ya masiabe m’mau ali ndi mvekelo /nkh/ m'magulu ao.
● Awelenge nambala ya masilabe m'mau ali ndi mvekelo /nk/ paokha.
Muyeso woyembekezeleka: Aphunzi azindikila namabala ya masilabe m’mau osiyana-siyana
moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kulumikidza masilabe kupanga mau, kusintha ndi
kucotsa masilabe kupanga mau atsopano, kuzindikila masilabe mu mau ndi kuwelenga masilabe.
KUWELENGA
MUTU 3: Kuwelenga mofulumila
85
Luso lapadela1: Kuwelenga mau mokweza ndi kaculidwe ka mau koyenela.
Nchito : Kuwelenga mau
I. Mphunzitsi:
● Phunzitsani aphunzi kawelengedwe ka mau omwe ali ndi mvekelo /nkh/ mokweza
komanso mosamala kaculidwe ka mau.
● Ikani aphunzi m'magulu ndipo muwapatse mau omwe ali ndi mvekelo /nkh/ kuti
awelenge mosamala kaculidwe ka mau.
● Patsani aphunzi mau ndipo muwauze kuti awelenge paokha mosamala kaculidwe ka mau.
II. Aphunzi:
● Aphunzile kawelengedwe ka mau omwe ali ndi mvekelo /nkh/ mokweza komanso
mosamala kaculidwe ka mau.
● Awelenge mau ali ndi mvekelo /nkh/ mokweza komanso mosamala kaculidwe ka mau.
● Awelenge mau ali ndi mvekelo /nkh/ paokha mosamala kaculidwe ka mau.
Muyeso woyembekezeleka: Mau awelengedwa moyenela.
Luso Lapadela 2: Kuwelenga nkhani mokweza ndi kaculidwe ka mau koyenela.
Nchito A:Kuwelenga ndi kumvetsetsa nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Phunzitsani kawelengedwe ka nkhani ndi kayankhidwe ka mafunso mokweza ndi
mosamala kaculidwe ka mau.
● Patsani aphunzi nkhani ndipo muwauze kuti awelenge m'magulu ao.
Nkhani:
Mnkhalango mumapezeka nyama zosiyana-siyana.
Nkhandwe ndi imodzi mwa nyama zazikali nkhalango.
86
Tiyenela kusamalila nkhalango.
● Funsani aphunzi mafunso pazomwe awelenga.
II. Aphunzi:
● Amvetsetse pomwe aphunzitsi akuphunzitsa kawelengedwe ka nkhani ndi kayankhidwe
ka mafunso mokweza ndi mosamala kaculidwe ka mau.
● Awelenge nkhani m'magulu ao
● Ayankhe mafunso ocokeloa mnkhani yomwe awelenga.
Mafunso
1. Kodi nyama zikhala kuti?
2. Chulani nyama yomwe mwamva mnkhani.
3. Fotokozani ubwino umodzi cabe wosamalila nkhalango.
Muyeso woyembekezeleka: Ziganizo zawelengedwa ndipo mafunso ayankhindwa moyenela.
Nchito B: Kuwelenga nkhani ya ziganizo zapakati pa ziwili ndi zitatu. (Kuwelenga
kwa bgulu, kubwelezela zomwe wina akuwelenga ndi kuwelenga awili-awili.
I. Mphunzitsi :
● Onetsani aphunzi kawelengedwe ka nkhani mokweza ndi maculidwe a mau oyenela
● Patsani aphunzi nkhani kuti awelenge m'magulu ao.
Nkhani:
Tsiku lina, atate anapita ku nkhalango kukatema nkhuni.
Alikutema nkhuni, anaona nthudza zakupsa mu mtengo.
Anakondwela kwambili cifukwa anli ndi njala.
87
● Uzani aphunzin kuti akhale awili-awili ndipo muwapatse kabuku ka nkhani kuti
awelenge.
II. Aphunzi
● Amvetsetse pomwe aphunzitsi akuphunzitsa kawelengedwe ka nkhani mokweza ndi
maculidwe a mau oyenela
● Awelenge nkhani m'magulu ao.
● Awelenge nkhani awili-awili mokweza ndi maculidwe a mau oyenela.
Nchito C: Kuwelenga nkhani zili ndi mvekelo zosiyana-siyana komanso
zolumikizidwa.
I. Mphunzitsi
● Phunzitsani kawelengedwe ka nkhani ili ndi mau ali ndi mvekelo/nkh/ polata masilabe
ndi mau ali m'nkhani.
● Ikani aphunzi m'magulu kapena awili-awili ndipo muwapatse nkhani kuti awelenge
polata masilabe ndi mau omwe ali kuwelenga.
● Uzani aphunzi kuti alembe nkhani ndi kuika kamzele munsi mwa mau omwe ali ndi
silabe ya mvekelo /nkh/.
II. Aphunzitsi:
● Amvetsetse pomwe aphunzitsi ali kuphunzitsa kawelengedwe ka nkhani ili ndi mau ali
ndi mvekelo/nkh/ polata masilabe ndi mau ali mnkhani.
● Awelenge awili-awili polata masilabe ndi mau omwe ali m'nkhani.
● Alembe ziganizo ndi kuika kamzele munsi mwa mvekelo /nkh/ m'mau.
Muyeso Woyembekezeleka: Nkhani zili ndi mvekelo zosiyana-siyana komanso zolumikizidwa
yawelengedwa moyenela.
Mwacidule: mutu uyu unali kuona pa kuwelenga mau mokweza ndi maculidwe a mau
oyenela komanso pa kuwelenga ziganizo mokweza ndi maculidwe a mau oyenela.
88
CAPAMUTU 4: MVETSO
MUTU 1: Mvetselo ya Kumvetsela
Mutu Waung’ono 1: Maganizo yeni-yeni.
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa kuzindikila ndi kutulutsa maganizo yeni-yeni pa zomwe
amva.
Luso Lapadela: Kupeleka maganizo eni-eni kulingana ndi zomwe zamva.
Zipangizo Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Makhadi a ziganizo, mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: Maganizo, mvetselo.
Mfundo zophunzitsa:
● Kuphunzitsa m’mene aphunzi angapelekele maganizo ao pa zomwe amva kapena
kuwelenga.
● Kuwelenga nkhani kwa aphunzi ndi kuwafunsa mafunso mwakulankhula cabe.
● Kuuza aphunzi kuti apeleke cigamulo kulingana ndi zomwe amva.
Nchito A: Kuzindikila ndi kupeleka maganizo yeni-yeni pa zomwe amva
I. Mphunzintsi:
● Uzani aphunzi kuti amvetsele ku nkhani yomwe muzanena cabe ndipo apeleke maganizo
ao kulingana ndi zomwe azamva.
● Nenani nkhani yapamtina ndipo aphunzi amvetsele ndi kupeleka maganizo ao.
● Aphunzi
● Amvetsele ku nkhani ndi kupeleka maganizo ao kulingana ndi zomwe amva.
Muyeso Woyembekezeka: Aphunzi apeleka maganizo eni-eni kulingana ndi zomwe amva
moyenela.
89
Nchito B: Kufupikitsa uthenga.
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti afotokoze nkhani yomwe amva mwakutengamo cabe mfundo zeni-
yeni.
II. Aphunzi:
● Afupikitse nkhani kulingana ndi zomwe amva.
Muyeso Woyembekezeleka: Nkhani yafupikitsidwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kufupikitsa maganizo kulingana ndi zomwe amva.
Mutu Waung’ono 2: Zoona ndi malingalilo
Ciyambi: Mutu uyu udzaona pa kuzindikila malingalilo mu nkhani ndi kuzindikila zoona
mu nkhani.
Luso Lapadela: Kusiyanitsa zoona ndi malingalilo.
Mau Ofunika Kudziwa: zoona, malingalilo, maganizo, kusiyanitsa nkhani.
Mfundo Zophunzitsa:
● Tanthauzo la mau “malingalilo, maganizo”, zoona.
● Kusiyanitsa zoona ndi malingalilo kapena kuti maganizo.
Nchito A: Kuzindikila zotuluka m’maganizo mu nkhani
I. Mphunzitsi:
● Kambani kankhani kosangalatsa kwa aphunzi.
Nkhalango ya akalulu
90
Kalulu ndi kanyama kokhala m’nkhalango.
Anthu ambili amakonda nkhani zake.
Iwo amati “Kakalulu ndi kocenjela kwambili”.
Iko kamanamiza nyama zinzake nthawi zambili.
Kalinso ndi liwilo loculuka zedi.
● Funsani aphunzi ngati kalulu amamudziwa.
● Afunseni za maonekedwe ake.
● Afunseni za nkhani zomwe anamva zokhudza kalulu.
● Uzani aphunzi kuti nkhani zomwe amamva zokhudza kalulu monga yakuti “kalulu ndi
mfumu ya m’nkhalango” ndi malingalilo cabe a anthu.
● Uzani Aphunzi kuti anene nkhani zomwe adziwa yokhudza Kalulu.
II Aphunzi:
● Amvetsele kwa mphunzitsi pomwe akusimba kankhani kosangalatsa.
● Anene ngati Kalulu amamudziwa.
● Anene za maonekedwe a kalulu.
● Anene nkhani zomwe anamva zokhudza kalulu.
● Amvetsele modekha kwa mphunzitsi pomwe akufotokoza za malingalilo a anthu.
● Anene nkhani zomwe adziwa yokhudza kalulu.
Muyeso Woyembekezeleka: Malingalilo a m’nkhani azindikilidwa moyenela.
Nchito B: Kuzindikila zoona mu nkhani.
I Mphunzitsi:
• Kambani kankhani kosangalatsa kwa aphunzi.
Nkhani:
Nkhalango ya akalulu
91
Kalulu ndi kanyama kokhala m’nkhalango.
Anthu ambili amakonda nkhani zake.
Iwo amati “Kakalulu ndi kocenjela kwambili”.
Iko kamanamiza nyama zinzake nthawi zambili.
Kalinso ndi liwilo loculuka zedi.
Funsani aphunzi ngati kalulu amamudziwa.
● Afunseni za maonekedwe ake.
● Afunseni za nkhani zomwe anamva zokhudza kalulu.
● Uzani aphunzi kuti zeni-zeni za Kalulu monga maonekedwe ndi zakudya zake ndi zimene
timati zoona.
● Uzani Aphunzi kuti anene zoona za kalulu zimene adziwa.
II Aphunzi:
● Amvetsele kwa mphunzitsi pomwe akusimba kankhani kosangalatsa.
● Anene ngati Kalulu amamudziwa.
● Anene za maonekedwe a kalulu.
● Anene nkhani zomwe anamva zokhudza kalulu.
● Anene zeni-zeni zokhudza kalulu.
● Anene nkhani zoona zimene adziwa zokhudza kalulu.
Muyeso Woyembekezeleka: Zoona zasiyanitsidwa ndi malingalilo moyenela.
Mutu uyu unali kuona pa kusiyanitsa zoona ndi malingalilo ndiponso kuzindikila zoona mu
nkhani.
MVETSO
Mutu 2: Mvetso ya kuwelenga.
Mutu Waung’ono: Zoona za nkhani.
92
Ciyambi: Mutu Waung’ono uyu udzaona pa Kufotokoza zomwe zawelengedwa,
kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa ndi kufotokoza zocitika m’nkhani
molondola.
Luso Lapadela: Kupeleka uthenga wocokela m’nkhani wofotokozedwa mokwanila.
Mau Ofunika Kudziwa: Kufotokoza, nkhani, molondola, mokwanila.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Mabuku a Aphunzi owelenga, mabuku a nthano.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuwelenga nkhani.
● Kufufuza zoona za nkhani.
● Kuzindikila zoona za nkhani.
Nchito A: Kufotokoza zomwe zawelengedwa m’nkhani.
II. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani yosonyeza amene anacita nkhani, kumene nkhani inacitikila ndi
m’mene nkhani inacitikila pomwe aphunzi akumvetsela modekha.
● Fufuzani zoona za nkhani mwa kukambilana ndi aphunzi zomwe zawelengedwa.
● Pezani mfundo zothandiza kuti muzindikile zoona za nkhani.
● Uzani Aphunzi kuti Awelenge nkhani ndi kuyankha mafunso kucokela ku nkhani yomwe
yawelengedwa.
II Aphunzi:
● Amvetsele ku nkhani yomwe mphunzitsi wawelenga yosonyeza amene anacita nkhani,
kumene nkhani inacitikila ndi m’mene nkhani inacitikila.
● Kufufuza nkhani mwa kukambilana ndi mphunzitsi.
● Kupeza mfundo zothandiza kuti azindikile zoona za nkhani.
93
● Awelenge nkhani ndi kuyankha mafunso.
Muyeso Woyembekezeleka: Kufotokoza zomwe zawelengedwa m’nkhani kwacitidwa
moyenela.
Nchito B: kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa.
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kuwelenga nkhani.
● Pamodzi ndi aphunzi, kambilanani zomwe zawelengedwa.
● Funsani Aphunzi mafunso kucokela ku nkhani yomwe yawelengedwa.
II Aphunzi:
● Amvetsele ku citsanzo ca kuwelenga kwa mphunzitsi.
● Akambilane ndi mphunzitsi zomwe zawelengedwa.
● Ayankhe mafunso kucokela ku nkhani yomwe yawelengedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuyankha mafunso kucokela ku nkhani yomwe yawelengedwa
kwacidwa moyenela
Nchito C: Kufotokoza zocitika m’nkhani molondola.
I Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi.
● Uzani aphunzi kuti awelenge nkhani yomwe yawelengedwa ndi mphunzitsi.
● Pamodzi ndi aphunzi, kambilanani ndi aphunzi zomwe zawelengedwa.
● Funsani aphunzi mafunso kucokela ku nkhani yowelengedwa.
II Aphunzi:
● Awelenge nkhani yomwe mphunzitsi wawelenga.
● Akambilane zomwe zawelengedwa m’nkhani.
94
● Amvetsele ku nkhani pomwe mphunzitsi akuwelenga.
Muyeso Woyembekezeleka: Kufotokoza zocitika m’nkhani kwacitidwa
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa Kufotokoza zomwe zawelengedwa m’nkhani ,
kuyankha mafunso kucokela ku nkhani yomwe yawelengedwa ndi kufotokoza zocitika m’nkhani
molondola.
CIGAWO 5: MALEMBEDWE
Mutu: Malembedwe
Mutu waung’ono 1: Mapangidwe a Lembo
Ciyambi: Mutu uyu udzaona pa kujambula malembo, kulemba malembo, kulemba
mam’malembedwe okhazikika ndi kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika posiya
mipata pakati pa mau.
Luso Lapadela: Kulemba malembo
Mau Ofunika Kudziwa: Malembedwe, owelengeka, okhazikika, mpata, kujambula.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Coko, phensulo, mabuku olembamo aphunzi.
Mfundo zophunzitsa:
● Kusonyeza majambulidwe a malembo kucokela koyambila polemba mpaka kumapeto
poonetsa mayendedwe a dzanja lomwe lili ndi colembela.
● Malembedwe a malembo opatsidwa.
● Kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika posiya mipata pakati pa mau.
Nchito A: Kujambula malembo
95
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kulemba malembo awa /n, k, h / m’malembedwe okhazikika
m’mizela olembedwelatu pa bolodi.
nnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnnn
Kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk
kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk
● Uzani aphunzi kuti ajambule malembo monga m’citsanzo canu pa bolodi ndipo
muwaongolele pomwe akujambula.
● Uzani aphunzi kuti ajambule malembo omwe alembedwa pa bolodi m’mabuku ao
olembamo.
II. Aphunzi:
● Aonetsetse pomwe mphunzitsi akulembela malembo m’malembedwe okhazikika
m’mizela olembedwelatu pa bolodi.
● Ajambule malembo monga m’citsanzo ca mphunzitsi pa bolodi mothandizidwa ndi
mphunzitsi..
● Ajambule malembo omwe alembedwa pa bolodi m’mabuku ao olembamo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kujambula malembo kwacitika moyenela.
Nchito B: Kulemba malembo (nz, zy, sh, nkh)
I. Mphunzitsi:
● Sonyezani m’mene malembo alembedwela m’malembedwe okhazikika m’mizela
olembedwelatu pa bolodi.
● Onetsani aphunzi mayambidwe a kulemba malembo kucokela koyambila mpaka
kumapeto.
● Uzani aphunzi kuti adzalembe malembo m’mizela ali pa bolodi.
● Uzani aphunzi kuti alembe malembo opatsidwa m’mabuku ao olembamo.
96
II Aphunzi:
● Aonetsetse m’mene mphunzitsi akulembela malembo pa bolodi m’mizela
olembedwelatu.
● Aonetsetse mayambidwe a kulemba lembo kucokela koyambila mpaka kumapeto kwa
lembo.
● Uzani aphunzi kuti adzalembe malembo m’mizela omwe ali pa bolodi.
● Alembe malembo omwe apatsidwa m’mabuku ao olembamo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kulemba malembo kwacitika moyenela.
Mutu Waung’ono 2: Malembedwe Okhazikika
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pa malembedwe okhazikika.
Luso lapadela: Kulemba mau m’malembedwe okhazikika.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Silabiki Chati, Mafulashi Khadi, Makhadi a Ziganizo,
Mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: Kulemba, Kukhazikika, Lembo, Malembedwe.
Mfundo Zophunzitsa:
● Uzdani aphunzi malamulo amalembedwe omwe afunika kulondoledwa polemba.
● Fotokozani za lamulo La malembo amucila wopita kumwamba komanso micila wopita
pansi mumalembedwe
Nchito A: Kujambula Mau M’malembedwe Okhazikika.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca malembedwe a mau polondola malembedwe okhazikika ndiponso
polemekeza micila yopita kumwamba komanso pansi.
97
Citani cimodzi-modzi ndi Malemba ena.
II. Aphunzi:
● Amvetsele citsanzo ndiponso alembe mau molondola bwino zomwe aphunzitsidwa
pakalembedwe ka malembo.
Zocita
Jambulani mau awa m’malembedwe okhazikika.
1. Nkhono.
2. Nkhumba.
3. Nkhani
Muyeso Woyembekezeleka: Mau alembedwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pakalembedwe ka mau kokhazikika.
Mutu Waung’ono 3: Mipata ya mau.
Ciyambi: Mutu uyu uzayangana pa malembedwe okhazikika.
Luso lapadela: kusiya mipata m’mau.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Fulashi khadi, makhadi a ziganizo, mabuku.
Mau Ofunikila Kudziwa: Kulemba, Kukhazikika, Lembo, Mipata.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kusiya mipata polemba mau m’ziganizo.
● Lamulo La malembo amucila wopita kumwamba komanso pansi.
98
Nchito A: Kujambula Ziganizo M’malembedwe Okhazikika.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca malembedwe a ziganizo pozindikila ndi kusiya mipata pakati pa
mau.
Citani cimodzi-modzi ndi mvekelo zina.
