Primary Literacy Programme
CINYANJA GIREDI 3
Buku la Mphunzi
Temu 1
Zambia Educational Publishing House
Lusaka
1
© Curriculum Development Centre, 2015
Edited by
Isaac G. Shawa
First published 2015 by
Zambia Educational Publishing House
Light Industrial Area
Chishango Road
P.O. Box 32708
Lusaka, Zambia
ISBN 9982-00-583-9
2022 Reprinting Funded by:
ALEMBI
Aston. K. Daka: Acting Specialist – Curriculum
Development (Cinyanja),
Curriculum Development Centre,
Lusaka.
Juziel C. Banda: Headteacher, Lumezi Day
Secondary School, Lundazi.
Adon K. Banda: Head of Department, Social
Sciences, Thornhill Boarding & Day
School, Lusaka.
Maureen Daka Manda: Head of Department, Languages,
Petauke Boarding Secondary
School, Petauke.
TEMU 1
MFUNDO YAIKULU: MAU
PHUNZIRO 1: Kuika Malembo A Alifabeti Mu
Mndandanda Woyenera
NCHITO
Ikani malemba awa mu mndandanda woyenera wa
alifabeti.
1. m , r, l, n, f
2. k, b, a, d, l
3. p, u, t, y, s
4. s, y, d
5. w, k, f, z, g
6. l, g, j
PHUNZIRO 2: Kuika Mau Mu Mndandanda
Woyenera Wa Alifabeti
NCHITO
Ikani mau mu mndandanda woyenera wa alifabeti
pogwiritsa nchito malemba oyambira.
1. wapita, dwala, khala.
2. agona, funa, coka.
3. atate, gwira, munda.
1
4. bande, atunga, lemba.
5. coipa, bwera, dzanja.
PHUNZIRO 3: Kuzindikira Mau Fanane
Werengani nkhani yotsatirayi:
Makedzana anthu amayenda ndi zibodo kupita kumalo
ena. Ici cinali cifukwa cakuti kunalibe zimbayambaya
zoyenderamo. Amatenga nthawi yaitali kufika komwe
amapita. Mnjira, kukada, amapempha malo kuti agone.
Dzuwa lisanatuluke amauka ndi kupitiriza ndi ulendo wao.
NCHITO
Pezani mau olingana matanthauzo m’nkhani yomwe
mwawerenga ndi mau awa:
1. Kale-kale
2. Miyendo
3. Malole
4. M’mamawa
5. Amagalamuka.
PHUNZIRO 4: Kuzindikira Mau Kanane
Werengani nkhani yotsatirayi ndipo m'magulu anu
muyankhe mafunso otsatira.
Abambo Chirwa anali munthu wokoma mtima. Iwo anali
kukonda kupha nyama m’thengo. Amapita ndi agalu
awo atatu kukazengera. Akapha nyama kuthengo,
2
amabwera nazo kumudzi. Aliyense m'mudzi
amamugawirako nyamazo. Anthu ambiri amawakonda
cifukwa ca cifundo cao.
NCHITO A:
Pezani mau kanane m’matanthauzo m’nkhani
mwawerenga ndi awa:
1. Amai
2. Woipa
3. M’mudzi
NCHITO B:
Mphunzi aliyense payekha apeze mau kanane ndi
awa:
1. Kuweta
2. Ang’ono
3. Nkhanza
3
MFUNDO YAIKULU: ZIGANIZO
PHUNZIRO 5: Ziganizo
ZOCITA
Werengani mau awa ndipo mupange ziganizo.
– cona
– cifukwa
– nyumba
– anathawa
– ng'ombe
– mtsikana
NCHITO A
Tsirizani ziganizo izi;
1. Buku langa ______________________________
2. Munda uyu ______________________________
3. Atate ako _______________________________
4. Amai apita ______________________________
5. Mbewa ndi ______________________________
NCHITO B
Lembani ziganizo ndi mau awa:
– wabodza.
