MACHINGA DISTRICT SECONDARY SCHOOLS
2022 MALAWI SCHOOL CERTIFICATE OF EDUCATION MOCK EXAMINATION
CHICHEWA PAPER III
MARKING SCHEME
1. a) Mwamuna amene akuyamikira, kukhumbira mkazi (1)
b) Akudziyankhulira yekha (1)
c) Akufotokoza za kukongola kwa mkazi / akufotokoza zomwe zimachitika akawona
mkaziyu (1)
d) - Kayankhulidwe / kamvekedwe koyamikira
Kapena
- Kayankhulidwe / kamvekedwe ka chikondi (chimodzi mwa icho (1))
e) (i) Mimvekero: myu, ndee, ndii, thi thi thi. (2)
(ii) Zifanifani: akakufulatira ngati akukuyang’ana
Akamayenda ngati akunjanja
Akamapita ngati akubwera kuno
Akamayankhula ngati akuyimba
Maso ake oyera ngati mpunga
Mano ake oyera ngati mkaka
Tsitsi la mzindo ngati chiyabwe
(iii) Zining’a: Chiphadzuwa
Nduke
f) (i) Mkazi wokongola (1)
(ii) Namalenga / chauta (1)
g) - Kuyamikira /
- Kusonyeza chikondi (2)
2.
a) Ku tawuni
b) Gehazi akukaniza Namayile kutenga katundu
c) (i) Samamusakira / samampatsa chakudya
(ii) Amabwera mochedwa kuchokera ku mowa
(iii) Kumukaniza Namayile kutenga katundu
Page 1 of 3
d) Anamkaniza mkazi wake kutenga katundu munthu woti anavutika kuti katunduyo
agulidwe
e) Zipangizo monga
(i) Chining’a – mwana wakana phala
Adadulitsa mutu wazizwa
(ii) Chibwereza cha mawu – Namayile, Gehazi
f) Mawu otsutsana m’matanthauzo
i. Kudanitsa – kuyanjanitsa
ii. Ulemelero – umphawi
iii. Adakondwera – adadandaula
g) Phunziro: Nkhanza ndi zoipa
3. NTHONDO
a) Makhalidwe oipa a chinyamata cha Nthondo ndi zitsanzo zake.
i. Ndewu ku dambo
ii. Kuba
iii. Bodza
iv. Ulesi
b) Kudalirana kwa atengambali
i. Nthondo amadalira amalume ake kumpatsa chakudya atate ake atamwalira
ii. Mayi a Nthondo amadalira anzawo kuwapatsa chimera cha mowa
iii. Anthu a m’mudzi amadalira mfumu Nthondo kuwapatsa chakudya
iv. Anthu amadalira Nthondo kubweretsera sukulu
v. Anyamata ochokera ku Harare amadalira Nthondo kuwagulira chakudya mnjira
4. a) Mudzi wa Mfumu Tandwe udali wadongosolo
i. Mfumu Tandwe simagwira yokha ntchito
- Idagawira nduna zake zochita ndipo nduna iliyonse imagwira ntchito yake
molumikizana ndi akuluakulu a m’malimana
- Pamsonkhano aliyense amatsatira ndondomeko poyankhula
ii. Chikondi
- Mayi Padengu adapita kukazonda amuna awo kundende ngakhale adamangidwa
kaamba kogwirira mwana wawo womupeza
Page 2 of 3
- Atsogoleri a m’mudzi mwa mfumu Tandwe adathetsa miyambo yakale yamakolo
yoipa monga kulowa kufa, chokolo komanso kupondereza azimayi
iii. Kusasalana
- Anthu a mudzi wa a Tandwe anali osiyana zipembedzo ndi mitundu koma
ankapita ku sukulu ndi chipatala cha mpingo wosiyana ndi chipembedzo chawo.
iv. Kuganiza mwakuya
- Amfumu amayitanitsa gulu la ovina monga amayi ndi atsikana komanso abambo
ndi anyamata a kanada pambuyo pa zoyankhula za nduna
- Izi zimathandiza anthu kuti asatope kaamba ka kutalika kwa msonkhano
- Komanso zomapereka mpata kwa woyankhula kuti akonzekere.
b) Mchira wa buluzi
i. Nadzonzi amachita uve pakhomo pake; osasesa, osachapa
ii. Anali waulesi
- Amalephera kuphikira banja lake
- Bambo Ndileya ndi ana amakhala ndi njala
iii. Wamiseche
- Amakhalira kupita kocheza kwa anzake ndi kumachita miseche ndi anzake monga
Nasiwelo
iv. Amakapempha mankhwala a “kondaine” kwa Nasiwelo mmalo mosintha makhalidwe
ake a pakhomo
v. Amamvera zokamba za anthu ena nkumayesa kupeza njira zofuyira Ndileya mmalo
mozindikira kuti mwamuna m’pamimba.
MAYANKHO ATHERA PANO
Page 3 of 3