II. Aphunzi:
● Alembe ziganizo ndi kulemekeza kusiya mipata pakati pa mau.
Zocita
Jambulani ziganizo izi m’malembedwe okhazikika.
1. Nkhono ipezeka kumtunda ndi m’madzi.
2. Nkhumba ndi nyama yoweta.
Muyeso woyembekezeleka: Malembedwe okhazikika alembedwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pakalembedwe ka mau kokhazikika.
MUTU 2: Cimangilizo
Mutu Waung’ono: Nkhani Yapafupi
Ciyambi: Mutu uyu uzayanga’na pakujambula zinthunzi zomwe zidzapeleka uthenga
womangilizidwa pamodzi.
Luso Lapadela: Kulemba nkhani yapafupi
99
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Phensulo, Pepala, Makileyoni.
Mau Ofunikila Kudziwa: Zithunzi, Uthenga, Kujambula.
Mfundo Zophunzitsila:
● Fotokozelani aphunzi kuti tingathe kufotokoza malingalilo pakulemba nkhani yapafupi
yomwe tiganiza.
● Patsani citsanzo camalingalilo omwe angalembedwe mkankhani kapafupi.
Nchito: composing a simple story
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti alembe kankhani kapafupi pa cinthu comwe akonda kwambili
● Pelekani citsanzo ca nkhani yapafupi
Nkhani
Amai apita kumunda.
Popita ambeleka mwana ndiponso anyamulanso thadza la manga pamutu.
Mwatsoka, poyenda akhumudwa ndipo thadza lagwa pansi.
II. Aphunzi:
● Amvetsele nkhani yokambidwa ndi mphunzitsi.
● Alembe nkhani yao-yao yapafupi
Muyeso Woyembekezeleka: Kulemba nkhani yaifupi kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutuyu unali kuona kulemba nkhani yapafupi yao-yao aphunzi
100
CAPAMUTU 4 : KUKAMBA ZILAPI
Ciyambi: Cigawo cidzaona pa Kumvetsela ndi Kulankhula, Kuwelenga, Kuwelenga
Mofulumila ndi Matanthauzo a Mau. Cidzaonanso pa ku Mvetsela, Mvetso, Kulemba ndi
Cimangilizo.
Kumvetsela Ndi Kulankhula
Mutu 1: Zilapi ndi Zopindika Lilime
Mutu Waung’ono 1 : Zilapi
Lambulo: Mutu uwu udzayanga pakukamba ndi kuyankha zilapi.
Luso lapadela:Kukamba ndi kuyankha zilapi
Mau ofunika kudziwa: Zilapi, matanthauzo.
Zida Zophunzitsila ndi Kuphunzilila: Zithunzi
Mfundo Zophunzitsa:
● Kunena zilapi.
● Matanthauzo a zilapi.
Nchito : Kukamba ndi kuyankha zilapi.
I. Mphunzitsi:
● Fotokozani za zilapi kuti zili ndi matanthauzo obisika.
● Onetsani cithunzi ca nyumba. Funsani ngati cili ndi khomo.
● Pelekani citsanzo.
Nyumba ya amai ilibe khomo.
101
Yankho ndi dzila.
● Nenani zilapi zina. Aphunzi ayankhe.
● Uzani aphunzi acite mpikisano m’magulu.
II. Aphunzi:
● Amvetsele kufotokoza za zilapi.
● Apenye cithunzi ca nyumba kuti cili ndi khomo.
● Amvetsele ku citsanzo.
● Apeleke mayankho a zilapi.
● Acite mpikisano m’magulu.
Zocita:
Pezani matanthauzo a zilapi izi.
1. Mumandimwa koma sindigwilika.
2. Ndili ndi miyendo 4, koma sindiyenda.
3. Mumagona ndi kalowa.
Mayankho:
1. Madzi
2. Thebo
3. Dzuwa
Muyeso Woyembekezeleka: Zilapi zakambidwa ndi kuyankhidwa moyenela.
Cidule: Mutu uwu unali kuona pakukamba ndi kuyankha zilapi.
KUWELENGA
Mutu 1: Kuzindikila Masilabe
102
Mutu Waung’ono 1: Kuzindikila Masilabe opangidwa ndi mph-, nth-, nch-, ngw-, mny-,
m’mau okambidwa.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse masilabe opangidwa ndi malemba opatsidwa imodzi-
imodzi mpaka onse oonetsedwa pa mwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila
masilabe ntha, mpha, mphe, mphi, mpho, mphu.
Lambulo: Mutu uyu udzaona pa kuzindikila masilabe m’mau okambidwa, kusewela
masewela owelenga masilabe, kupanga mau kugwilitsa nchito masilabe ndi kusewela masewela
osintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau atsopano.
Luso lapadela: Kuzindikila ndi kugwilitsa nchito masilabe.
Mau Ofunika Kudziwa : Silabe, mvekelo.
Zida Zophunzitsila ndi Kuphunzilila: Zithunzi
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuzindikila masilabe m’mau okambidwa.
● Kusewela masewela amasilabe.
Nchito A : Kuzindikila ndi kugwilitsa nchito masilabe mu mau okambidwa.
I. Mphunzitsi :
● Onetsani cithunzi ca mphasa ndi zinthu zina zili ndi silabe lili ndi mvekelo la /mph/
mu silabe.
● Chulani zinthu zili pa cithunzi.
● Chulani masilabe ali mu liu mphasa.
Citsanzo:
Mpha ndi sa
103
● Zindikilani masilabe mpha ndi mphe pamodzi ndi aphunzi m’mau okambidwa.
1. Mphale – mpha
2. Mphepo - mphe
II. Aphunzi:
● Apenye cithunzi ca mphasa ndi zinthu zina zili ndi masilabe ali oyamba ndi /mph/.
● Aone cithunzi ca mphasa ndi zinthu zina zili ndi silabe lili ndi mvekelo la /mph/ mu
silabe.
● Achule zinthu zili pa cithunzi.
● Anene masilabe ali mu liu mphasa.
Citsanzo:
Mpha ndi sa
● Azindikile masilabe mpha ndi mphe pamodzi ndi Mphunzitsi m’mau
okambidwa.
3. Mphale – mpha
4. Mphepo - mphe
Zocita:
1. Akambe masilabe mpha mphe mphi mpho mphu ali m’mau awa;
mphala, mphika, mphuno, mphemvu, mphongo.
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe azindikilidwa m’mau okambidwa moyenela.
Nchito B : Kusewela masewela owelenga masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Gwilitsani nchito chati ili ndi zithunzi za mphika ndi mphuno kuyamba phunzilo.
● Chulani mau mphika ndi mphuno.
● Sonyezani kupeza nambala ya masilabe mu mau okambidwa poomba m’manja pa
silabe lililonse.
● Thandizani aphunzi kucita sewelo loomba m’manja.
Citsanzo
104
mphika – kuomba kawili(2). mphi, kuomba 1 ndi ka kuomba 2.
II. Aphunzi:
● Apenye zithunzi za mphika ndi mphuno.
● Achule mau mphika ndi mphuno.
● Akambe masilabe pha phe phi pho phu .
● Amvetsele kumapezedwe a nambala ya masilabe pa liu poomba m’manja pa silabe
lililonse.
● Aombe m’manja pa silabe lili lonse mu liu mphika ndi mphuno kupeza nambala ya
masilabe.
Zocita:
Apeze nambala ya masilabe m’magulu amau awa poomba m’manja.
1. Mphako 2. Mphelo 3. Mphila 4. Mphemvu 5. Mphumi
Muyeso Woyembekezeleka: Masewela owelenga masilabe aseweledwa moyenela.
Nchito C : Kupanga mau okambidwa kulumikidza masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Chulani masilabe awa : mpha mphe mphi mpho mphu.
● Chulani masilabe ena monga le ndi mvu.
● Sonyezani kulumikidza masilabe.
Citsanzo:
Silabe mpha ndi mvu, ipanga mau mphamvu.
Silabe mphe ndi le, ipanga mphele.
● Uzani aphunzi apange mau m’magulu ndipo muwathandize.
II. Aphunzi:
● Amvetsele kuchulidwa kwa masilabe awa : mpha mphe mphi mpho mphu.
● Achule masilabe ena monga le ndi mvu.
105
● Amvetsele kulumikidza masilabe kulondola zitsanzo.
● Apange mau m’magulu mothandizidwa ndi Mphunzitsi..
Zocita:
Pangani mau asanu ( 5) ndi masilabe awa;
Mpha mphe mphi mpho mphu
tso la mi mvu ngo
Mayankho:
Mphatso mphemvu mphila mphongo mphuno
Muyeso Woyembekezeleka: Mau okambidwa apangidwa polumikidza masilabe moyenela.
Nchito D : Kusewela masewela osintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau atsopano.
I. Mphunzitsi:
● Chulani mau monga mphika, mphala ndi mphele.
● Sonyezani kusintha masilabe ndi kupanga mau ena.
Citsanzo:
mphaka kusintha silabe mpha ndi kuikapo silabe mphi, ipanga liu mphika.
● Pelekani citsanzo kucotsa silabe kupanga mau atsopano.
Citsanzo
Mnyamata kucotsa mnya, liu likhala mata.
● Uzani aphunzi asinthe ndi kucotsa masilabe kupanga mau atsopano m’magulu
II. Aphunzi:
● Achule mau monga mphika, mphala ndi mphele.
● Alondole citsanzo cosintha masilabe ndi kupanga liu latsopano.
● Amvetsele ku citsanzo cakucotsa silabe kupanga liu latsopano.
106
● Asinthe ndi kucotsa masilabe kupanga mau atsopano m’magulu mothandizidwa ndi
mphunzitsi.
Muyeso Woyembekezeleka: Masewela opanga mau aseweledwa moyenela.
Cidule: Mutu uyu unali kuona pa kuzindikila masilabe m’mau okambidwa, kusewela
masewela owelenga masilabe, kupanga mau kugwilitsa nchito masilabe ndi kusewela masewela
osintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau atsopano.
Mutu 2 : Kupanga Masilabe
Mutu Waung’ono 1 : Masilabe
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse kupanga masilabe pa kulumikidza makonsonanti
amodzi ndi mavawelo mpaka onse oonetsedwa pa mwambapa [Link] mwaonetsedwa
mophunzitsila kulumikidza makonsonanti ndi mavawelo.
Mpha mphe mphi mpho mphu
Lambulo: Mutu uyu udzaona pa kulumikidza makonsonati ndi mavawelo kupanga
masilabe, kuwelenga chati la masilabe, kusankha masilabe, kusintha lembo ndi kulumikidza
malembo ophatikizana koma omveka mosiyana ndi mavawelo.
Luso lapadela: Kulumikidza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
Mau Ofunika Kudziwa : Makonsonanti, mavawelo, kulumikidza, mamvekedwe.
Zida Zophunzitsila ndi Kuphunzilila: Zithunzi , Silabiki chati, ma fulashi khadi.
Mfundo Zophunzitsa
● Kulumikidza konsonati ndi vawelo.
107
● Kupanga silabe.
● Kuwelenga silabiki chati.
● Kusankha masilabe.
● Kusintha lembo.
Nchito A: Kupanga masilabe polumikidza makonsonanti ndi mavawelo.
I. Mphunzitsi:
● Sonyezani kapangidwe ka silabe polumikidza konsonanti ndi vawelo. kapangidwe ka
silabe kugwilitsa nchito makonsonanti m p h ndi mavawelo a e i o u.
mph kulumukidza a ipanga mpha
mph ndi e ipanga mphe
● Welengani masilabe.
● Thandizani aphunzi kulumikidza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
II. Aphunzi:
● Apenyetsetse kapangidwe ka silabe kugwilitsa nchito makonsonanti m p h ndi
mavawelo a e i o u.
● Awelenge masilabe.
● Alumikidze makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe mothandizidwa
ndi mphunzitsi
Zocita:
Lumikidzani makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
mpha mphe mphi mpho mphu
la le li lo lu
1. Mphala
2. _____lo
3. Mphi___
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe anapangidwa polumikidza makonsonanti ndi mavawelo
moyenela.
108
Nchito B: Kuwelenga chati la masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Chulani masilabe mpha ntha ncha ngwa mnya.
● Welengani silabiki chati lili ndi masilabe ali ndi masilabe achulidwa.
Citsanzo:
makansonanti a e i o u
mph mpha mphe mphi mpho mphu
● Thandizani aphunzi kuwelenga motele onse masilabe ali ndi mvekelo zili mcigawo ici.
II. Aphunzi:
● Achule masilabe.
● Awelenge chati la masilabe .
● Awelenge chati la masilabe m’magulu.
Zocita:
Pezani masilabe osowa
1. Mpha mphe mphi mpho mphi
2. Ntha nthe nthi ntho ____
3. Ngwa ngwe __ ngwo ngwu
Muyeso Woyembekezeleka: Chati la masilabe lawelengedwa moyenela.
Nchito C: Kusankha masilabe.
I. Mphunzitsi:
109
● Chulani mau ali ndi masilabe awili (2), atatu (3) ndi anai (4).
● Sewenzetsani mafulashi khadi ali ndi mau omwe ali ndi masilabe 2, 3 ndi 4.
● Thandizani aphunzi kuwelenga mau ali pa mafulashi khadi.
● Ikani mau m’magulu amasilabe 2, 3 ndi 4.
● Ombani m’manja kupeza nambala ya masilabe.
II. Aphunzi:
● Achule mau ali ndi masilabe awili (2), atatu (3) ndi anai (4).
● Aswenzetse mafulashi khadi omwe ali ndi masilabe 2, 3, 4.
● Awelenge mau ali pa mafulashi khadi.
● Aike mau m’magulu amasilabe amau ali ndi masilabe 2, 3 ndi 4.
● Aombe m’manja kupeza nambala ya masilabe.
Zocita:
1. lembani mau ali ndi masilabe atatu (3) mwa awa;
mphako, nthongololo, nthakula, mnyamata, mnyumba, nthungulu
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe asankhidwa moyenela.
Nchito D : Kusintha lembo
I. Mphunzitsi:
● Achule mau monga nthala ndi Ngwila.
● Sonyezani aphunzi kusintha lembo lili koyambila n ndi kuikapo m.
Nthala – mthala
● Uzani aphunzi asinthe mau m’magulu. Athandizeni pomwe apeza bvuto.
II. Aphunzi:
● Achule mau.
● Amvetsele kusintha lembo lili koyambila.
110
● Asinthe lembo loyamba ku liu m’[Link] pomwe apeza bvuto.
Zocita:
Pezani mau asanu (5) ndi kusintha lembo kupanga mau atsopano.
1. Mphele sinthani lembo lili kothela e kuikako o.
likhala ____
2. Mphako sinthani o kuikako a liu latsopano ______
Muyeso Woyembekezeleka: Malembo asinthidwa moyenela.
Nchito E: Kulumikidza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca malembo ophatikizana koma omveka mosiyana amakonsonanti
monga ngw, nth ndi mny.
● Lumikidzani ndi mavawelo kupanga masilabe.
Zitsanzo:
Ngw ndi a ipanga silabe ngwa.
Nth ndi a ipanga silabe ntha.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku zitsanzo.
● Apange masilabe.
Zocita:
Lumikidzani malembo ophatikizana koma omveka mosiyana amakonsonanti ndi mavawelo
kupanga masilabe.
a e i o u
ngw, nth, nch
Mayankho: Ngwa ngwe ngwi ngwo ngwu
111
Muyeso Woyembekezeleka: Malembo ophatikizana koma omveka mosiyana amakonsonanti
ndi mavawelo alumikizidwa ndi kupanga masilabe moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kulumikidza makonsonati ndi mavawelo kupanga
masilabe, kuwelenga chati la masilabe, kusankha masilabe, kusintha lembo ndi kulumikidza
malembo ophatikizana koma omveka mosiyana ndi mavawelo.
Mutu Waung’ono 2: Mau
Lambulo: Mutu uyu udzaona pakulumukidza masilabe kupanga mau, kusintha ndi
kucotsa silabe kupanga mau, kuzindikila masilabe ndi kuwelenga masilabe.
Luso lapadela1: Kulumikidza masilabe kupanga mau.
Mau Ofunika Kudziwa: Mphatso, mphusi, mphasa.
Zida Zophunzitsila ndi Kuphunzilila: Zithunzi , Silabiki chati, ma fulashi khadi.
Mfundo Zophunzitsa
● Kulumikidza masilabe.
● Kupanga mau.
Nchito A: Kulumikidza masilabe kupanga mau.
I. Mphunzitsi :
● Onetsani cithunzi ca mphasa.
● Funsani aphunzi achule dzina la mphasa.
● Sonyezani m’mene liu mphasa ingapangidwile kugwilitsa nchito masilabe
mpha mphe mphi mpho mphu
112
sa se si so su
mpha ndi sa ipanga mphasa
● Funsani aphunzi apange mau ena ndi masilabe apatsidwa m’magulu.
II. Aphunzi :
● Apenyetsetse m’mene liu mphasa ingapangidwile kugwilitsa nchito masilabe.
● Apange mau ena ndi masilabe apatsidwa m’magulu.
● Awelenge mau opangidwa monga, mphaso, mphesi, mphusi.
Zocita:
Pangani mau anai (4) ndi masilabe awa;
Mpha mphe mphi mpho mphu
La le li lo lu
Mau
1. Mphala
2. Mphale
3. mphele
4. Mphelo
Muyeso Woyembekezeleka: Masilabe alumikidzidwa kupanga mau moyenela.
Nchito B: Kusintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau.
I. Mphunzitsi:
● Welengani mau monga awa mphala, mphasa ndi mphuno.
● Sonyezani kucotsa silabe ndi kuikapo lina kupanga liu la tsopano.
mphala kucotsa mpha kuipo mphi , liu likhala mphila.
● Acotse silabe lili koyambila mau kupanga mau mosaikapo lina.
Zitsanzo: Ngwengwelele kucotsa Ngwe, liu likhala ngwelele.
Ngwenyama kucotsa Ngwe liu likhala nyama.
113
II. Aphunzi:
● Awelenge mau.
● Apange mau m’magulu kugwilitsa nchito mafulashi khadi.
mphala, mphasa.
● Acotse silabe lili koyambila ndi kuikapo lina kupanga liu latsopano.
● Awelenge mau atsopano.
Zocita:
Aphunzi acotse silabe lili koyambila kwa liu ndi kuikapo lina kupanga liu latsopano.
mpha mphe mphi mpho mphu
mphala - mphila
mphele - ____le
mphaka - ____ka
1. Cotsa silabe kupanga liu lina.
(i) Ngwenyama – nyama
(ii) Ngwengwelele - ____
Mayankho:
1. Mphele – mphale
Mphaka – mphika
2. (ii) Ngwengwelele - ngwelele
Muyeso woyembekezeleka: Masilabe asinthidwa ndi kucotsedwa moyenela.
Nchito C: Kuzindikila masilbe mu mau
I. Mphunzitsi :
114
● Welengani mau pa chati monga mphuno, nthele, nchenche, ngwilo ndi mnyengo.