4
1
– mtengo.
– yendetsa.
– waliwiro.
– dzanja.
PHUNZIRO 6: Ziganizo
NCHITO A
Werengani ziganizo izi zomwe ziri zosokoneza ndipo
mulembe ndime ziwiri.
– Ndiphunzira pasukulu la Dole
– Dzina langa ndine Fatima
– Mphunzitsi wamkulu ndi a Ngondo
– Ici cinacitika cifukwa ndinamunyoza
– Tsiku lina Yosefe anandimenya
– Mwendo wanga unathyoka pomwe
anandikankhira mdzenje
NCHITO B
Lembani ndime imodzi pogwiritsa nchito ziganizo izi;
– Matenda yomwe adwala ndi malungo.
– Maria adwala.
– Mawa apita ku cipatala, m’mamawa.
– Afuna kuonana ndi a Dotolo.
5
1
NCHITO C
– Ngati khoswe ali pafupi, amalumpha ndi
kum'gwira.
– Cona akonda makoswe.
– Amakhala cete kuti agwire khoswe.
– Nthawi zambiri, satsiriza khoswe yense.
– Akakhuta acita mkonono.
– Cona akagwira khoswe amadya kuyambira
ku mutu.
PHUNZIRO 7: Ziganizo
NCHITO A
Werengani ziganizo ndipo muzilembe m'ndime zitatu.
– Boma lidzafunika kukumba zitsime.
– Madzi adzabvuta.
– Caka cino mvula yacedwa.
– Anthu adzabvutikadi.
– Njala idzakula kwambiri.
– Ana ndiwo adzabvutika kwambiri.
– Mwina anthu angapulumuke.
– Boma lidzafunika kupereka cakudya.
NCHITO B
Lembani ndime ziwiri pogwiritsa nchito ziganizozi;
6
1
– Banjali ndi logwirizana.
– Ali ndi ana khumi.
– A Phiri ali ndi banja lalikulu.
– Mwana wao woyamba ndi Tamala.
– Athandiza amai ndi atate ake.
– Iyeyu agwira nchito ya udotolo
PHUNZIRO 8: Ziganizo
NCHITO A
Werengani ziganizo ziri munsimu ndipo mupange
ciganizo cimodzi pa nambala iri yonse.
1. Yosefe anali mwana wosamvera.
Yosefe anamangidwa.
2. Roidi anadwala kwambiri.
Roidi Anamwalira.
3. Maria anakwera mumtengo.
Maria anathyoka mwendo.
NCHITO B
Lumikidzani ziganizo izi;
1. Edina anali wanzeru ku sukulu.
Edina analephera mayeso.
2. Thandiwe anali kuthamanga kwambiri.
Thandiwe anatsalira pampikisano
wothamanga.
7
1
3. Caka cino mvula yacedwa.
Caka cino kudzakhala njala kwambiri.
8
MFUNDO YAIKULU: JENDA
PHUNZIRO 9: Kumvetsera Ndi Kulankhula
9
1
ZOCITA
Pangani ziganizo ndi mau awa;
bambo, amai, tambala ndi mnyamata.
PHUNZIRO 10: Mvetso
Werengani nkhani iyi:
Mitundu ya maina acimuna ndi acikazi.
Pali mitundu ya maina acimuna ndi acikazi.
Mwacitsanzo, nkhuku yaimuna ichedwa tambala.
Nkhuku yaikazi ichedwa msote. Mwana wacikazi
achedwa mtsikana pamene wamwamuna achedwa
mnyamata. Mbuzi yaimuna ichedwa tonde. Yaikazi,
yosabalapo, ndi msona. Akazi acikulire ndi amai
ndipo amuna ndi abambo. Ziweto zambiri
zimapezeka m'mapulazi ndi m'midzi.
NCHITO A
1. Kodi dzina la nkhuku yaimuna ndi ciani?
2. Mwana wacikazi achedwa ________.
3. ____ ndi akazi acikulire.