● Lembani kamzele pa silabe lililonse m’mau.
● Zindikile silabe powelenga coimilila pa silabe lilonse m’mau.
● Citani mpikisano ozindikila masilabe m’mau.
II. Aphunzi:
● Awelenge mau pa chati.
● Alembe kamzele pa silabe lililonse m’mau.
● Azindikile silabe powelenga coimilila pa silabe lilonse m’mau.
● Acite mpikisano ozindikila masilabe m’mau.
Zocita:
Lembani masipelo amau awa.
1. Nthele
2. Mnyamata
3. Ngwilo
Muyeso woyembekezeleka: Masilabe m’mau azindikilidwa moyenela.
Nchito D : Kuwelenga masilabe m’mau.
I. Mphunzitsi:
● Wonetsani chati ili ndi mau.
● Uzani awelenge [Link] coimilila pa silabe lili lonse.
● Aombe m’manja kuzindikila silabe.
● Uzani aphunzi achule nambala ya masilabe.
II. Aphunzi:
● Apenye mau ali pa chati.
115
● Awelenge [Link] pa silabe lililonse.
● Aombe m’manja kuzindikila silabe.
● Achule nambala ya masilabe.
Zocita:
Pezani nambala ya masilabe m’mau awa.
1. Nthambi
2. Mphemvu
3. Ngwengwelele
Mayankho: 1. Masilabe 2, 2. Masilabe 2, 3. Masilabe 3
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga masilabe kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pakulumukidza masilabe kupanga mau, kusintha ndi
kucotsa silabe kupanga mau, kuzindikila masilabe ndi kuwelenga masilabe.
Luso Lapadela 2: Kuwelenga mau mokweza kulondola kachulidwe ka mau koyenela.
I. Mphunzitsi:
● Ikani chati yomwe ili ndi zithunzi za zinthu monga mphasa, nthambo, nchenche,
ndalama ya ngwee ndi mnyamata.
● Uzani aphunzi achule maina a zinthuzi.
● Awelenge maina a zinthu kugwilitsa nchito mafulashi khadi ndi chati mokweza mau.
II. Aphunzi:
● Achule maina a zinthuzi.
● Awelenge maina.
● Awelenge mau ena awili awili mokweza mau.
116
Zocita:
Aphunzi awelenge mau m’magulu kugwilitsa nchito mafulashi khadi.
Muyeso Woyembekezeleka: Mau awelengedwa moyenela.
Nchito C : Kuwelenga ndi kumvetsetsa ziganizo.
I. Mphunzitsi:
● Wonetsani chati lili ndi mau awa.
Mphika, moto, mnyamata, galu, mphasa, pa, mnyanja, walowa, wakhala, pa, uli.
● Pelekani citsanzo ca ciganizo potenga mau kucokela pa chati ndi kupanga ciganizo.
Citsanzo:
Mphika uli pa moto.
● Welengani ziganizo zina zocokela ku mau ali pa chati .
● Afunseni afotokoze zomwe amvapo pa ziganizo.
II. Aphunzi:
● Awelenge mau ali pa chati.
● Londolani citsanzo.
● Awelenge ziganizo.
● Afotokoze zomwe amvapo pa ziganizo.
Zocita:
Awelenge ziganizo m’magulu.
Muyeso Woyembekezeleka: Ziganizo zawelengedwa ndi mafunso ayankhidwa moyenela.
Nchito D : Kuwelenga ndi kumvetsa zolembedwa mziganizo.
I. Mphunzitsi:
117
● Ikani mafulashi khadi ali ndi mau osiyana siyana kutsogolo.
● Welengani mau ali pa mafulashi khadi.
● Patsani aphunzi zolembedwa mziganizo m’magulu.
Atate anyamula mphale, mwana ndi cigubu pa njinga.
Amalume ao a Ngwenya ali kupsela nthongololo.
● Welengani kulondola zopumila ndi kusonyeza mawelengedwe oyenela.
● Funsani aphunzi afotokoze mawelengedwe [Link] mafunso ena.
● Uzani aphunzi awelenge onse pamodzi, m’magulu ndi awili awili, komanso m’modzi
m’modzi.
II. Mphunzi :
● Apenye mau pa mafulashi khadi .
● Apenye zolembedwa mziganizo m’magulu.
Atate anyamula mphale, mwana ndi cigubu pa njinga.
Amalume ao a Ngwenya ali kupsela nthongololo.
● Atsatile kuwelenga polata ndi cala.
● Afotokoze mawelengedwe amphunzitsi. Ayankhe mafunso yoonetsa kuti amvetsetsa
zowelengedwa.
● Awelenge onse pamodzi, m’magulu ndi awili awili, komanso m’modzi m’modzi.
Zocita:
Tsilizani ziganizo ndi mau awa.
njinga nchenche mphale
1. Atate ananyamula mphale, ____ ndi cigubu pa ____.
2. Jambula cithunzi ca [Link] ciganizo pa cithunzi.
________ ibweletsa matenda.
118
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga zolembedwa mziganizo zitatu zawelengedwa
moyenela.
Nchito E: Kuzindikila zolembedwa zili ndi mvekelo zosiyana siyana ndi zolumikidza.
I. Mphunzitsi:
● Sewenzetsani mafulashi khadi ali ndi mvekelo /n/, /t/ ndi /h/.
● Zindikilani mvekelo imodzi-imodzi.
● Chulani mau ali ndi mvekelo /nth/.
● Uzani aphunzi achule mvekelo zonse pamodzi /nth/.
● Auzeni achule mau ali ndi mvekelo zophatikiza /nth/.
● Welengani mau, muimilile mkafika pa mvekelo zophatikizidwa.
II. Aphunzi:
● Penyani mvekelo zili pa mafulashi khadi /n/, /t/ ndi /h/.
● Azindikile mvekelo imodzi-imodzi.
● Achule mau ali ndi mvekelo /nth/.
● Achule mvekelo zonse pamodzi /nth/.
● Achule mau ali ndi mvekelo zophatikiza /nth/.
● Awelenge mau, aimilile akafika pa mvekelo zophatikizidwa.
Zocita:
Sankhani mau ali ndi mvekelo zophatikizidwa.
1. Mphila
2. Mnyamule
3. Nthele
Muyeso Woyembekezeleka: Kulumikiza makonsonanti ndi mavawelo kupanga mau, ndi
kuwelenga mau kwacitidwa moyenela
119
Cidule: Mutuyu unali kuona pa kuwelenga masilabe, kuwelenga mau mokweza ndi
kuwelenga nkhani kulondola mawelengedwe woyenela.
MATANTHAUZO A MAU
Mutu 4: Maina
Mutu Waung’ono 1 : Maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa.
Ciyambi: Mutu uyu unali kuona pakupanga, kulinganiza, kusewela masewela a
maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
Luso lapadela: Kupanga maina oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
Mau ofunika kudziwa: Dzina, maina, ambiri, oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Zithunzi, mafulashi khadi, machati
Mfundo Zophunzitsa
● Kupanga maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
● Kulinganiza dzina ndi maina.
● Kusewela masewela woculukitsa ndi kucepetsa maina.
Nchito A: Kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
Zindikilani kuti poculukutsa maina, munga gwilitse nchito mvekelo kapena silabe monga a, ma,
mi, zi ndi ena.
I. Mphunzitsi:
● Gwilitsani nchito zinthu kapena zithunzi za zinthu zili ndi mvekelo izi;
/mph/, /nth/, / mny/, / ngw/, /nch/
120
● chulani maina a zinthu.
Mphika nthoci mnyamata mphonda ngwilo ngwee
● Sonyezani kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
Citsanzo:
Mphika – miphika
Nyumba – manyumba
● Auzeni aphunzi apange maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
II. Aphunzi :
● Achule maina a zinthu zili pa cithunzi zili ndi mvekelo izi ;
/mph/, /nth/, / mny/, / ngw/, /nch/
Mphika nthoci mnyamata mphonda ngwee
● Sonyezani kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
Citsanzo:
Mphika – miphika
Nyumba – manyumba
● Apange maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
Zocita:
Pangani maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
1. Mtsikana – atsikana
2. Mnyamata - anyamata
3. Mtengo – mitengo
Muyeso Woyembekezeleka: Maina oculukitsidwa apangidwa moyenela.
Nchito B: Kupanga maina osaculuka kucokela ku maina oculuka.
I. Mphunzitsi:
● Gwilitsani nchito mtsikana, mnyamata ndi mtengo kuphunzitsa phunzilo ili.
121
● Pelekani citsanzo cosonyeza kupanga maina osaculukitsidwa kucokela ku maina
oculukitsidwa.
Citsanzo:
1. Atsikana – mtsikana
2. Anyamata – mnyamata
3. Mitengo – mtengo
● Uzani aphunzi apange maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa
m’magulu. Thandizani aphunzi.
II. Aphunzi :
● Achule maina; mtsikana, mnyamata, mtengo.
● Aphunzi achule maina oculukitsidwa.
● Apange maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
Zocita:
Pangani maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
1. Magalimoto - ______
2. Masukulu - ________
3. Makapu - ________
Muyeso Woyembekezeleka: Maina osaculukitsidwa apangidwa moyenela.
Nchito C : Kulinganiza maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
I. Mphunzitsi:
● Sonyezani zithunzi za zinthu zoculukitsidwa ndi zoculukitsidwa.
● Uzani aphunzi achule maina.
122
miphika, anyamata, mabuku.
● Sonyezani kulinganiza cinthunzi cimodzi ndi zambili.
● Uzani aphunzi atenge cithunzi ca nyumba ca fulashi khadi ndikupita kukaika pa cithunzi ca
manyumba. Alinganize tele zinthu zonse.
II. Aphunzi :
● Aone zithunzi zoculukitsidwa ndi zosaculukitsidwa.
● Achule maina.
● Atsatile kulinganiza kwa cithunzi cimodzi ndi zambili kwa Mphunzitsi.
● Alinganize cithunzi cimodzi ndi zambili.
● Atenge cithunzi ca nyumba ca fulashi khadi ndikupita kukaika pa cithunzi ca manyumba.
Alinganize tele zinthu zonse.
Zocita:
Linganizani maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa.
1. Munthu - anthu
2. Mwana - midzi
3. Mlendo - acona
4. Cona - ana
5. Mudzi - alendo
Muyeso Woyembekezeleka: Maina osaculukitsidwa alinganizidwa ndi maina oculukitsidwa
moyenela.
Nchito D : Kusewela masewela a maina osaculukitsidwa kapena oculukitsidwa.
I. Mphunzitsi :
● Gawilani aphunzi mafulashi khadi ali ndi maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa osiyana
siyana.
123
● Welengani maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa .
● Sewela masewela a maina osaculukitsidwa kapena oculukitsidwa. Mukachula liu la dzina
losaculukitsidwa , gulu limodzi lipeleke yankho la dzina loculukitsidwa. Mupeleke
mamalikisi pa yankho lilonse [Link] limene lidzatenga mamalikisi yambili, lapamba
masewela.
II. Aphunzi:
● Apenye mau ali pa mafulashi khadi osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa.
● Awelenge maina osaculukitsidwa ndi oculukitsidwa.
● Asewele masewela m’magulu.
Muyeso Woyembekezeleka: Kusewela masewela a maina osaculukitsidwa kapena
osaculukitsidwa kwacitika moyenela.
Cidule: Mutu uyu unali kuona pakupanga, kulinganiza, kusewela masewela a maina
oculukitsidwa ndi osaculukitsidwa.
MVETSELO
Mutu 1: Mvetselo
Mutu Waung’ono 1: Mfundo Yaikulu.
Lambulo: Mutuyu udzaona pa mfundo yaikulu, kupfupikitsa nkhani, kuzindikila
lingalilo ndi coona ca nkhani.
Luso lapadela: Kuzindikila ndi kufotokoza mfundo yaikulu pa uthenga omwe amva.
Zida Zophunzilila ndi Kuphunzilila: Mabuku owelenga, mafulashi khadi.
Mau ofunika kudziwa: Nkhani, zoona, uthenga, maganizo.
124
Mfundo Zophunzitsa
● Kuzindikila mfundo yaikulu.
● kufotokoza mfundo yaikulu.
Nchito A: Kuzindikila ndi kufotokoza mfundo yaikulu pa uthenga omwe amva.
I. Mphunzitsi :
● Fotokozan nkhani yaipfupi.
Chalesi ndi mwana omvela. Amatsatila zolankhula wamkulu. Cifukwa ca ici, amalume ake
anamgulila njinga. Amakwela popita kusukulu ndi ku chalichi.
● Funsani mafunso osiyana siyana monga , anali mwana womvela ndani?
● Uzani aphunzi afotokoze zomwe amva pa nkhani.
● Funsani aphunzi afotokoze mfundo yaikulu pa nkhani.
II. Aphunzi :
● Amvetsele ku nkhani yaipfupi.
● Afotokoze zomwe amva pa nkhani.
● Ayankhe mafunso osiyana siyana monga, anali mwana womvela ndi Chalesi.
● Afotokoze mfundo yaikulu pa nkhani.
Zocita:
Tsilizani ziganizo izi.
1. _______ anali mwana womvela.
2. Anamgulila njinga a ______ ake.
3. Amakwele njinga popita ku ____ ndi ku chalichi.
Muyeso woyembekezeleka: Mfundo yaikulu yazindikilidwa ndi kufotokozedwa moyenela.
125
Nchito B: Kupfupikitsa uthenga.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani cithunzi ca mnyamata ali ndi njinga.
● Funsani aphunzi zimene aona pa cithunzi.
● Welengani nkhani iyi.
Chalesi ndi mwana omvela. Amatsatila zolankhula wamkulu. Cifukwa ca ici,
amalume ake anamgulila njinga. Amakwela popita kusukulu ndi ku chalichi.
● Uzani aphunzi awelenge.
● Fotokozani mfundo yaikulu.
II. Aphunzi :
● Apenye pa cithunzi ca mnyamata ali ndi njinga.
● Akambe zimene aona pa cithunzi.
● Amvetsele ku khani.
● Awelenge nkhani.
● Azindikile mfundo yaikulu.
Muyeso Woyembekezeleka: Uthenga wapfupikitsidwa moyenela.
Mutu Waung’ono 2 : Coona ndi Lingalilo
Luso Lapadela : Kusiyanitsa coona ndi lingalilo
Nchito A: Kuzindikila lingalilo la nkhani
I. Mphunzitsi :
● Onetsani zinthu monga buku, cola, delesi ndi nsapato.
● Mufotokoze kuti delesi ili ndi la maonekedwe abwino kwambili dziko lonse.
126
● Fotokozani kuti ao ndi lingalilo cabe cifukwa kuli madelesi ena opambana
maonekedwe a delesi ilo.
Mucite tele ndi buku, cola ndi nsapato.
● Welengani nkhani.
● Funsani aphunzi kuti apeze mau oonetsa malingalilo cabe.
II. Aphunzi :
● Aone zinthu monga buku, cola, delesi ndi nsapato.
● Amvetsele kuzofotokoza za maonekedwe a delesi.
● Amvetsele ku zofokoza kuti ndi lingalilo cabe limene mphunzitsi wanena,
cifukwa kuli madelesi ena opambana maonekedwe a delesi ilo.
● Awelenge nkhani.
● Apeze mau kapena ziganizo zoonetsa malingalilo cabe.
Zocita:
M’magulu, awelenge nkhani ndi kupeza mau kapena ziganizo zoonetsa
malingalilo cabe.
Muyeso Woyembekezeleka: Lingalilo mu nkhani lazindikilidwa moyenela.
Nchito B: Kuzindikila coona mu nkhani
I. Mphunzitsi :
● Uzani aphunzi awelenge ziganizo zili pa chati.
1. Galu ali ndi miyendo anai (4).
2. Nyumba ili ndi khomo.
● Mufotokoze kuti izi ndi zoona ndipo ndi zooneka ndi maso.
● Uzani aphunzi akambe zoona zina.
● Welengani nkhani mu buku lowelenga.
127
● Funsani aphunzi kuti apeze zonena zoona.
II. Aphunzi :
● Awelenge ziganizo zili pa chati.
Galu ali ndi miyendo anai (4).
Nyumba ili ndi khomo.
● Amvetsele kufotokoza kwa mphunzitsi kuti ziganizo zifotokoza zoona.
● Akambe zoona zina.
● Awelenge nkhani mu buku lowelenga.
● Apeze zonena zoona zili mu nkhani.
Zocita:
Aphunzi awelenge nkhani ndi kupeza ziganizo zonena zoona mu nkhani zwili (2).
Mwacidule: Mutuyu unali kuona pa mfundo yaikulu, kupfupikitsa nkhani, kuzindikila
lingalilo ndi coona ca nkhani.
Mutu 2 :Mvetso
Mutu Waung’ono : Coona Ca Nkhani
Ciyambi: Mutuyu udzaona pa coona ca nkhani., kufotokoza zomwe zawelengedwa,
kuyankha mafunso ndi kufotokoza mwatsatane tsatane zomwe zinacitika mu nkhani.
Luso lapadela : Kupeleka uthenga wapapfupi omwe wafotokozedwa mu nkhani . (mu
ziganizo ziwili (2) kapena zitatu (3)).
Zida Zophunzitsila ndi Kuphunzilila: Chati, mafulashi khadi.
128
Mau Ofunika kudziwa: Nkhani, kolela, zinyalala, nkhando, zapapfupi.
Mfundo yophunzitsa
● Kufotokoza zomwe zawelengedwa.
Nchito A: Kufotokoza zomwe zawelengedwa.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani cithunzi ca nchenche.
● Uzani aphunzi afotokoze zimene aona.
● Welengani nkhani.
Nchenche ikonda kukhala pa malo aubve monga a zinyalala. Anthu afunika kutentha
zinyalala, kutaya mu bini ndi mu nkhando. Ici cithandiza kupewa matenda monga a
kolela.
● Funsani mafunso pa nkhani yawelengedwa.
● Auzeni aphunzi afotokoze zomwe zawelengedwa.
II. Aphunzi:
● Apenye zili pa cithunzi.
● Afotokoze zimene aona.
● Amvetsele ku nkhani.
● Ayankhe mafunso pa nkhani yawelengedwa.
● Afotokoze zomwe zawelengedwa.
Zocita:
Jambula cithunzi ca nchenche ndi kulemba ziganizo ziwili za papfupi.
Muyeso woyembekezeleka: Uthenga wowelengedwa wafotokozedwa moyenela.
129
Nchito B: Kuyankha mafunso pa zomwe zawelengedwa.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani.
Nchenche ikonda kukhala pa malo aubve monga a zinyalala. Anthu afunika kutentha
zinyalala, kutaya mu bini ndi mu nkhando. Ici cithandiza kupewa matenda monga a
kolela.
● Funsani mafunso monga mwamvapo ciani pa nkhani? Ndi ciani cikonda kukhala pa malo
aubve? Nanga matenda a kolela angapewedwe bwanji?
● Awelenge nkhani mu buku lowelenga la mphuzi.
II. Aphunzi:
● Awelenge nkhani.
● Ayankhe mafunso yofunsidwa ndi mphunzitsi.
● Awelenge nkhani mu buku lowelenga la mphuzi.
Zocita:
Yankhani mafunso
1. Kodi nchenche ikonda kukhala pa malo otani?
2. Chula malo komwe zinyalala zifunika kutidwa.
3. Ndi matenda otani angapewedwe?
Muyeso oyembekezeleka: Mafunso ayankhidwa moyenela.
Nchito C : Kufotokoza mwatsatane tsatane momwe zinacitikila mu nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani.
130
Kuphika zitumbuwa ndi cinthu cosabvuta. Zofunika kuti muphike zitumbuwa ndi
ufa wa fulaulo, mafuta ophikila, shuga, mcele ndi isiti. Mungagule izi ku sitolo.
● Funsani aphunzi mafunso.
● Auzeni afotokoze mwatsatane tsatane zinthu zomwe zifunika kuphika
zitumbuwa.
● Uzani aphunzi amvetsele ku nkhani yowelengedwa.
Kupanga galimoto loseweletsa ndi cinthu cosabvuta. Zofunika kuti
mupange galimoto ili ndi botolo la pulasitiki monga momwe munali
maheu, tubwinikililo ndi waya waung’ono.
● Funsani aphunzi mafunso osiyana siyana.
● Auzeni afotokoze mwatsatane tsatane zinthu zomwe zifunika kupanga
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku nkhani yowelengedwa.
● Ayankhe mafunso.
● Afotokoze mwatsatane tsatane zinthu zomwe zifunika kupanga galimoto
loseweletsa.
Zocita:
Yankhani mafunso awa.
[Link] galimoto.
2. Lemba zinthu zomwe zifunika kupanga galimoto la mawaya.
Muyeso Woyembekezeleka: Zocitika mu nkhani zafotokozedwa mwatsatane tsatane.
Cidule: Mutuyu unali kuona pa zoona zili mu nkhani, kufotokoza zomwe
zawelengedwa, kuyankha mafunso ndi kufotokoza mwatsatane tsatane zomwe zinacitika mu
nkhani.
131
KULEMBA
Mutu 1: Malembedwe
Mutu Waung’ono 1: Kulemba Malembo
Ciyambi: Mutuyu udzaona pakujambula ndi kulemba malembo. Kulemba mau ndi
ziganizo mu malembo okhazikika. Kulemba ziganizo mosiya mpata pakati pa mau.
Luso lapadela: Kulemba malembo
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Chati la malembo, chati la mau, chati la ziganizo,
mafulashi khadi.
Mau Ofunika Kudziwa: Kulemba, malembo, aliphabeti, kumwamba, pansi.
Mfundo yophunzitsa
● Malembedwe a malembo akuluakulu.
Nchito A : Kujambula malembo.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani chati la malembedwe oyenela a malembo akuluakulu.
● Lembani pa bolodi.
● Uzani aphunzi alembe lembo limodzi limodzi kulondola m’mene mulembela.
Zindikilani kuthandiza aphunzi ali ndi bvuto pa malembedwe oyenela.
II. Aphunzi:
● Apenyetsetse malembo ali pa chati.
● Apenyetsetse malembedwe ya mphunzitsi pa bolodi.
● Alembe lembo limodzi limodzi kulondola m’mene Mphunzints alembela.
Zocita:
132
[Link] malembo akulu akulu.
ABCDEFGHIJKLMNOPQRSTUVWXYZ
Muyeso woyembekezeleka: Malembo ajambulidwa ndi kulembedwa moyenela.
Nchito B : Kulemba malembo
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi aimbe nyimbo ya mavawelo iliyonse.
● Pelekani citsanzo colemba malembo ang’ono ang’ono ya [Link] apenyelele
ndi kulemba malembedwe oyenela a malembo.
a b c d e f g h I j k l m n o p q r s t u v w.
Penyelelani m’mene alembela [Link].
● Lembani malembo ali ndi micila yopita [Link] malembedwe ake ndipo
aphunzi amalembedwe.
gjpqy
● Lembani malembo yali ndi micila yopita [Link] alembe.
Khblt
ZINDIKILANI : kuti muyenela kupenyelela ndi kuthandiza aphunzi kulemba malembo
[Link] ayenela kukhazikika pa mzele.
II. Aphunzi:
● Aimbe nyimbo ya mavawelo iliyonse.
● Apenyelele citsanzo colemba malembo ang’ono ang’ono ya aliphabeti ya apa kesi ( lower
case).
● Alembe malembo moyenela.
a b c d e f g h I j k l m n o p q r s t u v w.
Penyelelani m’mene alembela [Link].
● Apenyelele malembedwe a malembo ali ndi micila yopita pansi ndipo alembe.
gjpqy
● Apenyelele malembewe a malembo ali ndi micila yopita kumwamba ndipo alembe.
133
Khblt
Zindikilani kuti muyenela kupenyelela ndi kuthandiza aphunzi kulemba malembo
[Link] ayenela kukhazikika pa mzele.
Zocita:
1. Lembani malembo ali ndi micila yopita pansi.
2. Lembani malembo ali ndi micila yopita kumwamba.
Mayankho:
1. g j p q y
2. k h b l t
Muyeso Woyembekezeleka: Malembo alembedwa moyenela.
Mutu Waung’ono 2: Malembedwe okhazikika
Nchito : Kulemba mau yooneka ndi yowelengeka mosabvuta m’malembedwe
okhazikika.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani chati yomwe ili ndi mau olembedwa mobvuta kuwelenga.
● Onetsani cati lili ndi mau olembedwa moyenela.
● Funsani aphunzi zamalembedwe amenewa.
● Fotokozani malembedwe oyenela, amalembo otayana ndi okhazikika.
● Uzani aphunzi alembe ndipo muyang’anile malembedwe ao.
● Lembani ciganizo molongosoka.
● Uzani aphunzi naonso alembe mau ndi ciganizo molongosoka.
II. Aphunzi:
134
● Apenye pa chati ili ndi mau olembedwa mobvuta kuwelenga.
● Afotokoze zamalembedwe awa.
● Apenye pa cati ili ndi mau olembedwa moyenela.
● Afotokoze zamalembedwe amenewa.
● Amvetsele ndi kupenyetsetsa malembedwe oyenela amalembo otayana a okhazikika.
● Alembe ndipo mphunzitsi ayang’anile malembedwe ao.
Zocita:
Lembani mau awa moyenela. Malembo muyalembe motayana.
1. Balalika
2. Chadiza
3. Gulugufe
4. Nyani
5. Phulantenga
Muyeso Woyembekezeleka: Mau alembedwa mokhazikika moyenela.
Mutu Waung’ono 3: Mipata ya mau
Nchito D : Kulemba mau mosiya mpata.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani chati lili ndi malembedwe osasiya mpata.
Citsanzo:
Ganizaniwapitakukaonaagogo.
● Welengani ciganizo.
● Uzani aphunzi awelenge.
● Funsani zolakwika.
● Fotokozani malembedwe oyenela osiya mpata pakati pa mau.
135
● Lembani ciganizo moyenela.
● Patsani ziganizo zolembedwa mosasiya mpata pakati pa mau ku aphunzi m’magulu.
● Auzeni alembe molongosoka.
II. Aphunzi:
● Onetsani chati lili ndi malembedwe osasiya mpata.
● Welengani ciganizo.
● Uzani aphunzi awelenge.
● Funsani zolakwika.
● Fotokozani malembedwe oyenela osiya mpata pakati pa mau.
● Lembani ciganizo moyenela.
● Patsani ziganizo zolembedwa mosasiya mpata pakati pa mau ku aphunzi m’magulu.
● Auzeni alembe molongosoka.
Zocita:
Lembani ziganizo ndi kusiya mipata.
1. Mphunzitsiwalowamkalasi.
2. Amalumeakwelanjinga.
Muyeso Woyembekezeleka: Ziganizo zalembedwa ndi mipata yasiyidwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pakujambula ndi kulemba [Link] mau
ndi ziganizo mokhazikika. Kulemba ziganizo mosiya mpata pakati pa mau.
KULEMBA
Mutu 1: Cimangilizo
Mutu Waung’ono 1: Kujambula
Ciyambi: Mutuyu udzaona pakufotokoza maganizo kupyolela mu kujambula.
136
Luso lapadela: Kufotokoza maganizo kupyolela mu kujambula.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: ZIthunzi.
Mau Ofunika Kudziwa: Nkhani, kujambula, kufotokoza.
Mfundo yophunzitsa
● Kujambula zithunzi.
Nchito A : Kujambula zocitika kupanga nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Kambani nkhani yaipfupi.
● Funsani aphunzi akambe nkhani ziwili zazipfupi.
● Fotokozani kuti nkhani zingakambidwe kugwilitsa nchito zithunzi.
● Onetsani zithunzi zinai (4) za nkhani.
● Welengani nkhani ndipo aphunzi aike zithunzi mundondomeko yolondola tsatane-
tsatane wa nkhani.
● Aphunzi jambule zithunzi kutsatila nkhani.
II. Aphunzi :
● Amvetsele ku nkhani yaipfupi.
● Akambe nkhani ziwili zazipfupi.
● Amvetsele kufotokoza kwa Mphunzitsi pa kalembedwe ka nkhani kugwilitsa nchito
zithunzi.
● Apenye zithunzi zinai (4) za nkhani.
● Awelenge nkhani ndipo aphunzi aike zithunzi mundondomeko yolondola tsatane-tsatane
wa nkhani.
● Ajambule zithunzi kutsatila nkhani.
137
Zocita:
Pangani nkhani pakujambula zithunzi.
Muyeso Woyembekezeleka: Kujambula kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutuyu unali kuona pakufotokoza maganizo kupyolela mu kujambula.
138
CAPAMUTU 5 KUMVETSELA NDI KULANKHULA
Mutu: Zilapi ndi mau opinda lilime (Tongue Twisters)
Mutu waung’ono: Mau opinda lilime (Tongue twisters)
Ciyambi: Mutu waung’ono uyu udzaona pa mau opinda lilime, malankhulidwe ake ndi
zolinga zosiyana-siyana za mau opinda lilime.
Luso lapadela: Kuloweza mau opinda lilime
Mau ofunika kudziwa: Zilapi, kupinda, lilime, kuloweza, kuceza, kufulumila,
tanthauzo, kulondola, kuthandiza, luso, zosangalatsa.
Zida zophunzitsila ndi zophunzilila: Mabuku a aphunzi, mabuku a zilapi ndi a mau opinda
lilime .
Mfundo Yophunzitsa:
● Kuphunzitsa aphunzi mau opinda lilime ndi malowezedwe ake.
Nchito : Kuloweza Ndi Kubwezela Kunena Mau Opindika Lilime .
I . Mphunzitsi:
● Lankhulani ciganizo ca mau opinda lilime modekha kwa aphunzi ndipo
muwafunse zomwe amvapo.
● Bwezani kunena ciganizoco mofulumila ndi Kufunsanso aphunzi zomwe
amvapo.
● Fotokozani tanthauzo la mau opinda lilime kwa aphunzi
139
1. Mau opinda lilime ndi ziganizo zopangidwa kukhala zobvuta kalankhula
mofulumila ndi molondola mau cifukwa ca kufanana kwa mamvekedwe a mau
m’ziganizozo.
2. Mau opinda lilime amagwilitsidwa nchito kukhala masewela a mau, kuphunzila
kulankhula, kuceza ndi zosangalatsa.
3. Yamathandiza kupititsa patsogolo maluso a kachulidwe ka mau, kuwelenga
mofulumila ndi kulankhula zofunika kulemba.
4. Lankhulani ciganizo ca mau opinda lilime cimodzi mofulumila ndi kuuza aphunzi
kuti acilankhulenso mofulumila.
Citsanzo:
Mnkhwele wamankhwala wagwa mphwai ndi kutaya mnkhwani pomva mtswatswa wa nkhwali
mnkhalango.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ndi kukambilana momwe aphunzitsi alankhulila mau opinda lilime.
● Ayamikile zolankhula aphunzitsi.
● Ayetselele Kulankhula mau opindika lilime.
● Alankhule mau opinda lilime osiyana-siyana m’magulu.
Zocita:
Kambilanani mau opindika lilime osiyana-siyana m’magulu anu.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuloweza ndi kubweleza kunena mau opinda lilime kwacitika
moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa mau opinda lilime, malankhulidwe ake ndi zolinga
zosiyana-siyana za mau opinda lilime.
140
KUWELENGA
Mutu: Kuzindikila Masilabe
Mutu waung’ono : Kuzindikila Masilbe opangidwa ndi malemba awa; mts--, mdz-, mkw-,
phw- , thy- , m’mau okambidwa.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
Mtsa mtse mtsi mtso mtsu.
Ciyambi: Mutu uyu udzaona pakupanga Masilabe kucokela ku mau okambidwa
,kusewela masewela akuwelenga Masilabe omwe ali mu mau pakuomba m’manja ndi masewela
akupanga mau ena pakusintha ndi kucotsa Masilabe kupanga mau atsopano.
Luso Lapadela: Kuzindikila Masilabe m’mau olankhulidwa.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: fulashi khadi, chati ya Masilabe.
Mau Ofunikila Kudziwa: Masilabe, vawelo, Mfundo zophunzitsa .
Mfundo zophunzitsa:
● Kuzindikila Masilabe m’mau okambidwa
● Kutsewela masewela owelenga nambala ya Masilabe mliu
Nchito A: Kuzindikila Masilabe m’mau okambidwa (mts, mdz, phw, mkw, thy)
I. Mphunzitsi:
● Nenani mau
141
● Funsani aphunzi Masilabe omwe apezeka mu mau okambidwa.
● Sonyezani Masilabe omwe apezeka m’mau okambidwa
Citsanzo:
1. Mtsikana ---- mtsi / ka /na ( Masilabe atatu )
II. Aphunzi :
● Amvetsele ku mau okambidwa
● Apeze Masilabe m’mau okambidwa m’magulu ao
● Azindikile Masilabe m’mau okambidwa m’magulu awili-awili.
Zocita:
Pezani Masilabe m’mau awa okambidwa.
1. Mtsuko
2. Mtsasa
Muyeso Woyembekezeleka: Kuzindikila Masilabe mu Mau okambidwa kwacitika moyenela
Nchito B: Kusewela masewela owelenga nambala ya Masilabe mliu (mts, mdz,
mkw, phw, thy )
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi:
● Nenani mau
● Citani ndi kusonyeza mocitila masewela osiyana-siyana akupanga
Masilabe.
142
Citsanzo:
Kumtsekela = ku --ombani m’manja, mtse --ombani m’manja, ka --ombaninso m’manja-
pamodzi aphunzi azaomba katatu
● Udzani aphunzi kuti aombe m’manja akazindikila silabe mliu
1. Mdzandipeza = /mdza/, /ndi/ , /pe/, /za/= kuomba m’manja kanai.
2. Mdzukulu = /mdzu/,/ku/,/lu/. = kuomba m’manja katatu
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku mau
● Acite masewela osiyana-siyana akupanga ndi Kudzindikila Masilabe pakuomba
m’manja.
● Aombe m’manja akamva silabe ndi kuwelenga nambala ya Masilabe mliu.
● Acite masewela awa m’magulu awili- awili.
Zocita:
Lembani nambala ya Masilabe mliu.
1. Mdzathu
2. Ndimdziwa
Muyeso Woyembekezeleka: Kusewela masewela akuwelenga masilabe mliu pakuomba
m’manja kwacitika moyenela
Nchito C: Kupanga mau okambidwa kugwilitsa nchito Masilabe—( mts , mdz,
mkw, thy phw)
143
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi:
● Pelekani zitsanzo zolumikidza Masilabe ndi kupanga mau okambidwa.
Citsanzo:
1. Thyo / ka/ ipanga thyoka
2. Mkwe / kwe / sa/ apanga mkwekwesa
II. Aphunzi:
● Aonelele zitsanzo zopelekedwa ndi Mphunzitsi.
● Alumikize Masilabe kupanga mau okambidwa.
Zocita:
Lumikizani Masilabe awa kupanga mau okambidwa.
1. /Thyo/, /ke /,/la/ apanga -----------
2. /Ci/, / thye/, /thye/ apanga------------
Muyeso Woyembekezeleka: Kupanga mau olankhulidwa kugwilitsa nchito masilabe kwacitika
moyenela
Nchito D: Kusewela Masewela A Kucotsa Silabe Ku Liu Ndi Kuikako Ina Kupanga
Mau Atsopano ---mts , mdz, mkw, thy phw.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
144
I. Mphunzitsi :
● Nenani mau
● Onetselani kucotsa silabe ndi kuikako Ina kupanga mau atsopano.
Zitsanzo:
1. Kanya = phwanya = cotsani /ka/ ikani / phwa/
2. Switi = phwiti = cotsani /swi/ ikani /phwi/ .
II. Aphunzi :
● Amvetsele mau kucokela kwa mphunzitsi .
● Ayeselele kupanga mau atsopano pakucotsa silabe ndi kuikako Ina.
Zocita:
Pangani mau ena atsopano pakucotsa silabe ndi kuikako Ina.
1. Ngwee = phwee = cotsani /Ngwe/ ikani /phwe/.
2. Waphwanya = ndaphwanya = cotsani /wa/ ikani /nda/.
Muyeso Woyembekezeleka: Kucita masewela a kucotsa silabe ku Liu ndi kuikako Ina kupanga
mau atsopano kwacitidwa moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pakupanga Masilabe kucokela ku mau okambidwa
,kusewela masewela akuwelenga Masilabe omwe ali mu mau pakuomba m’manja ndi masewela
akupanga mau ena pakusintha ndi kucotsa Masilabe kupanga mau atsopano.
Mutu 2 : Ubale wa Lembo ndi Mvekelo.
Mutu waung’ono 1 : Masilabe ---mts , mdz, mkw, thy phw.
145
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
Ciyambi : Mutu uyu udzaona pa Kulumikiza makonsonanti ndi mavawelo kupanga
Masilabe, kuwelenga silabiki chati, kusankha Masilabe kucoka m’mau, kusinthanitsa malembo
kupanga mau ndi Kulumikiza gulu la makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
Mau Ofunika Kudziwa : Masilabe , makonsonanti, mavawelo.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: mafulashi khadi, chati ya Masilabe.
Mfundo Zophunzitsa :
● Kupanga masilabe polumikiza makonsonanti ndi mavawelo.
● Kuwelenga Masilabe opangidwa.
Nchito A: Kupanga Masilabe Pa kulumikiza Makonsonanti Ndi Mavawelo. ---mts ,
mdz, mkw, thy phw.
I. Mphunzitsi:
● Lembani mvekelo la tsiku ndi mavawelo
● Sonyezani kulumikiza mavawelo ku makonsonanti opatsidwa kupanga Masilabe.