NCHITO B
Pezani maina anai cabe omwe anena za jenda ndipo
mulembe m'mabuku anu.
10
1
PHUNZIRO 11: Kulemba
Lembani ziganizo izi m'mabuku mwanu.
1. Tambala wathu ndi wamkulu.
2. Dzulo atate anagula msona kuti asunge.
3. Amai apita kumunda.
4. Mnyamata wabvala bwino.
5. Nkhawi zathu ziwiri zija zilima bwino.
6. Msote wa amai uli ndi mazira.
PHUNZIRO 12: Kuwerenga
ZOCITA A
Werengani nkhani iyi:
Mitundu ya maina acimuna ndi acikazi.
Pali mitundu ya maina acimuna ndi acikazi. Mwacitsanzo,
nkhuku yaimuna ichedwa tambala. Nkhuku yaikazi
ichedwa msote. Mwana wacikazi achedwa mtsikana
pamene wamwamuna achedwa mnyamata. Mbuzi
yaimuna ichedwa tonde pomwe yaikazi ndi msona. Akazi
acikulire ndi amai ndipo amuna ndi abambo. Ziweto
zambiri zimapezeka m'mapulazi ndi m'midzi.
ZOCITA B
Werengani mau awa:
msote tambala
11
1
mnyamata msona
amai buthu
atate nkhunzi
PHUNZIRO 13: Kubwereza, Kumvetsera Ndi
Kulankhula
ZOCITA A
Aphunzi achule maina a nyama, mbalame ndi anthu
akazi ndi amuna zomwe ziri pa Phunziro 9 m'buku la
mphunzi.
ZOCITA B
Kubwereza kuwerenga.
Werengani nkhani iyi:
Mitundu ya maina acimuna ndi acikazi.
Pali mitundu ya maina acimuna ndi acikazi. Mwacitsanzo,
nkhuku yaimuna ichedwa tambala. Nkhuku yaikazi
ichedwa msote. Mwana wacikazi achedwa mtsikana
pamene wamwamuna achedwa mnyamata. Mbuzi
yaimuna ichedwa tonde pomwe yaikazi ndi msona. Akazi
acikulire ndi amai ndipo amuna ndi abambo. Ziweto
zambiri zimapezeka m'mapulazi ndi m'midzi.
12
1
MFUNDO YAIKULU: UMOYO
PHUNZIRO 14: Kumvetsera Ndi Kulankhula
13
1
PHUNZIRO 15: Mvetso
Nkhani
Munthu aliyense afunika kudzisamala. Tingadzisamale
m'njira zosiyana-siyana. Madzi akumwa afunika kuphitsa
kupha tizilombo. Tikacoka kucimbudzi tifunika kusamba
m'manja. Zobvala zifunika kuchapa ndi sopo. Komanso
aliyense afunika kusamba mthupi. Tikatero tidzapewa
matenda ndipo ku cipatala sitidzapitako.
Mafunso
1. Kodi nkhani iyi ikamba zaciani?
2. Kodi tizilombo ta m'madzi timadzetsa ciani ku
anthu?
3. Aliyense afunika kusamba m'manja ngati
wacoka kuti?
4. Kodi ku cipatala timapezako ciani?
A. Tizilombo.
B. Mankhwala.
PHUNZIRO 16: Kulemba
NCHITO A
Lembani ziganizozi moyenera.
1. Munthualiyenseafunikakudzisamala.
2. Madzindiyofunikirapodzisamala.
14
1
NCHITO B
Ikani mipata pakati pa mau ali m'ziganizo zotsatirazi.
1. Tikacokakucimbudzi tifunikakusamba
m'manja.
2. Zobvala zifunikakuchapa ndisopo.
3. Aliyenseafunika kusambamthupi
masikuonse.
PHUNZIRO 17: Kuwerenga
Werenga nkhani iyi:
Munthu aliyense afunika kudzisamala. Pali njira zosiyana-
siyana zodzisamalira. Pa nyumba pafunika cimbudzi.