Zitsanzo :
a e i o u
/Mkw/ = mkwa mkwe mkwi mkwo mkwu
II. Aphunzi:
● Aone mvekelo la tsiku lolembedwa.
146
● Apange Masilabe polumikidza malembo ndi mavawelo m’magulu ao
polondola citsanzo kucokela kwa mphunzitsi.
Zocita:
Pangani Masilabe pogwilitsa nchito mamvekelo ndi mavawelo opatsidwa .
a e i o u
1. /mts/ =
2. /mkw/ =
Masilabe apangidwa kucokela ku makonsonanti ndi mavawelo moyenela.
Nchito B: Kuwelenga silabiki chati---mts , mdz, mkw, thy phw.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi:
● Onetsani chati ya masilabe kwa aphunzi.
● Sonyezani mawelengedwe a Masilabe pa chati.
● Udzani aphunzi kuti awelenge Masilabe ya pa chati.
Citsanzo
a e i o u
Mts Mtsa Mtse Mtsi Mtso Mtsu
147
I. Aphunzi :
● Aone chati ya Masilabe
● Awelenge Masilabe kucokela pa silabiki chati.
● Acite izi m’magulu ao kapena awili-awili.
Zocita:
Welengani silabiki chati m’magulu
Muyeso Woyembekezeleka : Kuwelenga silabiki chati kwacitidwa moyenela.
Nchito C: Kusankha Kapena Kupeza Masilabe Kucokela Ku Mau. ---mts , mdz,
mkw, thy phw.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi :
● Konzekelani mau pa mafulashi khadi
● Sonyezani aphunzi momwe angathe Kuzindikila Masilabe.
Citsanzo:
1. Mdzikoli = /mdzi/,/ko/, /li /= muli Masilabe atatu
II. Aphunzi :
● Azindikile Masilabe ali mau
● Anene Masilabe amene apezeka m’mau
Zocita:
148
Zindikilani Masilabe omwe ali m’mau awa.
1. Phwanyika
2. Waphwanya
Muyeso Woyembekezeleka : Kusankha Masilabe Kucokela M’mau Kwacitika Moyenela.
Nchito D: Kucotsa Silabe La Mau Ndi Kuikako Ina.(Letter Substitution) ---mts ,
mdz, mkw, thy phw.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amalemba amodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi :
● Nenani mau
● Sonyezani kucotsa lembo ku mau ndi kuikako Lina.
Zitsanzo:
1. Waphwanya = taphwanya = cotsani /w/ ikani /t/
2. Phwiti = switi = cotsani /ph/ ikani /s/
II. Aphunzi :
● Amvetsele ku mau okambidwa ndi mphunzitsi
● Acotse lembo ku mau ndi kuikako Ina kupanga mau atsopano
Zocita:
Cotsani lembo loyambilila ku mau ndi kuikako Ina kupanga mau atsopano.
149
1. Mdzathu
2. Mdzakhala
3. Mdzabwela
Muyeso Woyembekezeleka: Kucotsa lembo ku mau kuikako Ina kupanga mau atsopano
kwacitidwa moyenela
NCHITO E: Kulumikiza Malembo Ophatikizana Amakonsonanti Koma Amamvekedwe
osiyana Ndi Mavawelo Kupanga Masilabe. ---mts , mdz, mkw, thy phw.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi :
● Lembani makonsonanti ophatikizana pa bolodi.
● Sonyezani Kulumikiza makonsonanti ophatikizana ndi mavawelo
kupanga Masilabe.
Citsanzo:
a e i o u
Mkwa mkwe mkwi mkwo mkwu
Phwa phwe phwi phwo phwu
II. Aphunzi :
● Amvesele ndi kuona makonsonanti ophatikizana omwe alembedwa pa bolodi
● Alumikize makonsonanti ophatikizana aja ndi masilabe m’magulu ao.
Zocita:
150
Lumikizani makonsonanti ophatikizana awa ndi mavawelo kuti mupange Masilabe.
a e i o u
1. Mkw
2. Phw
Muyeso Woyembekezeleka : Kulumikiza makonsonanti ophatikizana ndi mavawelo kupanga
Masilabe kwacitika moyenela.
MUTU 2 : Kupanga Mau
Mutu Waung’ono 2: Mau ---mts- , mdz-, mkw-, thy-, phw-.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse masilabe opangidwa ndi malembo ali pamwambapa
imodzi –imodzi mpaka onse atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila masilabe
opangidwa ndi mts- mtsa, mtse, mtsi, mtso, mtsu
Ciyambi: Mutu waung’ono uyu udzaona pa Kulumikiza masilabe kupanga mau,
masewela akusintha ndi kucotsa masilabe kupanga mau, Kuzindikila Masilabe m’mau.
Luso Lapadela: Kulumikiza masilabe kupanga mau.
Mau Ofunikila Kudziwa: Masilabe, mau
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Chati ya Masilabe, fulashi khadi
Mfundo Zophunzitsa:
● Kulumikiza masilabe
● Kusintha ndi kucotsa Masilabe kupanga mau.
151
Nchito A: Kulumikiza Masilabe Kupanga Mau. ---mts , mdz, mkw, thy phw.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi:
● Lembani masilabe
● Sonyezani kulumikiza Masilabe kupanga mau
Zitsanzo:
mtsa/ na apanga mtsana
mtsi, / ka / / na / ipanga mtsikana
II. Aphunzi :
● Apenyelele molumikidzila Masilabe kupanga mau.
● Alumikize Masilabe opatsidwa kupanga mau m’magulu ao.
Zocita: Lumikizani Masilabe awa ndi kupanga mau
1. Mtsa + sa =
2. Mtsi + ka + na =
3. mtsa+ na =
4. Mtso + nyo
Muyeso Woyembekezeleka : Kulumikiza masilabe kupanga mau kwacitika moyenela.
Nchito B: kusintha Masilabe kuikako ena kupanga mau atsopano. . ---mts , mdz,
mkw, thy phw.
152
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi:
● Konzekelani mau pa mafulashi khadi
● Funsani aphunzi kusintha silabe loyamba kapena laciwili kuikapo Ina kupanga
mau atsopano
Zitsanzo:
1. Mtsikana = kukana --- cotsani /mtsi/ ikani /ku/
2. Mdzinja = manja --- cotsani /mdzi/ ikani /ma/
II. Aphunzi :
● Aone zomwe aphunzitsi ao ali kucita
● Naonso m’magulu ao asinthe silabe ndi kuikapo Ina kupanga mau atsopano
Zocita:
Pangani mau atsopano pakucotsa silabe ndi kuikapo Ina.
1. Mdzathu
2. Mdzukulu
3. Thyola
Muyeso Woyembekezeleka : Kusintha masilabe ku mau kuikapo ena kupanga mau atsopano
kwacitika moyenela.
153
Nchito C: Kuzindikila Masilabe Mu Mau. ---mts , mdz, mkw, thy phw.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi:
● Onetsani mau omwe alembedwa pa mafulashi khadi
● Funsani aphunzi kuti aombe m’manja pakuzindikila Masilabe m’mau opatsidwa
Zitsanzo:
1. Mtsuko = /mtsu/ ombani m’manja, /ko/ ombani m’manja . Pamodzi muzaomba m’manja
kawili.
2. Phwando = /phwa/ ombani m’manja, /ndo/ ombani m’manja. Pamodzi muzaomba m’manja
kawili.
II. Aphunzi :
● Awelenge mau opatsidwa.
● Azindikile Masilabe m’mau
● Aombe m’manja kulingana ndi Masilabe ali m’mau.
Zocita:
Zindikilani ndi kulemba Masilabe omwe ali m’mau awa.
1. Phwanyika
2. Phwetekele
3. Thyokela
Muyeso Woyembekezeleka : Kuzindikila Masilabe m’mau kwacitika moyenela.
154
Nchito D: Kuwelenga Masilabe M’mau .
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse Masilabe amvekelo imodzi mpaka onse oonetsedwa
pamwambapa atatha. Munsimu mwaonetsedwa mophunzitsila Masilabe
I. Mphunzitsi:
● Konzekelani mau pa mafulashi khadi
● Funsani aphunzi kuti awelenge Masilabe omwe ali m’mau
Zitsanzo:
[Link] = mdza + bwe + la = Masilabe atatu
2. Ndimdziwa = ndi + mdzi + wa = Masilabe atatu
II. Aphunzi:
● Apenyelele zomwe aphunzitsi Ali kucita
● Awelenge ndi kupeza nambala ya Masilabe omwe ili m’mau m’magulu ao.
Zocita:
Welengani manambala amasilabe omwe apezeka m’mau opatsidwa.
1. Mtsikana
2. Mdzukulu
3. kumtseka
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga nambala ya Masilabe kucokela m’mau opatsidwa
kwacitika moyenela.
155
Mwacidule : Mutu uyu unali kuona pa mvekelo la lembo, kuzindikila ndi kupeza lembo,
kulumikiza lembo ndi vawelo kupanga silabe, kulumikiza Masilabe kupanga mau, komanso
kuwelenga nambala ya Masilabe m’mau.
MUTU 3: KUWELENGA MOFULUMILA
Nchito B: kuwelenga mau
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse mau omwe ali ndi mvekelo mts, mdz,mkw,thy,phw.
Yetsesani kuti aphunzi akwanilitse kuwelenga mau awa popanda bvuto lililonse.
I. Mphunzitsi:
● Nenani mau
● Lembani mau pa chati kapena pabolodi ndi sonyeza kuwelengele aphunzi
polondola mawelengedwe abwino ( model reading)
● Udzani aphunzi kuti awelenge mau.
Zitsanzo:
1. Mtsikana
2. Phwiti
3. Inaphwanyika
II. Aphunzi:
● Awelenge mau mokuwa m’magulu ao
● Awelenge mau ndi machulidwe oyenela awili- awili.
Zocita:
156
Welengani mau awa mokuwa ndiponso mofulumila m’magulu awili–awili
1. Thyola
2. Cithyethye
3. Anamkwiyila
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga Mau kwacitika moyenela.
Nchito C: Kuwelenga Ndi Kumvetsa Ziganizo. ---mts , mdz, mkw, thy phw.
ZINDIKILANI: Mphunzitsi aphunzitse mau omwe ali ndi mvekelo mts, mdz,mkw,thy,phw.
Yetsesani kuti aphunzi akwanilitse kuwelenga mau ndi ziganizo momwe mau amukati akhale ndi
masilabe opangidwa ndi mvekelo zonse zopatsidwa pamwambapa.
I. Mphunzitsi:
● Lembani ziganizo pa bolodi
● Udzani aphunzi kuti awelenge ziganizo
● Funsani aphunzi kuti apeleke matanthauzo a ziganizo.
II. Aphunzi :
● Aone ziganizo zolembedwa pa bolodi.
● Awelenge ziganizo zolembedwa
● Apeleke matanthauzo a ziganizo zolembedwa.
Zocita:
Pelekani matanthauzo a ziganizo izi.
1. Mtsikana Ali kuphika cakudya
2. Onani anyamata Ali kuteya mpiri wa miyendo.
157
3. Anyamata ndi atsikana apita kukathyola nkhuni.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga ndi kupeleka matanthauzo a ziganizo moyenela.
Nchito D: Kuwelenga Kankhani Ka Mizele Iwili Kapena Isanu.
I. Mphunzitsi:
● Lambani nkhani ya cidule yokwanila mizele iwili kapena itatu
● Welengani nkhani pomwe aphunzi akulondola.
● Funsani aphunzi kuti awelenge nkhani imeneyo.
II. Aphunzi :
● Amvetsele kawelengedwe ka nkhani kucokela kuli mphunzitsi.
● Awelenge nkhani onse mkalasi
● Awelenge nkhani awili-awili.
Zocita:
Welengani nkhani iyi awili- awili.
Malita ndi mwana wanzelu kwambili. Acita bwino’ kwambili mu mayeso ake. Lelo malita
watenga nambala wanu mkalasi lao.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga nkhani ya cidule kwacitika moyenela.
Nchito E: Kuzindikila Zolembedwa Zili Ndi Mvekelo Zosiyana -Siyana Ndi
malemba olumikizana (Decoding Text With Variety Of Sounds And Blends)
I. Mphunzitsi:
● Sewenzesani makhadi Ali ndi mvekelo mts, mdz, mkw, ndi phw.
158
● Zindikilani mvekelo imodzi -imodzi pa nthawi.
● Udzani aphunzi kuti Achule mau Ali ndi mvekelo zophatikizana izi.
● Pelekani nkhani momwe muli mvekelo zonse za tsiku ndipo powelenga
zindikilani mamvekelo awa mts, mdz, mkw, ndi phw.
II. Aphunzi :
● Zindikilani mvekelo mts, mkw, phw, ndi mdz pamakhadi oonetsedwa.
● Achule mau omwe Ali ndi mvekelo mts, mdz, mkw, ndi phw.
● Awelenge nkhani yopatsidwa ndi Kuzindikila mvekelo zonse zopasidwa pa tsiku.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuzindikila mvekelo mnkhani kwacitidwa moyenela.
CIGAWO: MVETSO
Mutu 1: Mvetso ya kumvetsela
Mutu Waung’ono 1: Colinga ceni-ceni
Luso Lapadela: Kuzindikila ndi kusonyeza colinga ceni-ceni ca uthenga umene
amva.
Ciyambi: Mutu uyu udzaona pa kuzindikila ndi kusonyeza colinga ceni-ceni
ca uthenga umene wamveka, kufupukitsa uthenga, kuzindikila colinga ca nkhani ndi
kuzindikila zoona za nkhani.
Mau Ofunika Kudziwa: Colinga, Kusonyeza, Uthenga, Kufupukitsa, Nkhani,
Zoona
Zida Zophunzitsila Ndi Zophunzilila: Mabuku a aphunzi , Machati a Nkhani.
159
Mfundo Zophunzitsa:
● Phunzitsani aphunzi m’mene angazindikilile colinga ceni-ceni ca uthenga
umene amva.
● Phunzitsani aphunzi m’mene angafupikitsile uthenga.
● Phunzitsani aphunzi m’mene angazindikilile colinga ca nkhani ndi
m’mene angazindikilile zoona za nkhani.
Nchito A: Kuzindikila Ndi Kusonyeza Colinga Ceni-Ceni Ca Uthenga
Umene Wamveka.
I. Mphunzitsi:
● Nenani nkhani yaifupi yomwe ili ndi uthenga omveka bwino
Citsanzo:
Maliya ndi mwana waulemu. Makolo ake amukonda kwambili. Iye akabwela
kucokela ku sukulu , amatunga madzi ndi kusuka mbale. Uyu ndi mwana wocititsa
cidwi kwambili.
● Kambilanani colinga ceni-ceni ca uthenga umene uli munkhaniyi.
● Nenani nkhani ina yaifupi yomwe ili ndi uthenga womveka bwino. Udzani aphunzi kuti
azindikile colinga ceni-ceni ca uthenga umene amva m’nkhaniyo.
II. Aphunzi:
● Amvele nkhani yofotokezedwa ndi mphunzitsi
● Azindikile colinga ceni-ceni ca uthenga umene amva m’nkhani.
● Anene nkhani m’magulu ao yomwe ili ndi uthenga womveka bwino’.
160
Muyeso Woyembekezeleka: Kuzindikila ndi kusonyeza colinga ceni-ceni ca uthenga m’nkhani
kwacitika moyenela.
Nchito B: Kufupukitsa nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Phunzitsani aphunzi m’mene angafupikitsile nkhani.
● Fotokozani kwa aphunzi kuti pofupikitsa uthenga timatenga mfundo zeni-zeni za nkhani.
● Pelekani citsanzo comveka bwino ca kufupikitsa uthenga ponena nkhani yaifupi ndi
kunena mfundo zeni-zeni za nkhaniyo.
II. Aphunzi :
● Amvesele zolankhula mphunzitsi
● Awelenge nkhani yopatsidwa.
● Ayetsese kufupikitsa nkhani pogwilitsa nchito mfundo zeni-zeni za nkhani.
Muyeso Woyembekezeleka: Dongosolo yakufupukitsa nkhani yacitika moyenela.
Mutu Waung’ono 2: Cilungamo Ndi Zoganiza.
Ciyambi : Mutu waung’ono uyu udzaona pa zacilungamo ndi zoganiza za
munthu kucokela mnkhani.
Mau Ofunikila Kudziwa: Cilungamo, maganizo.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Buku ya nkhani, chati ya nkhani.
Mfundo Zophunzitsa:
● Cilungamo ndi zoganiza mnkhani.
● Kusiyanitsa pa zacilungamo ndi zoganiza mnkhani.
161
Nchito A: Kupeza Zoganiza Kucokela Mnkhani
I. Mphunzitsi:
● Lembani nkhani pa bolodi
● Welengani nkhani ku aphunzi
Citsanzo
Ayisi kilimu ndi cakudya cabwino mu calo conse. Koma ine ndikonda mtundu wopangidwa ndi
cokoleti.
● Funsani aphunzi mafunso awa kuti mumvele zoganiza Zao.
1. Kodi munthu uyu anali kuganiza ciani mnkhaniyi?
2. Cifukwa ninji ayisi kilimu anthu ambili aikonda?
3. Kodi Inu muikonda ayisi kilimu?
4. Ndicifukwa nciani muikondela?
II. Aphunzi :
● Awelenge nkhani.
● Ayankhe mafunso pakupeleka maganizo ao pa nkhani.
● Akambilane ndi kugawana maganizo ao pa nkhani.
Muyeso Woyembekezeleka: Kupeza zomwe munthu aganiza pa nkhani zacitika moyenela.
Nchito B: Kupeza Zacilungamo Mnkhani
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani kwa aphunzi.
162
Citsanzo
Dzuwa inalengedwa ndi mulungu. Iyo imacokela kumawa ndi kulowela ku madzulo. Koma
anthu ambili akhulupilila kuti dzuwa siyiyenda .
● Funsani aphunzi pa za nkhani yowelengedwa.
1. Kodi zacilungamo mu nkhaniyi ndi zotani?
2. Kodi ndi zoona kuti dzuwa icokela ku mawa?
3. Kodi ndi cilungamo kuti dzuwa siyiyenda?
II. Aphunzi :
● Awelenge nkhani
● Akambilane pa nkhani yomwe awelenga
● Ayankhe mafunso ndi Kulankhula cilungamo pa zomwe Zalembedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kupeza cilungamo mnkhani yolembedwa kwacitidwa moyenela.
Mwacidule : Mutu uyu unali kuona pa kuzindikila ndi kusonyeza colinga ceni-ceni ca uthenga
umene wamveka, kufupukitsa uthenga, kuzindikila colinga ca nkhani ndi kuzindikila zoona za
nkhani.
Mutu 2: Mvetso Ya Kuwelenga
Mutu Waung’ono : Zoona Za Nkhani
Luso Lapadela: Kupeleka uthenga ofotokozedwa mokwana mndime (Ziganizo ziwili kapena
zitatu)
Ciyambi: Mutu uyu udzaona pa kunena zomwe zawelengedwa ,Ocita sewelo,
malo ocitikila sewelo ndi m’mene sewelo linacitikila kucokela ku ciyambi mpaka
kumapeto, kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa pophatikizapo
163
poyankha mafunso otele; ( Ciani? Ndani? Kuti? Liti? Motani?) ndi kunena
mwatsatane-tsatane wa zocitika mnkhani.
Mau Ofunikila Kudziwa: mvetso, zoona, cilungamo.
Zida Zophunzitsila Ndi Kuphunzilila: Mchati ya nkhani, Mabuku a nkhani.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kunena (kufotokoza) zomwe zawelengedwa.
● kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa.
● kunena mwatsatane-tsatane wa zocitika mnkhani.
Nchito A: Kunena Zomwe Zawelengedwa
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani yosangalatsa yomwe ifotokoza za Ocita sewelo
● Uzdani aphunzi kuti nawonso awelenge nkhani yomwe mphunzitsi wawelenga
● Funsani aphunzi mafunso kucokela ku nkhani yomwe awelenga.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku nkhani yowelengedwa ndi mphunzitsi
● Awelenge nkhani yomwe mphunzitsi wawelenga.
● Anene zomwe amvela atawelenga nkhani.
Muyeso Woyembekezeleka: Kunena zomwe zawelengedwa kwacitika moyenela.
Nchito B: Kuyankha Mafunso Kucokela Ku Zomwe Zawelengedwa
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani yaifupi kwa aphunzi.
164
● Funsani aphunzi kuti awelenge nkhani yomweyo
● Udzani aphunzi kuti awelenge nkhani m’magulu awili-awili.
● Funsani mafunso kucokela ku nkhani yowelengedwa.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku nkhani yowelengedwa
● Awelenge nkhani onse pamodzi
● Awelenge nkhani awili-awili
● Ayankhe mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa kwacitika
moyenela.
Nchito C: Kunena Mwatsatane-Tsatane Wa Zocitika Mnkhani
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani yaifupi yoyenelela pomwe aphunzi akumvetsela modekha.
● Fotokozani tsatane-tsatane wa nkhani yomwe mwawelenga.
● Uzani aphunzi kuti nawonso awelenge nkhani yaifupi yoyenelela ndipo
amvetsetse nkhaniyo.
● Udzani aphunzi kuti Afotokoze tsatane-tsatane wa nkhani yomwe awelenga
kucokela ku ciyambi mpaka kuothela.
II. Aphunzi:
● Amvelele ku nkhani yowelengedwa
● Amvetsele tsatane – tsatane wa nkhani wofotokozedwa ndi mphunzitsi
● Anene tsatane-tsatane wa zocitika m’nkhani yomwe awelenga kucokela ku
ciyambi mpaka kothela
● Awelenge nkhani yaifupi ndi Kufotokoza tsatane – tsatane wa nkhani.
165
Muyeso Woyembekezeleka: Kunena tsatane-tsatane wa zocitika mnkhani kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa Kunena zomwe zawelengedwa, kuyankha
mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa ndi kunena tsatane-tsatane wa zocitika mnkhani.
Mutu : Malembedwe
Mutu Waung’ono 1: Kapangidwe ka lembo
Ciyambi : Mutu waung’ono uyu udzaona pa kapangidwe ndi kujambula malembo.
Luso Lapadela : Kulemba malembo
Mau Ofunikila Kudziwa : Malembedwe, malembo.
Zida Zophunzitsila Ndi Zophunzilila : Chati ya malembo, pensulo, mapepala.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuphunzitsa mapangidwe a lembo.
● Malembedwe a malembo akulu ndi ang’ono.
Nchito A: Kujambula Malembo
I. Mphunzitsi:
● onetsani aphunzi kabuku ka malembedwe a malembo.
● onetsani ndi kusonyeza kagwilidwe ka pensulo polemba.
● phunzitsani molembela lembo iliyonse kwa aphunzi pa mapepala ao.
Zitsanzo:
166
eeeeeeeeeeeeeeeeeeeeeee
kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk
mmmmmmmmmmmmmmm
II. Aphunzi :
● Amvetsele kwa Mphunzitsi molembela malembo.
● Ayetselele kulemba malembo pa mapepala ao.
● Alembe malembo akulu paokha ndiponso ang’ono m’njila yolungama.
Zocita:
Jambulani malembo awa.
1. a a a a a a a
2. b b b b b b b
3. c c c c c c c
Muyeso Woyembekezeleka: kujambula ndi kulemba malembo kwacitika moyenela.
Nchito B: Kulemba Malembo
I. Mphunzitsi :
● onetsani aphunzi kabuku ka malembedwe a malembo.
● onetsani ndi kusonyeza kagwilidwe ka pensulo polemba.
● phunzitsani molembela lembo iliyonse kwa aphunzi pa mapepala ao.
Zitsanzo:
aaaaaaa
167
bbbbbbb
ccccccc
II. Aphunzi :
● Amvetsele kwa Mphunzitsi molembela malembo.
● Ayetselele kulemba malembo pa mapepala ao.
● Alembe malembo akulu paokha ndiponso ang’ono m’njila yolungama.
Muyeso Woyembekezeleka: Kujambula ndi kulemba malembo kwacitika moyenela.
Mutu Waung’ono 2: Kujambula Mau m’malembedwe okhazikika
Ciyambi: Mutu waung’ono uyu udzaona pakujambula mau m’malembedwe okhazikika
Luso Lapadela: Kulemba mau mnjila yokhazikika.
Mau Ofunikila Kudziwa: Malembedwe, kujambula, kukhazikika.
Zida Zophunzitsila Ndi Zophunzilila: Machati ya malembedwe, pensulo, mapepala.
Mfundo Zophunzitsa:
● Malembedwe okhazikika
● Kujambula mau m’malembedwe okhazikika
Nchito A: Kujambula Mau Mumalembedwe Abwino Ndiponso Okhazikika.
168
I. Mphunzitsi:
● Onetsani mau olembedwa pa pepala.
● Udzani aphunzi kuti ajambule mau aja m’malembedwe oyenela.
Zitsanzo:
1. Mdzathu
2. Mdzandipeza
3. Mdzabwela
II. Aphunzi:
● Aone mau olembedwa pa pepala.
● Alembe mau aja m’malembedwe abwino kulondola lamulo La malembedwe.
Zocita:
Jambulani ndi kulemba mau awa.
1. Mtsikana, mtsinje, mtsinika
2. Nkhuku, nkhani, nkhuni, nkhululu.
Muyeso Woyembekezeleka: Kulemba mau m’malembedwe abwino kwacitika moyenela.
Mutu Waung’ono 3: Mipata Ya Mau.
Ciyambi: Mutu waung’ono uyu udzaona pa kujambula ziganizo m’malembedwe
abwino ndiponso okhazikika pakusiya mipata.
Luso Lapadela: Kusiya mipata m’mau polemba.
Mau Ofunikila Kudziwa: Mau, mipata.
169
Zida Zophunzitsila Ndi Zophunzilila: Makhadi ya mau, chati ya ziganizo.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kalembedwe ka ziganizo
● Mipata ya mau
Nchito : Kujambula Ziganizo M’malembedwe okhazikika Pa Kusiya Mipata.
I. Mphunzitsi:
● Onetsani ziganizo zomwe zilibe mipata pakati pa mau.
● Pelekani zitsanzo pakufotokoza bwino-bwino mosiyila mipata.
Citsanzo:
1. Mtsikanaalikutungamadzi.
= Mtsikana Ali kutunga madzi
II. Aphunzi:
● Aone ziganizo zolembedwa ndipo azindikile mau pomwe apelela pakuonetsa
mipata.
● Apenyelele pa zitsanzo zopatsidwa zakuonetsa ziganizo zopanda mipata.
Zocita:
Onetsani mipata ya mau pa kulemba ziganizo izi.
1. Anyamataanaphwanyamtsukodzulo.
2. Atateanagulankhumbadzulo.
170
Muyeso Woyembekezeleka: Kujambula ziganizo m’malembedwe abwino pakusiya mipata
kwacitika moyenela.
Mwacidule : Mutu uyu unali kuona pa kapangidwe ka malembo, malembedwe
okhazikika, kulemba mau pakusiya mipata ndi kujambula ziganizo mnjila yokhazikika.
MUTU 2: CIMANGILIZO
Mutu Waung’ono: Nkhani Yapafupi
Ciyambi: Mutu uyu uzaona pakujambula zinthunzi zomwe zidzapeleka uthenga
womangilizidwa pamodzi.
Luso Lapadela: Kulemba nkhani yapafupi
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Phensulo, Pepala, Makileyoni.
Mau Ofunikila Kudziwa: Zithunzi, Uthenga, Kujambula.
Mfundo Zophunzitsila:
● Fotokozelani aphunzi kuti tingathe kufotokoza malingalilo pakulemba nkhani yapafupi
yomwe tiganiza.
● Patsani citsanzo camalingalilo omwe angalembedwe mkankhani kapafupi.
Nchito: Kulemba Nkhani Yapafupi
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti alembe kankhani kapafupi pa cinthu comwe akonda kwambili
● Pelekani citsanzo ca nkhani yapafupi
171
Nkhani
Bechani ndi mwana wosamvela.
Kawili-kawili amacita ndeu ndi anzake powatema myala,
Dzulo, mphunzinzitsi anampanda ndi kumpatsa cilango kamba kakuba mapensulo a anzake
II. Aphunzi:
● Amvetsele nkhani yokambidwa ndi mphunzitsi.
● Alembe nkhani yao-yao yapafupi
Muyeso Woyembekezeleka: Kulemba nkhani yaifupi kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutuyu unali kuona pa kulemba nkhani yapafupi yao-yao aphunzi
172
CAPAMUTU 6: KULOWEZA MAU OPINDA
LILIME
CIGAWO: KUMVETSELA NDI KULANKHULA
Ciyambi: Cigawo ici cidzaona pa kumvetsela ndi kulankhula zomwe ndi nthambi za
maluso a kachulidwe ka mau ndi kasankhidwe ka mau ogwilitsa nchito polankhula. Cigawoci
cidzaonanso pa kuwelenga mofulumila, matanthauzo a mau ndi mvetso ya kumvetsela ndi ya
kuwelenga. Cidzaonanso pa malembedwe owelengeka ndi okhazikika.
Mutu: ZIlapi ndi mau opinda lilime
Mutu waung’ono: Mau opinda lilime
Ciyambi: Mutu waung’ono uyu udzaona pa mau opinda lilime, malankhulidwe ake ndi
zolinga zosiyana-siyana za mau opinda lilime.
Luso Lapadela: Kuloweza mau opinda lilime
Mau ofunika kudziwa:
Zilapi, ndagi, kupinda, lilime, kuloweza, kuceza, kufulumila, tanthauzo, kulondola,
kuthandiza, luso, zosangalatsa.
Zida zophunzitsila ndi zophunzilila: Mabuku a aphunzi owelenga, mabuku a zilapi ndi a mau
opinda lilime .
Mfundo zophunzitsa: Kuphunzitsa aphunzi mau opinda lilime ndi malowezedwe ake.
Nchito: Kuloweza mau opinda lilime
I Mphunzitsi:
173
● Lankhulani ciganizo ca mau opinda lilime modekha ndiponso mofulumila kwa
aphunzi ndipo muwafunse zomwe amvapo.
● Fotokozani tanthauzo la mau opinda lilime kwa aphunzi (Mau opinda lilime ndi
ziganizo zopangidwa kukhala zobvuta kalankhula mofulumila ndi molondola mau
cifukwa ca kufanana kwa mamvekedwe a mau m’ziganizozo. Mau opinda lilime
amagwilitsidwa nchito kukhala masewela a mau, kuphunzila kulankhula, kuceza ndi
zosangalatsa. Yamathandiza kupititsa patsogolo maluso a kachulidwe ka mau,
kuwelenga mofulumila ndi kulankhula zofunika kulemba).
● Lankhulani ciganizo ca mau opinda lilime cimodzi mofulumila ndi kuuza aphunzi
kuti acilankhulenso mofulumila.
Mau opinda lilime:
Citsanzo:
Mnkhwele wamankhwala wagwa mphwai ndi kutaya mnkhwani pomva mtswatswa
wa nkhwali mnkhalango.
● Kambilanani momwe aphunzi alankhulila mau opinda lilime.
● Uzani aphunzi kuti alankhule mau opinda lilime yomwe adziwa.
● Kambilanani zolankhula zao.
● Lankhulani mau opinda lilime osiyana-siyana ndi aphunzi.
● Uzani aphunzi m'modzi-m'modzi kuti alankhule mau opinda lilime omwe
mukukambilana nao.
II Aphunzi:
● Amvetsetse pomwe mphunzitsi akulankhula mau opinda lilime ndi kuyankha mafunso.
● Kumvetsela ku tanthauzo la mau opinda lilime.
● Kulankhulanso mau opinda lilime okambidwa ndi mphunzitsi.
● Kukambilana ndi mphunzitsi momwe mau opinda lilime akambideila.
● Alankhule mau opinda lilime m'modzi-m'modzi pamodzi ndi mphunzitsi.
● Kukambilana ndi mphunzitsi momwe alankhulila mau opinda lilime.
174
Muyeso Woyembekezeleka: Kuloweza mau opinda lilime kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali uzaona pa mau opinda lilime, malankhulidwe ake ndi
zolinga zosiyana-siyana za mau opinda lilime.
CIGAWO: KUWELENGA
Mutu: Kuzindikila Masilabe
Mutu Waung’ono: Kuzindikila mvekelo mtsw-, mphw-, nkhw-, mnkhw-
Lambulo: mutu waung’ono uyu udzayang’ana pa kuzindikila masilabe m’mau
olankhulidwa, kucita masewela owelenga masilabe, kupanga mau olankhulidwa pogwilitsa
nchito masilabe ndi kucita masewela opanga mau.
Luso lapadela: Kuzindikila masilabe ndi kupanga mau pogwilitsa nchito masilabe Mtswa,
mtswe, mtswi.
Mphwa, mphwe, mphwi.
Nkhwa, nkhwe, nkhwi.
Mnkhwa, mnkhwe, mkhwi
Mau ofunika kudziwa: Masilabe, mau, chati, makhadi
Zida zophunzitsila ndi zophunzilila:
Chati ya masilabe, mabuku a aphunzi owelenga ndi makhadi ya masilabe.
Mfundo zophunzitsa:
● Kuzindikila masilabe omwe apanga mau.
● Kuzindikila malembo omwe apanga masilabe.
175
● Kupanga mau pogwilitsa nchito masilabe.
Nchito A: Kuzindikila masilabe m’mau olankhulidwa
I Mphunzitsi:
● Lankhulani mau osiyana-siyana ndi kuuza aphunzi zigawo za mauwo kuti ndiye masilabe.
Citsanzo:
Mu liu ‘mtswatswa’ muli masilabe awili (2), mtswa - tswa.
● Lankhulani mau osiyana-siyana pamodzi ndi aphunzi ndi kuyagawa-gawa.
Citsanzo:
Kamtswatswako Ka - mtswa - tswa - ko
● Uzani aphunzi kuti alankhule mau awo-awo, kuyagawa-gawa ndi kuwelenga nambala ya
masilabe omwe alimo.
● Citani cimodzi-modzi ndi mau ena osiyana-siyana.
II Aphunzi:
● Kumvetsela pomwe mphunzitsi akufotokoza masilabe.
● Alankhule mau osiyana-siyana ndi kuyagawa-gawa.
● Alankhule mau awo-awo, kuyagawagawa ndi kuwelenga nambala ya masilabe m'mauwo.
Nchito B: Kucita masewela owelenga masilabe
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kuwelenga nambala ya masilabe m’mau olankhulidwa mwa kuwomba
m'manja kulingana ndi nambala ya masilabewo.
Citsanzo:
mnkhwele mnkhwe ----- le (kuomba kawili ------ 2).
mnkwani mnkhwa ----- ni (kuomba kawili ------ 2).
176
● Uzani aphunzi kuti acite masewela owelenga nambala ya masilabe omwe ali m'mau
poomba m'manja.
II Aphunzi:
● Aonetsetse pomwe mphunzitsi akupeleka citsanzo ca nambala ya masilabe m'mau
poomba m'manja.
● Acite masewela owelenga nambala ya masilabe m'mau poomba m’manja.
● Citani cimodzi-modzi ndi mau omwe ali ndi masilabe ena onse otsalila.
a e i o u
mtsw mtswa mtswe mtwsi mtswo mtswu
mphw mphwa mphwe mphwi mphwo mphwu
nkhw nkhwa nkhwe nkhwi nkhwo nkhwu
mnkhw mnkhwa mnkhwe mnkhwi mnkhwo mnkhwu
Muyeso Woyembekezeleka: Kucita masewela owelenga masilabe kwacitika moyenela.
Nchito C: Kupanga mau olankhulidwa pogwilitsa nchito masilabe.
I Mphunzitsi:
● Pangani mau olankhulidwa pogwilitsa nchito masilabe. Citsanzo:
mtswatswa,
mtswetswetswe, mtswitswi.
II Aphunzi:
177
● Apange mau pogwilitsa nchito masilabe.
Nchito D: Kucita masewela opanga mau
I Mphunzitsi:
● Pangani mau osiyana-siyana kucokela ku masilabe olankhulidwa.
Citsanzo:
mtswatswa – mphatswa, mtswetswetswe – tswetswe.
● Uzani aphunzi kuti apange mau osiyana-siyana kucokela ku masilabe
olankhulidwa.
II Aphunzi:
● Amvetsele modekha kwa mphunzitsi pomwe akupanga mau kucokela ku masilabe.
● Apange mau osiyana-siyana kucokela ku masilabe olankhulidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuzindikila masilabe kucokela ku mau olankhulidwa kwacitidwa
moyenela.
Mwacidule: Aphunzi aphunzila kuzindikila masilabe, kucita masewela owelenga
nambala ya masilabe kucokela ku mau olankhulidwa, kupanga mau kucokela ku masilabe
olankhulidwa ndi kucita masewela opanga mau olankhulidwa.
Mutu: Kupanga Masilabe
178
Mutu Waung’ono 2: Masilabe
Luso Lapadela: Kulumikidza makonsonanti ndi mavawelo kupanga masilabe.
Mau ofunika kudziwa: Makonsonanti, mavawelo, Kulumikidza.
Nchito A: Kupanga masilabe kucokela ku makonsonanti ndi mavawelo.
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kupanga masilabe polumikidza makonsonanti ndi mavawelo.
Citsanzo:
Mphw ---- a mphwa.
Mphw----e mphwe.