Madzi yakumwa yafunika kukhala yaukhondo. Zobvala
zifunika kuchapidwa nthawi zonse. Tikatero tidzapewa
matenda.
PHUNZIRO 18: Kubwereza
Werengani zotsatirazi:
Ukhondo ukasowekera, matenda yamafala. Pofuna
kupewa matenda, aliyense afunika kugwapo. Tifunika
kugwiritsa nchito zimbudzi ndi sopo. Malo okhalapo
afunika kusesedwa nthawi zonse. Tikatero tidzapewa
matenda.
15
MFUNDO YAIKULU: CITETEZO CA PA MSEU
PHUNZIRO 19: Kumvetsera Ndi Kulankhula
Njira yodzitetezera pa mseu.
PHUNZIRO 20: Mvetso
– Kupewa - pa mphambano
– Utoto - Cenjezo
Munthu ngati adutsa mseu akhale ocenjera popewa
ngozi. Miseu yomwe magalimoto ayendamo nthawi ndi
nthawi, maloboti amaikidwa pa mphambano. Maloboti
awa amaonetsa utoto wosiyana-siyana pakapita nthawi.
Utoto uliwonse uli ndi tanthauzo lake. Utoto ofiira ndiye kuti
16
1
galimoto lisadutse mseu. Utoto wa msipu ndiye kuti
galimoto lingadutse mseu. Utoto wa lalanje ndi cenjezo
kuti posacedwa utoto ungasinthe.
NCHITO
1. Kupewa ndi ku___________
2. Kodi cifukwa ndi ciani amaika maloboti
pa mphambano pa mseu?
3. Maloboti ngati yaonetsa utoto wa lalanje
ndiye kuti_____________
4. Kudutsa ndi ________
PHUNZIRO 21: Kulemba
Werengani nkhani iyi:
Munthu ngati adutsa mseu akhale ocenjera popewa
ngozi. Miseu yomwe magalimoto ayendamo nthawi ndi
nthawi, maloboti amaikidwa pa mphambano. Maloboti
awa amaonetsa utoto wosiyana-siyana pakapita nthawi.
Utoto uliwonse uli ndi tanthauzo lake. Utoto ofiira ndiye kuti
galimoto lisadutse mseu. Utoto wa msipu ndiye kuti
galimoto lingadutse mseu. Utoto wa lalanje ndi cenjezo
kuti posacedwa utoto ungasinthe.
NCHITO
Lembani ziganizo zitatu zomwe ziri ndi mau awa; ofiira,
msipu ndi lalanje kucokera m'nkhani iri pa mwambapa.
PHUNZIRO 22: Kuwerenga
17
1
ZOCITA
Werengani nkhani iyi:
Munthu ngati adutsa mseu akhale ocenjera. Popewetsa
ngozi m'miseu ikulu-ikulu muli maloboti pa mphambano.
Maloboti awa amaonetsa utoto wosiyana-siyana
pakapita nthawi. Utoto uli wonse uli ndi tanthauzo lake.
Utoto ofiira utanthauza kuti galimoto lisadutse. Utoto wa
lalanje ndi cenjezo kuti utoto udzasintha posacedwa.
PHUNZIRO 23: Kubwereza
Bwerezerani Phunziro la 20 ndi la 22.
18
1
MFUNDO YAIKULU: MALO OKHALAMO
PHUNZIRO 24: Kumvetsera Ndi Kulankhula
19
1
PHUNZIRO 25: Mvetso
Malo okhalamo.
Malo okhalamo afunika kusamalidwa masiku onse.
Cisamaliro ciri mosiyana-siyana. Tiyenera kupsera ndi
kukolopa cipinda cogonamo. Tiyenera kukonza pamalo
pomwe tigona poyanza zofunda. Ici cimathandiza
cifukwa ngati pali tizilombo toluma timaticotsapo. Ici
cimathandiza kuti malo omwe tigonapo azikhala
aukhondo.