● Uzani aphunzi kuti apange masilabe ena mofanana.
a e i o u
mtsw mtswa mtswe mtswi mtswo mtswu
mphw mphwa mphwe mphwi mphwo mphwu
nkhw nkhwa nkhwe nkhwi nkhwo nkhwu
mnkhw mnkhwa mnkhwe mnkhwi mnkhwo mnkhwu
II Aphunzi:
● Kumvetsela ndi akuonetsetsa pomwe mphunzitsi akupeleka citsanzo ca kupanga masilabe
pogwilitsa nchito makonsonanti ndi mavawelo.
● Apange masilabe ena pogwilitsa nchito makonsonanti ndi mavawelo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kulumikidza masilabe kupanga mau kwacitka moyenela.
179
Nchito B: Kuwelenga chati ya masilabe
a e i o u
mtsw mtswa mtswe mtswi mtswo mtswu
mphw mphwa mphwe mphwi mphwo mphwu
nkhw nkhwa nkhwe nkhwi nkhwo mkhwu
mnkhw mnkhwa mnkhwe mnkhwi mnkhwo mnkhwu
I Mphunzitsi:
● Citani citsanzo ca kuwelenga masilabe pa chati ya masilabe.
Citsanzo:
Kuwelenga, kucokela dzanja lamanzele kupita ku dzanja lamanja, kucokela kumwamba
kupita pansi, mopendeka (diagonal ), zigizagi.
● Uzani aphunzi kuti adzawelenge masilabe pa chati ya masilabe m’modzi-m’modzi.
● Ikani aphunzi awili-awili ndi kuwapatsa timachati ting’ono-ting’ono kuti awelenge.
II Aphunzi:
● Aonetsetse zomwe mphunzitsi akucita popanga masilabe pa chati ya masilabe.
● Awelenge masilabe pa chati ya masilabe.
● Awelenge masilabe pa timachati ting’ono-ting’ono ali awili-awili.
Muyeso Woyembekezeleka: kuwelenga masilabe kucokela pa chati ya masilabe
kwacitika moyenela.
180
Nchito C: Kusankha masilabe
I. Mphunzitsi:
● Sonyezani aphunzi kusankhani masilabe kucokela pa makhadi ya malembo, masilabe ndi
mau .
● Uzani aphunzi kuti asankhe masilabe kucokela pa makhadi ya malembo, masilabe ndi
mau.
Citsanzo:
Uzani aphunzi kuti asankhe masilabe pa makhadi otsatilawa:
tema, mwa, mwala, kh, phu, ndende, mbi, mtswa, mtsw, njuzi, ny, ng’, ng’o, mphwa, mf,
khwe, bwino, thyo, vwe, gwi, dwambe.
mnkhwele vwe nyemba nkhwa Mnkhw mphwi nthyo
mwa gwi mtswa mph nd ng'o mwala
ng' tyo. mnkhwani njuta nkhwe bv ng'ombe
dwambe kh ndende kwi phula nthy mnkhwe
II Aphunzi:
● Aonetsetse zomwe mphunzitsi akucita posankha makhadi ya malembo, masilabe ndi
mau.
● Asankhe masilabe kucokela pa makhadi ya malembo, masilabe ndi mau moyenela.
Muyeso Woyembekezeleka: Kusankha masilabe kucokela pa makhadi ya malembo, masilabe
ndi mau kwacitika moyenela.
Nchito D: Kusintha Masilabe
181
I Mphunzitsi:
● Phunzitsani kasinthidwe ka malembo ku masilabe.
Citsanzo:
“mphwa” ngati mwacotsako “mphw” ndi kuikako “phw” iknala “phwa”.
● Uzani aphunzi kuti asinthe malembo ndi kupanga masilabe atsopano.
II Aphunzi:
● Kumvetsela mofatsa pomwe mphunzitsi akupeleka citsanzo ca kusintha masilabe ndi
kupanga mau atsopano.
● Asinthe malembo ku masilabe ndi kupanga masilabe atsopano.
Muyeso Woyembekezeleka: kusintha masilabe mu mau kwacitika moyenela.
Nchito E: Kulumikidza makonsonanti omwe sapanga mvekelo limodzi ndi
mavawelo kupanga masilabe.
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca makonsonanti omwe sapanga mvekelo limodzi ndi kupanga
masilabe poikako mavawelo.
Citsanzo:
mphwa, ngwe, thyo, mthyu, mkwi.
● Uzani aphunzi kuti apange masilabe awo pogwilitsa nchito makonsonanti omwe amveka
mosiyana popanga masilabe.
II. Aphunzi:
● Aonetsetse citsanzo ca makonsonanti omwe sapanga mvekelo limodzi poikako mavawelo
ndi kupanga masilabe.
182
● Apange masilabe kugwilitsa nchito makonsonanti omwe sapanga mvekelo imodzi
poikako mavawelo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kusinthanitsa malembo ku masilabe ndi kupanga masilabe
atsopano kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kupanga masilabe kucokela ku makonsonanti ndi
mavawelo, kuwelenga chati ya masilabe, kusankha masilabe kucokela ku makhadi ya malembo,
masilabe ndi mau ndi kusintha malembo ku masilabe kuti yapange masilabe yatsopano.
Mutu2: Kupanga Mau
Mutu waung’ono 2: Mau (mtswi/mphwi/nkhw/mnkhw)
Lambulo: Mutu waung’ono uyu udzaona pa kulumikidza masilabe ndi kupanga mau
kusintha ndi kucotsa masilabe ndi kuwelenga nambala ya masilabe.
Luso lapadela: Kulumikidza masilabe ndi kupanga mau.
Mau ofunika kudziwa: Kulumikidza, Kusintha, kucotsa, tsopano
Zida zophunzitsila ndi zophunzilila: Makhadi, chati, masilabe, mphunzi
Mfundo zophunzitsa:
● Kulumikidza masilabe ndi kupanga mau.
● Kusintha ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano.
● Kuzindikila masilabe m’mau ndi kuwelenga nambala ya masilabe m’mau.
Nchito A: Kulumikidza masilabe ndi kupanga mau (mtswi/mphw/nkhw//mnkhw)
I Mphunzitsi:
● Sonyezani kulumikidza masilabe kucokela pa chati ya masilabe ndi kupanga mau.
183
● Lumikidzani masilabe kucokela ku makhadi ya masilabe ndi kupanga mau.
● Uzani aphunzi kuti alumikidze masilabe kucokela pa chati ya masilabe ndi ku makhadi
ya masilabe ndi kupanga mau.
II Aphunzi:
● Aonetsetse kalumikidzidwe ka masilabe kucokela pa chati ya masilabe ndi kupanga mau.
● Alumikidze masilabe kucokela ku makhadi ya masilabe ndi kupanga mau.
● Alumikidze masilabe kucokela pa chati ya masilabe ndi ku makhadi ya masilabe ndi
kupanga mau.
Muyeso Woyembekezeleka: Kulumikidza masilabe ndi kupanga mau kwacitika moyenela.
Nchito B: Kusintha ndi kucotsa masilabe
I Mphunzitsi:
● Sinthani ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano.
Citsanzo:
“nkhwangwa” mukacotsa “nkhwa” ndi kuikako “mnkhwa” ikhala “mnkhwangwa”,
“zamankhwala”, mukacotsako “za” ikhala “mankhwala”.
● Uzani aphunzi kuti asinthe ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano moyenela.
II Aphunzi:
● Aonetsetse citsanzo ca kusintha ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano.
● Asinthe ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano.
184
Muyeso Woyembekezeleka: Kusintha ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano
kwacitika moyenela.
Nchito C: Kuzindikila masilabe m’mau.
I Mphunzitsi:
● Phunzitsani m’mene aphunzi angazindikilile masilabe m’mau.
Mwacitsanzo, konsonanti iliyonse yomwe ili ndi vawelo kutsogolo kwake imachedwa
kuti silabe.
Citsanzo:
mu liu lakuti “lunkhwakwa” muli masilabe atatu (3) “lu”, “nkhwa” ndi “kwa”.
● Uzani aphunzi kuti azindikile masilabe m’mau opatsidwa.
Mau:
Cinkhwa, nkhwakwa, nkhwangwa, nkhwali, nkhwekwe, nkhwewakwewa,
mnkhwani, mankhwala, bilimankhwe, nkhwazi.
II Aphunzi:
● Amvetsele kwa mphunzitsi m'mene angazindikilile masilabe m'mau.
● Azindikile masilabe m’mau opatsidwa ndi m’mabuku owelenga.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuzindikila masilabe m’mau kwacitika moyenela.
Nchito D: Kuwelenga nambala ya masilabe
I Mphunzitsi:
● Lembani mau pa bolodi ndi kuwelenga nambala ya masilabe m’mau olembedwawo.
● Citsanzo:
“bilimankhwe” muli masilabe anai (4): bi – li – ma - nkhwe.
185
● Uzani aphunzi kuti alankhule mau, anene ndi kulemba nambala ya masilabe m’mauwo.
II Aphunzi:
● Alankhule mau, anene ndi kulemba nambala ya masilabe m’mauwo.
Meyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga nambala ya masilabe m’mau kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kulumikidza masilabe ndi kupanga mau, Kusintha
ndi kucotsa masilabe ndi kupanga mau atsopano, kuzindikila masilabe m’mau ndi kuwelenga
nambala ya masilabe m’mau.
Mutu 3: Kuwelenga Mofulumila
Mutu Waung’ono 1: Kuwelenga mau mokweza.
Lambulo: Mutu uyu udzaona pa kuwelenga mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau
koyenela.
Luso Lapadela 2: Kuwelenga mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau komveka moyenela.
Mau ofunika kudziwa: Nthano, bolodi, kufulumila.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Makhadi ya mau, timabuku ta nthano, mabuku a
aphunzi.
Mfundo Zophunzitsa: Kuwelenga mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau komveka bwino.
Nchito: Kuwelenga mau
I Mphunzitsi:
186
● Pelekani citsanzo ca kuwelenga mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau komveka
koyenela powelenga mau pa bolodi ndi pogwilitsa nchito timabuku ta nthano.
● Uzani aphunzi kuti awelenge mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau komveka
moyenela monga m'citsanzo.
● Ikani aphunzi awili-awili ndi kuwauza kuti awelenge mau mofulumila ndi kachulidwe ka
mau komveka bwino monga mcitsanzo ca mphunzitsi.
II. Aphunzi:
● Amvetsele modekha pomwe Mphunzitsi akupeleka citsanzo ca kuwelenga Mofulumila.
● Awelenge mau mofulumila ndi kachulidwe Ka mau koyenela monga m'citsanzo.
● Awelenge mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau komveka koyenela.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau komveka
bwino kwacitika moyenela.
Luso Lapadela 3: Kuwelenga ndime mokweza ndi kachulidwe ka mau komveka bwino.
Mau Ofunika Kudziwa: Nthano, bolodi, kufulumila.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Makhadi ya mau, timabuku ta nthano, mabuku a
aphunzi.
Mfundo zophunzitsa: Kuwelenga mau mofulumila ndi kachulidwe ka mau komveka bwino.
Nchito A: Kuwelenga ndi kumvetsa ziganizo
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kuwelenga ndime mofulumila.
● Welengani ndime pamodzi ndi aphunzi ndipo funsani aphunzi mafunso kucokela mu
ndime yowelengedwa.
II Aphunzi:
187
● Kumvetsela pomwe mphunzitsi akupeleka citsanzo ca kuwelenga ndime mofulumila.
● Awelenge ndi kuyankha mafunso kucokela ku ndime yowelengedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga ndime mofulumila, kuimvetsetsa ndi kuyankha
mafunso kucokela m'ndimeyo kwacitika moyenela.
Nchito B: Kuwelenga ndime kucoka pa ziganizo ziwili (2) kufika pa ziganizo zisanu
(5) ( kuwelenga kwa gulu, kubwelezela zomwe wina wawelenga kale, kuwelenga awili-
awili).
I Mphunzitsi:
● Welengani ndime momveka bwino pomwe aphunzi akumvetsela modekha.
● Welengani Pamodzi ndi aphunzi (Choral Reading).
● Uzani aphunzi kuti adzibwelezela zomwe mphunzitsi akuwelenga (Echo Reading).
● Uzani aphunzi kuti awelenge awili-awili (Paired Reading).
II Aphunzi:
● Amvetsele modekha pomwe mphunzitsi akupeleka citsanzo ca kuwelenga.
● Awelenge pomodzi ndi mphunzitsi.
● Adzibwelezela zomwe mphunzitsi akuwelenga
● Awelenge pamodzi ndi mphunzitsi, abwelezele zomwe mphunzitsi akuwelenga ndiponso
awelenge awili-awili.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga ndime kucoka pa ziganizo ziwili (2) kufika pa ziganizo
zisanu (5), kuwelenga kwa gulu, kubwelezela zomwe wina wawelenga kale, kuwelenga awili-
awili kwacitika moyenela.
188
Nchito C: Kuwelenga momveka ndime yomwe ili ndi mamvekelo ndi malembo
osiyana-siyana.
I Mphunzitsi:
● Lembani malembo, masilabe ndi mau omwe ali ndi mamvekelo osiyana-siyana.
Mwacitsanzo:
Malembo:
mtsw, mkw, thy, mdw, nkh, khw.
Masilabe: mtswa, mphwa, nkhwe, mnkhwe, mkwi, thyo, ndwa, nkhu, khwe.
Mau:
mtswatswa , mphwai, nkhwekwe, mnkhwele,mkwiyo, thyola, nkhunda, khwenga.
● Welengani ndi kumvetsetsa mau opangidwa kucokela ku masilabe omwe apangidwa
ndi malembo amamvekedwe osiyana-siyana.
● Uzani aphunzi kuti alembe, awelenge ndi kumvetsetsa mau opangidwa kucokela ku
masilabe omwe apangidwa ndi malembo amamvekedwe osiyana-siyana.
II Aphunzi:
● Aonetsetse m'mene mphunzitsi akulembela malembo, masilabe ndi mau omwe ali ndi
mamvekelo osiyana.
● Awelenge ndi kumvetsetsa mau omwe ali ndi mamvekelo osiyana.
● Alembe, awelenge ndi kumvetsetsa mau opangidwa kucokela ku masilabe omwe
apangidwa ndi malembo amamvekedwe osiyana-siyana.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuwelenga momveka ndime yomwe ili ndi mamvekelo ndi
malembo osiyana-siyana kwacitika moyenela .
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kuwelenga mau mofulumila pogwilitsa nchito
kachulidwe ka mau komveka bwino.
189
CIGAWO: MAU.
Mutu : Maina
Mutu Waung’ono : Maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
Lambulo: Mutu uyu udzaona pa kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku maina
osaculukitsidwa , kupanga maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa,
Kulinganiza maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa ndi kusinthanitsa zocitikazi ndi
kucita masewela a maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
Luso Lapadela: Kupanga maina oculukitsidwa ndi maina osaculukitsidwa (Mtsw, mphw,
nkhw, mnkhw).
Mau Ofunika Kudziwa: Dzina , maina, kuculukitsa, cimodzi, kuzindikila
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Chati ya maina, .
Mfundo Zophunzitsa: Kazindikilidwe ka maina eni-eni ndi maina wamba
Nchito A: Kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa .
I Mphunzitsi: .
● Sonyezani kunga maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa .
Mwacitsanzo:
1. Mtsogoleli —-- atsogoleli
2. mphunzitsi —-- aphunzitsi
● Pamodzi ndi aphunzi, pangani maina oculukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
● Uzani aphunzi kuti apange ndi kulemba maina oculukitsidwa kucokela ku maina
osaculukitsidwa.
190
II Aphunzi:
● Aonetsetse momwe mphunzitsi akupangila maina oculukitsidwa kucokela ku maina
osaculukitsidwa.
● Pamodzi ndi mphunzitsi, apange maina oculukitsidwa kucokela ku maina
osaculukitsidwa.
● Apange ndi kulemba maina oulukitsidwa kucokela ku maina osaculukitsidwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku Maina osaculukitsidwa
kwacitika moyenela.
Nchito B Kupanga Maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kupanga maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
Citsatnzo
1. Amnkhwele ….. mnkhwele
2. Amphawi ….. m’mphawi
● Pangani maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa pamodzi ndi
aphunzi.
● Uzani aphunzi kuti apange maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa.
II Aphunzi:
● Aonetsetse m'mene mphunzitsi akupangila maina osaculukitsidwa kucokela ku maina
oculukitsidwa.
● Apange maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa pamodzi ndi
mphunzitsi.
● Apange dzina la cinthu cimodzi kucokela ku maina a zinthu zambili.
191
Muyeso Woyembekezeleka: Kupanga maina osaculukitsidwa kucokela ku maina
oculukitsidwa kwacitika moyenela.
Nchito C: Kulinganiza maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa
I Mphunzitsi:
● Sonyezani kulinganiza maina osaculukitsidwa comwe cili ku dzanja lamanzele ndi maina
oculukitsidwa omwe ali ku dzanja lamanja.
Citsanzo:
1. mkwekwesa—-- mikwekwesa 2. mphunzitsi —- aphunzitsi
● Pamodzi ndi aphunzi, linganizani maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
● Uzani aphunzi kuti alinganize maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
II Aphunzi
● Aonetsetse m'mene mphunzitsi akulinganizila maina osaculukitsidwa ndi maina
oculukitsidwa.
● Aonetsetse momwe mphunzitsi akulinganizila dzina la cinthu cimodzi ndi maina ambili
Muyeso Woyembekezeleka: Kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku maina
osaculukitsidwa kwacitika moyenela.
Nchito D: Kucita masewela a maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
I. Mphunzitsi:
● Ikani aphunzi m’magulu a asanu.
● Ikani makhadi ya maina oculukitsidwa ndi makhadi a maina osaculukitsidwa pansi pa
gulu lililonse kuti aphunzi adzipikisana posankha makhadi yofunika kuti asankhe maina
osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
192
● Uzani aphunzi kuti asankhe makhadi ya maina osaculukitsidwa ndi makhadi ya maina
oculukitsidwa.
II. Aphunzi
● Akhale m'magulu a asanu-asanu.
● Alandile makhadi a maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa.
● Asankhe makhadi ya maina oculukitsidwa ndi makhadi ya maina osaculukitsidwa .
Muyeso Woyembekezeleka: kucita masewela osankha maina osaculukitsidwa ndi maina
oculukitsidwa kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kupanga maina oculukitsidwa kucokela ku maina
osaculukitsidwa, kupanga maina osaculukitsidwa kucokela ku maina oculukitsidwa, kulinganiza
maina osaculukitsidwa ndi maina oculukitsidwa ndi kulinganiza maina oculukitsidwa ndi maina
osaculukitsidwa.
CIGAWO: MVETSO
Mutu 1: Mvetso ya Kumvetsela
Mutu Waung’ono 1: Colinga ceni-ceni
Lambulo: Mutu uyu udzaona pa kuzindikila ndi kusonyeza colinga ceni-ceni ca uthenga
umene wamveka, kuzindikila ndi Kupeleka maganizo pa uthenga umene wamveka ndi
kufupukitsa uthenga.
Luso Lapadela: Kuzindikila ndi kusonyeza colinga ceni-ceni ca uthenga umene amva.
Mau Ofunika Kudziwa: Maganizo, lingalilo, maganizo, kusonyeza, uthenga,
kufupikitsa, nkhani, zoona
193
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: mabuku a aphunzi
Mfundo zophunzitsa:
● Phunzitsani aphunzi m’mene angazindikilile colinga ceni-ceni ca uthenga umene amva,
m’mene angafupikitsile uthenga, m’mene angazindikilile colinga ca nkhani ndi m’mene
angazindikilile zoona za nkhani.
Nchito A: Kuzindikila ndi kusonyeza colinga ceni-ceni ca uthenga umene wamveka.
I. Mphunzitsi:
● Nenani nkhani yaifupi yomwe ili ndi uthenga omveka bwino.
Citsanzo:
Ukhondo ndi ofunika kwambili.
Tiyenela kusesa panyumba masiku [Link] tidzateteza matenda ambili
monga cifuwa ndi kolela. Anthu aukhondo amakhala athanzi labwino nthawi
zonse.
● Pamodzi ndi aphunzi, kambilanani colinga ceni-ceni ca uthenga umene uli
m'nkhaniyi.
● Nenani nkhani ina yaifupi yomwe ili ndi uthenga womveka bwino.
● Uzani aphunzi kuti azindikile colinga ceni-ceni ca uthenga umene amva
m’nkhaniyo.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku nkhani yaifupi yomwe mphunzitsi adzanena.
● Pamodzi ndi mphunzitsi, akambilane colinga ceni-ceni ca uthenga umene uli m'nkhani.
● Amvetsele ku nkhani ina yaifupi yomwe ili ndi uthenga womveka bwino.
● Azindikile colinga ceni-ceni ca uthenga umene amva m’nkhani.
194
Muyeso Woyembekezeleka: Kuzindikila ndi kusonyeza colinga ceni-ceni ca uthenga umene
wamveka kwacitika moyenela.
Nchito B: Kufupikitsa uthenga
I. Mphunzitsi:
● Fotokozani kwa aphunzi kuti pofupikitsa uthenga timatenga mfundo zeni-zeni
za nkhani.
● Pelekani citsanzo comveka bwino ca kufupikitsa uthenga ponena nkhani
yaifupi ndi kunena mfundo zeni-zeni za nkhaniyo.
● Kambilanani ndi aphunzi momwe mungafupikitsile uthenga wa nkhani
potengamo mfundo zeni-zeni.
● Uzani aphunzi nkhani yomveka bwino ndipo muwauze kuti aifupikitse
popeleka mfundo zeni-zeni.
II. Aphunzi
● Amvetsele modekha pomwe mphunzitsi akufotokoza m'mene angafupikitsile uthenga.
● Amvetsele mofatsa pomwe mphunzitsi akusimba nkhani yaifupi ndi Kufupikitsa uthenga.
● Akambilane ndi mphunzitsi momwe angafupikitsile uthenga wa nkhani potengamo
mfundo zeni-zeni.
● Abweleze kunena nkhani yomwe mphunzitsi wanena ndi kuifupikitsa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kufupukitsa uthenga kwacitika moyenela
Mutu Waung'ono 2: Zoona ndi malingalilo.
Lambulo: Mutu Waung'ono uyu udzaona pa kuzindikila malingalilo m'nkhani ndi
kuzindikila zoona za nkhani.
Luso Lapadela: Kusiyanitsa zoona ndi malingalilo.
195
Mau Ofunika Kudziwa: Malingalilo, kusiyanitsa, zoona, nkhani, kuzindikila.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Makhadi ya nkhani, mabuku a aphunzi owelenga.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kuphunzitsa tanthauzo la liu "Malingalilo".
● Kuphunzitsa za malingalilo pa nkhani yokambidwa.. .
Nchito A: Kuzindikila malingalilo m'nkhani.
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca nkhani ndipo kambilanani ndi aphunzi pozindikila
malingalilo m'nkhaniyo.
● Kambilanani ndi aphunzi ndipo apeleke maganizo ao pa colinga ca nkhaniyo.
● Nenani nkhani ina yofanana ndi citsanzo ndipo uzani aphunzi kuti apeleke
maganizo ao pa kuzindikila colinga ca nkhaniyo.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku citsanzo ca nkhani.
● Akambilane ndi mphunzitsi pa malingalilo a nkhani yokambidwa.
● Apeleke maganizo ya kuzindikila colinga ca nkhani yonenedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuzindikila colinga ca nkhani kwacitika moyenela.
Nchito B: Kuzindikila zoona za nkhani
I. Mphunzitsi:
● Nenani nkhani yaifupi ya ziganizo zoti aphunzi anu amvetse.
196
Mwacitsanzo:
Kalulu ndi kanyama kocenjela kwambili.
Iko kamanamiza nyama zinzake nthawi zambili.
Kalinso ndi liwilo loculuka zedi. Makutu ake ndi atali-atali ndipo mcila wake
ndi waufupi. Kamakonda kudya udzu wochedwa kasendandulu.
● Kambilanani ndi aphunzi zoona za nkhani yomwe yokambidwa.
● Uzani aphunzi kuti anene zoona za nkhani yomwe amva.
II. Aphunzi:
● Amvetsele ku nkhani yaifupi yokambidwa ndi mphunzitsi.
● Akambilane ndi mphunzitsi pa zoona za nkhani yomwe amva.
● Anene zoona za nkhani yomwe amva.
Muyeso woyembekezeleka: kuzindikila malingalilo m’nkhani ndi kuzindikila zoona za nkhani
kwacitika moyenela.
Mutu 2: Mvetso ya Kuwelenga
Mutu waung’ono : Zoona za nkhani
Ciyambi: Mutu uyu udzaona pa kunena zomwe zawelengedwa (Ocita sewelo, malo
ocitikila sewelo ndi m’mene sewelo linacitikila kucokela ku ciyambi mpaka kumapeto…),
kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa kuphatikizapo ( Ciani? Ndani? Kuti?
Liti? Motani?) ndi kunena zocitika m’nkhani molondola.
Luso lapadela: Kupeleka uthenga wofotokozedwa mokwana m'ndime (Ziganizo ziwili kapena
zitatu)
Mfundo zophunzitsa:
● Kufotokoza zomwe zawelengedwa
197
● kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa
● kunena zocitika m'nkhani molondola.
Nchito A: Kufotokoza zomwe zawelengedwa
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani yosangalatsa yomwe ifotokoza za Ocita sewelo, malo
komwe sewelo linacitikila ndi m’mene sewelo linacitikila kucokela pa
ciyambi mpaka ku mapeto.
● Kambilanani ndi aphunzi za nkhani yomwe yawelengedwa.
● Ikani aphunzi m'magulu ang'ono-ang'ono.
● Uzani aphunzi kuti awelenge nkhani yomwe mphunzitsi wawelenga
mcitsanzo ca kuwelenga.
II. Aphunzi:
● Amvetsele nkhani yomwe yawelengedwa ndi mphunzitsi yofotokoza za Ocita sewelo,
malo komwe kunacikila sewelo ndi momwe sewelo linacitikila kucokela pa ciyambi
mpaka kumapeto.
● Akambilane ndi mphunzitsi za nkhani yomwe yawelengedwa.
● M'magulu a asanu-asanu, awelegenso nkhani yomwe mphunzitsi wawelenga.
Muyeso Woyembekezeleka: Kufotokoza zomwe zawelengedwa kwacitika moyenela.
Nchito B: Kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa
I. Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kuwelenga nkhani yaifupi yoyenelela kwa aphunzi.
● Welengani pamodzi ndi aphunzi.
198
● Uzani aphunzi kuti awelenge nkhani m’magulu a awili-awili.
● Funsani mafunso kucokela ku nkhani yowelengedwa.
II. Aphunzi:
● Amvetsele kwa mphunzitsi pomwe akuwelenga nkhani.
● Awelenge nkhani pamodzi ndi mphunzitsi
● Awelenge nkhani ali awili-awili .
● Ayankhe mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa.
Muyeso Woyembekezeleka: Kuyankha mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa kwacitika
moyenela.
Nchito C: Kunena zocitika m'nkhani molondola.
I. Mphunzitsi:
● Welengani nkhani yaifupi yoyenelela pomwe aphunzi akumvetsela modekha.
● Kambilanani ndi aphunzi zomwe zawelengedwa m'nkhani.
● Fotokozani nkhani yomwe mwawelenga molondola.
● Uzani aphunzi kuti awelenge nkhani yaifupi yoyenela ndipo aimvetsetse.
● Uzani aphunzi kuti Afotokoze nkhani yomwe awelenga kucokela ku ciyambi
mpaka kumapeto.
II Aphunzi:
199
● Amvetsele modekha kwa mphunzitsi pomwe akuwelenga nkhani.
● Akambilane ndi mphunzitsi pa zomwe zawelengedwa m'nkhani.
● Afotokoze zocitika m'nkhani molondola.
● Afotokoze zocitika m’nkhani yomwe awelenga molondola.
Muyeso Woyembekezeleka: Kufotokoza zocitika m'nkhani molondola kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona pa kufotokoza zomwe zawelengedwa, kuyankha
mafunso kucokela ku zomwe zawelengedwa ndi kufotokoza zocitika m’nkhani molondola.
CIGAWO: KULEMBA
Mutu: Malembedwe
Mutu waung’ono1: Mapangidwe a Lembo
Ciyambi: Mutu uyu udzaona pa kujambula malembo, kulemba malembo, kulemba mau
m’malembedwe okhazikika ndi kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika posiya mipata
pakati pa mau.
Luso Lapadela: Kulemba malembo
Mau Ofunika Kudziwa: Malembedwe, owelengeka, okhazikika, mpata, kujambula.
200
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Coko, phensulo, mabuku olembamo aphunzi.
Mfundo zophunzitsa:
● Kusonyeza majambulidwe a malembo kucokela koyambila polemba mpaka kumapeto
poonetsa mayendedwe a dzanja lomwe lili ndi colembela.
● Malembedwe a malembo opatsidwa.
● Kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika posiya mipata pakati pa mau.
Nchito A: Kujambula malembo
I Mphunzitsi:
● Pelekani citsanzo ca kulemba malembo awa : m, t, s, w / m, p, h, w / n, k, h, w / m,
n, k, h, w / m’malembedwe okhazikika m’mizela olembedwelatu pa bolodi.
● Uzani aphunzi kuti ajambule malembo monga m'citsanzo ca mphunzitsi pa bolodi.
● Ongolelani aphunzi pomwe akujambula malembo pa bolodi.
● Uzani aphunzi kuti ajambule malembo omwe alembedwa pa bolodi m'mabuku ao
olembamo.
II Aphunzi:
● Aonetsetse pomwe mphunzitsi akulembela malembo m'malembedwe okhazikika
m'mizela olembedwelatu pa bolodi.
● Ajambule malembo monga m'citsanzo ca mphunzitsi pa bolodi mothandizidwa ndi
mphunzitsi..
● Ajambule malembo omwe alembedwa pa bolodi m’mabuku ao olembamo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kujambula malembo kwacitika moyenela.
Nchito B: Kulemba malembo
201
I Mphunzitsi:
● Sonyezani m’mene malembo alembedwela m’malembedwe okhazikika m’mizela
olembedwelatu pa bolodi.
● Onetsani aphunzi mayambidwe a kulemba malembo kucokela koyambila mpaka
kumapeto.
● Uzani aphunzi kuti adzalembe malembo m’mizela ali pa bolodi.
● Uzani aphunzi kuti alembe malembo opatsidwa m'mabuku ao olembamo.
II Aphunzi:
● Aonetsetse m'mene mphunzitsi akulembela malembo pa bolodi m'mizela olembedwelatu.
● Aonetsetse mayambidwe a kulemba lembo kucokela koyambila mpaka kumapeto kwa
lembo.
● Uzani aphunzi kuti adzalembe malembo m'mizela omwe ali pa bolodi.
● Alembe malembo omwe apatsidwa m'mabuku ao olembamo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kulemba malembo kwacitika moyenela.
Mutu Waung’ono 2: Malembedwe okhazikika
Luso Lapadela: Kulemba mau owelengeka m’malembedwe okhazikika.
Ciyambi: Mutu waung’ono uyu udzaona pa kujambula mau owelengeka m’malembedwe
okhazikika m’mizela opangidwilatu pa bolodi.
Mau Ofunika Kudziwa: Mau, kujambula, mizela, owelengeka, okhazikika.
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Coko, mapensulo, mabuku olembamo aphunzi.
Mfundo Zophunzitsa:
● Kujambula mau m’malembedwe okhazikika.
202
Nchito: Kujambula mau owelengeka m’malembedwe okhazikika.
I Mphunzitsi:
● Lembani mau pa bolodi m’mizela pomwe aphunzi akuonetsetsa mayendetsedwe
a dzanja lomwe likulemba.
● Uzani aphunzi kuti adzajambule mau owelengeka m’malembedwe okhazikika
m’mizela pa bolodi mothandizidwa ndi mphunzitsi.
● Uzani aphunzi kuti ajambule mau owelengeka m’malembedwe okhazikika
m’mizela m’mabuku ao olembamo.
II Aphunzi:
● Aonetsetse m'mene mphunzitsi akulembela mau pa bolodi.
● Ajambule mau owelengeka m'malembedwe okhazikika pa bolodi mothandizidwa ndi
mphunzitsi.
● Ajambule mau owelengeka m’malembedwe okhazikika m’mizela m’mabuku ao
olembamo.
Muyeso Woyembekezeleka: Kujambula mau owelengeka m’malembedwe okhazikika
kwacitika moyenela.
Mutu Waung’ono 3: Kusiya mipata pakati pa mau.
Ciyambi: Mutu waung’ono uyu udzaona pa kujambula ziganizo m’malembedwe
okhazikika posiya mipata pakati pa mau.
Luso Lapadela: Kusiya mipata pakati pa mau.
Mau Ofunika Kudziwa: Kujambula, ziganizo posiya mipata, pakati, mau.
203
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Coko, mapensulo, mabuku owelenga a aphunzi, mabuku
olembamo aphunzi.
Mfundo zophunzitsa:
● Kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika posiya mipata pakati pa mau.
Nchito: Kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika posiya mipata pakati pa mau.
I Mphunzitsi:
● Lembani ziganizo m’malembedwe okhazikika pa bolodi pomwe aphunzi
akuonetsetsa.
● Lankhulani za mipata yomwe mukusiya polemba ziganizo.
● Uzani aphunzi kuti adzajambule ziganizo m’malembedwe okhazikika m’mizela
pa bolodi, (mphunzi m’modzi ciganizo cimodzi), mothandizidwa ndi mphunzitsi.
● Kambilanani za majambulidwe a ziganizo zomwe aphunzi ajambula pa bolodi.
● Uzani aphunzi kuti ajambule ziganizo m’malembedwe okhazikika m’mizela
omwe ali m’mabuku ao olembamo posiya mipata pakati pa mau.
II Aphunzi:
● Aonetsetse m'mene mphunzitsi akulembela ziganizo m'malembedwe okhazikika
m'mizela olembedwelatu pa bolodi.
● Amvetsele kwa mphunzitsi za mipata yomwe akusiya polemba ziganizo.
● Ajambule ziganizo m'malembedwe okhazikika m'mizela olembedwelatu pa bolodi
mothandizidwa ndi mphunzitsi.
● Kambilanani ndi mphunzitsi za majambulidwe a ziganizo zomwe ajambula m'mizela
olembedwelatu pa bolodi.
● Ajambule ziganizo m’malembedwe okhazikika posiya mipata pakati pa mau m'mabuku
ao olembamo.
204
Muyeso Woyembekezeleka: Kujambula ziganizo m’malembedwe okhazikika posiya mipata
pakati pa mau kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu waung’ono uyu unali kuona pa kujambula malembo, Kulemba
malembo, kulemba mau owelengeka m’malembedwe okhazikika ndi Kujambula ziganizo
m’malembedwe okhazikika posiya mipata pakati pa mau.
Mutu 2: Cimangilizo
Mutu Waung’ono: Nkhani Yapafupi
Ciyambi: Mutu uyu uzayanga’na pakujambula zinthunzi zomwe zidzapeleka uthenga
womangilizidwa pamodzi.
Luso Lapadela: Kulemba nkhani yapafupi m’mizele iwili kapena itatu
Zida Zophunzitsila ndi Zophunzilila: Phensulo, Pepala, Makileyoni.
Mau Ofunikila Kudziwa: Zithunzi, Uthenga, Kujambula.
Mfundo Zophunzitsila:
● Fotokozelani aphunzi kuti tingathe kufotokoza malingalilo pakulemba nkhani yapafupi
yomwe tiganiza.
● Patsani citsanzo camalingalilo omwe angalembedwe mkankhani kapafupi.
Nchito: composing a simple story
I. Mphunzitsi:
● Uzani aphunzi kuti alembe kankhani kapafupi pa cinthu comwe akonda kwambili
m’mizele iwili kapena itatu
205
● Pelekani citsanzo ca nkhani yapafupi
Nkhani
Kupanga congo mkalasi ndi koipa.
Kumasokonezana polemba
Ena amalemba zomwe anzao akamba mcongo cija.
II. Aphunzi:
● Amvetsele nkhani yokambidwa ndi mphunzitsi.
● Alembe nkhani yao-yao yapafupi
Muyeso Woyembekezeleka: Kulemba nkhani yaifupi kwacitika moyenela.
Mwacidule: Mutu uyu unali kuona kulemba nkhani yapafupi yao-yao aphunzi
206
BIBLIOGRAPHY
Ministry of Education. (2023). Early Childhood Education Syllabus (3-5 Years) Level 1
– 3. Lusaka: Curriculum Development Centre
Ministry of Education. (2023). 2023 Zambia Education Curriculum Framework.
Lusaka: Curriculum Development Centre
Ministry of General Education. (2019). Early Childhood Development and Education:
Guide on Production of Low-Cost Play, Teaching and Learning Materials.
Lusaka: Directorate of Early Childhood Education.
Ministry of General Education. (2015). Early Childhood Education Teachers’ Diploma
Syllabus. Lusaka: Directorate of Teacher Education and Specialised Services.
Ministry of Education, Science, Vocational Training and Early Education. (2013).
National Literacy Framework. Lusaka: Curriculum Development Center.
Ministry of Education, Science, Vocational Training and Early Education. (2013). Early
Childhood Education Syllabi (3-6 Years) Level 1 – 3. Lusaka: Zambia
Education Publishing House.
Ministry of Education. (1977). Zambian Languages Orthography. Lusaka: National
Educational Company of Zambia (NECZAM)
Ministry of Education. (1977). Educating Our Future Policy. Lusaka: Institutional
supplier limited.
Ministry of Education. (1996). Educating Our Future: National Policy on Education.
Lusaka: ZEPH. Available at [Link]
207