NCHITO A
Kuyankha mafunso:
1. Chulani njira ziwiri zomwe tingacite kuti tisamale
malo okhalamo.
2. Nanga malo ogonapo tiyenera kuwasunga
motani?
3. Kodi tizilombo timadzetsa ciani?
4. Kodi ndani afunika kusunga malo ogonamo
mwaukhondo?
NCHITO B
Yankhani mafunso awa:
Perekani matanthauzo a mau awa:
a. Cipinda.
b. Kuyanza.
20
1
PHUNZIRO 26: Kulemba
NCHITO A
Lembani ziganizo izi:
1. Malo akhalamo afunika kusamaliridwa masiku
onse.
2. Tifunika kubzala maluwa ndi kapinga.
3. Tikabzala, tifunika kuthirira masiku onse.
NCHITO B
Lembani ziganizozi moyenera:
1. amai ndiatate ali kulima.
2. Mateyo watayazinyalala m’cibekete.
3. Tifunika kusamalamalo okhalapo.
PHUNZIRO 27: Kuwerenga
Malo okhalamo.
Malo okhalamo afunika kusamalidwa masiku onse.
Cisamaliro ciri mosiyana-siyana. Tiyenera kupsera,
kukhwapa udzu ndi kuwola zinyalala. Tifunikanso kubzala
maluwa ndi kapinga. Tikabzala, tifunika kuthirira masiku
onse.Tikatero, tidzapewa matenda.
21
1
PHUNZIRO 28: Kubwereza
Malo Okhalamo.
Malo okhalamo afunika kusamalidwa masiku onse.
Cisamaliro ciri mosiyana-siyana. Tiyenera kupsera,
kukhwapa udzu ndi kuwola zinyalala. Tifunikanso kubzala
maluwa ndi kapinga. Tikabzala, tifunika kuthirira masiku
onse. Tikatero, tidzapewa matenda cifukwa malo
adzakhala aukhondo.
NCHITO A
Kuyankha mafunso.
1. Chulani njira ziwiri zomwe tingacite kuti tisamale
malo okhalamo.
2. Nanga malo okhalamo afunika kukhala otani?
3. Tikabzala maluwa ndi kapinga, tifunika kucita
ciani?
4. Kodi ndi cifukwa ciani tisamalira pa malo
okhalapo?
NCHITO B
Kulemba.
Pangani ziganizo ndi mau awa:
i. zinyalala.
ii. maluwa.
iii. cipserero.
22
1
MFUNDO YAIKULU: KUNZUNZA ANA
PHUNZIRO 29: Kumvetsera Ndi Kulankhula
PHUNZIRO 30: Mvetso
Werengani nkhani yotsatirayi ndipo muyankhe mafunso
yotsatira.
Nkhani
Kawiri-kawiri ana amanzunzidwa ndi anthu osiyana
-siyana. Ena mwa anthuwa ndi acibale.
Mwana wonzunzidwa akula mokwinyirira. Ngakhale
kusukulu sacita bwino ai. Maganizo yamamuculukira.
23
1
Mwana ngati anzunzidwa afunika kudziwitsa ena. Aliyense
wodziwa za izi, angathe kupereka lipoloti. Malipoloti
yangaperekedwe kwa apolisi ndi atsogoleri ena.
NCHITO
Mafunso
1. Kodi ndi zoona kapena ai kuti mwana
anganzunzidwe ndi atsibweni ake?
2. Perekani cifukwa comwe mwana wonzunzidwa
akulira mosakondwa.
3. Chulani magulu atatu cabe omwe angalandire
malipoloti ya ana onzunzidwa.
PHUNZIRO 31: Kulemba
NCHITO
Tsirizani ziganizo zotsatirazi moyenera.
1. Kupatsa______nchito yopitirira msinkhu____ndi
kunzunza_______.
2. ______afunika kusunga bwino ana ao kuti
asamakula________.
3. Onse _____ana afunika kumangidwa.
4. ______tifunika kuonetsetsa kuti palibe yemwe
_____mwana m'malo momwe tikhala.
24
1
PHUNZIRO 32: Kuwerenga
ZOCITA
Werengani nkhani iri pa phunziro la 30 (Mvetso),
m'mabuku mwanu.
PHUNZIRO 33: Kubwereza
NCHITO
1. M'magulu mwanu, fotokozani momwe ana
anzunzikira ndi momwe kunzunzikaku kungathere.
2. Lembani ciganizo cimodzi cabe conena
momwe mwana anganzunzidwire kapena
zomwe mwana angacite ngati ali kunzunzidwa
25
MFUNDO YAIKULU: ZOKONDWERETSA NDI
ZOKHUMUDWITSA
PHUNZIRO 34: Kumvetsera Ndi Kulankhula
26
1
PHUNZIRO 35: Mvetso
Pali zinthu zambiri zimene zimakondweretsa anthu. Ena
amakondwera akapita kukaonerera magule. Magule
amakhala osiyana-siyana. Pali magule monga nyau,
ngoma, vimbuza ndi ena. Wopita kumagulewa
amakhala wokondwera cifukwa amakumana ndi
kuonana ndi anzao.
Nthawi zina anthu amakhala wokhumudwa. Ici ndi
cifukwa cakuti mwina pamudzi pamakhala matenda
kapena imfa. Izi sizimakondweretsa anthu cifukwa cakuti
munthu watisiya.
NCHITO
Tsopano yankhani mafunso yotsatira.
1. Anthu ena amakondwera akapita_________.
2. Mitundu ya magule atatu amene achulidwa
ndi awa:
a) __________________
b) __________________
c) __________________
3. Kodi cifukwa ndi ciani munthu wopita
kumagule amakhala wokondwera?
4. Anthu amakhala wokhumudwa pamudzi
cifukwa________________.
5. Tikati munthu watisiya titanthanza kuti ______.
27
1
PHUNZIRO 36: Kulemba
Pali zinthu zambiri zimene zimakondweretsa anthu. Ena
amakondwera akapita kukaonerera magule. Magule
amakhala osiyana-siyana. Pali magule monga nyau,
ngoma, vimbuza ndi ena. Wopita kumagulewa
amakhala wokondwera cifukwa amakumana ndi
kuonana ndi anzao.
Nthawi zina anthu amakhala wokhumudwa. Ici ndi
cifukwa cakuti mwina pamudzi pamakhala matenda
kapena imfa. Izi sizimakondweretsa anthu cifukwa cakuti
munthu watisiya.
NCHITO
We r e n g a n i n k h a n i i r i p a m w a m b a p a n d i p o
mukatsiriza citani nchito iyi;
1. Lembani ziganizo ziwiri, cimodzi cokhudza
zokondweretsa ndi cina cokhudza
zokhumudwitsa.
a) _________________
b) _________________
PHUNZIRO 37: Kuwerenga
ZOCITA
Werengani nkhani iyi mosiyirana-siyirana:
Pali zinthu zambiri zimene zimakondweretsa anthu. Ena
amakondwera akapita kukaonerera magule. Magule
28
1
amakhala osiyana-siyana. Pali magule monga nyau,
ngoma, vimbuza ndi ena. Wopita kumagulewa
amakhala wokondwera cifukwa amakumana ndi
kuonana ndi anzao.
Nthawi zina anthu amakhala wokhumudwa. Ici ndi
cifukwa cakuti mwina pamudzi pamakhala matenda
kapena imfa. Izi sizimakondweretsa anthu cifukwa cakuti
munthu watisiya.
PHUNZIRO 38: Kubwereza
ZOCITA
Bwerezani kuwerenga nkhani iri pa Phunziro 37.
29
1
MFUNDO YAIKULU: ULAMULIRO
PHUNZIRO 39: Kumvetsera Ndi Kulankhula
30
1
PHUNZIRO 40: Mvetso
Werengani nkhani iri munsimu:
MALAMULO
Pamalo pomwe tikhala pali malamulo. Anthu saloledwa
kudula mitengo cidule-dule. Salola kutaya zinyalala pali
ponse. Salola munthu kucitira cimbudzi kuthengo
koma mcimbudzi. Salola ana acicepere kulowa
m'mabawa. Salola malo omwe ziweto zidyerako
kumangako nyumba. Salola anthu kuyenda usiku.
NCHITO
Yankhani mafunso awa:
1. Kodi pamalo pomwe tikhala pali ciani?
2. Anthu saloledwa kudula ______cidule-dule.
3. Chulani lamulo limodzi cabe.
4. Kodi ana acicepere sayenera kutani?
5. Salola munthu kucita cimbudzi_______.
6. Salola malo omwe ______zidyera kumangako
nyumba.
7. Salola_____kuyenda usiku.
31
1
PHUNZIRO 41: Kulemba
NCHITO
Lembani ndi kuika mau osowa mziganizo izi:
1. Salola munthu kulima_______wamwini wake.
2. Salola ana kupezeka m'malo omwera ______
3. Salola ______ kukwatiwa akali wacicepere.
4. Salola anthu kutaya __________ pali ponse.
PHUNZIRO 42: Kuwerenga
Werengani nkhani iyi:
MALAMULO
Pamalo pomwe tikhala pali malamulo. Anthu saloledwa
kudula mitengo cidule-dule. Salola kutaya zinyalala pali
ponse. Salola munthu kucitira cimbudzi kuthengo,
koma mcimbudzi. Salola ana acicepere kulowa
m'mabawa. Salola malo omwe ziweto zidyerako
kumangako nyumba. Salola anthu kuyenda usiku.
PHUNZIRO 43: Kubwereza
Werengani nkhani iri pa Phunziro 42 mofulumira.
32
1
MFUNDO YAIKULU: JENDA
PHUNZIRO 44: Kumvetsera Ndi Kulankhula
PHUNZIRO 45: Mvetso
NCHITO
Werengani nkhani yotsatirayi mwakacete-cete ndipo
muyankhe mafunso otsatira.
Nkhani
Cilengedwe cipatula nchito zina. Mwacitsanzo,
mwamuna sangayamwitse mwana ai. Koma kuphika ndi
kuphunzitsa, aliyense angacite. Aliyense angakhale
msirikali, nesi kapena makanika.
33
1
Miyambo ndiyo iletsa nchito zina. Mkazi angamange
nyumba. Ife tifunika kudziwa tanthauzo la jenda.
Mafunso
1. Kodi ndiciani ciletsa mwamuna kuyamwitsa
ana?
2. Mwamuna angambereke mwana, koma
satero cifukwa ca ____________.
3. Kodi miyambo ndi ciani?
4. Nanga jenda ndi ciani?
PHUNZIRO 46: Kulemba
A) Tsirizani ziganizo zotsatirazi moyenera.
1. Mwamuna anga _____________
2. Mkazi anga __________________
3. Yosefe sanga ________________
4. Jelita sanga _________________
B) Onetsani mipata pakati pa mau mziganizo izi;
1. Mkazikapenamwamunaangaphike.
2. Mtsikanakapenamnyamataangatsukembale.
3. Mwamunakapenamkaziangakhalemtsogoleri.
34
1
PHUNZIRO 47: Kuwerenga
Werengani nkhani yomwe iri pa Phunziro 45 (Mvetso)
m'mabuku mwanu.
PHUNZIRO 48: Kubwereza
Fotokozeranani nchito zomwe zingagwiridwe ndi amuna
kapena akazi koma siziritero m'madera momwe
mukhala.
35
1
MFUNDO YAIKULU: MAYESO AKUTHA
KWA TEMU
36
1