EXAMINATION NUMBER: ________________________________________________
CENTRAL EAST EDUCATION DIVISION
2023 MALAWI SCHOOL CERTIFICATE OF EDUCATION
MOCK EXAMINATIONS
CHICHEWA
Wednesday, 29th March Subject Number: M032/III
Time Allowed: 2 hours
(8:00 a.m.-10:00 a.m.)
PAPER III
(Malikisi 70)
Malangizo
1. Onetsetsani kuti pepala ili lili ndi Question Tick if Do not write in
Number answered these columns
masamba osindikizidwa asanu ndi
1
anayi.
2
2. Pepalai lili ndi magawo awiri
3
3. M’gawo A: Yankhani mafunso onse.
(Malikisi 30) 4
4. M’gawo B: Yankhani mafunso awiri 5
okha. (Malikisi 40) 6
5. Lembani dzina kapena nambala 7
yanu pamwamba pa tsamba lililonse
loyankhirapo.
6. Muchitebulo chilli kumbalichi onetsani funso lililonse lomwe mwayankha
pochonga mubokosi lomwe lili kutsogolo kwake.
7. Perekani pepalali kwa oyang’anira mayeso nthawi ikakwana.
@ 2023 CEED MOCK TURN OVER!
Page 1 of 9
EXAMINATION NUMBER: ________________________________________________
Gawo A (Malikisi 30)
Nkhani za Mchezo ndi Zolembedwa
Langizo:Yankhani mafunso onse m’gawoli.
1. Werengani ndakatulo il im’munsiyi ndipo muyankhe mafunso otsatirawo.
Nkhuyu zomwe adadya akulu (I.D. Zabuloni)
Monga n’kuterodi kodi makolonu?
Kutichotsa anafe m’chiwaya,
N’kumatinyeketsa m’nthukuta ya dzuwa,
Mutasinthitsa nyengo idali yokometsetsa, yachikondi,
Podzitchukitsa ndi nkhwangwa zotafuna mitengo
Mwa kang’oma kolira, kong’ambika msanga?
Eyadi, mnzanga walasa, tatiyankheni makolo.
Mudatani kudzikanganula ku chilengedwe,
Monga matowo okhwima, akupsa?
Kuthawitsa nkhalango n’kuvula nthaka
M’chimbulimbuli mwa kusadziwa n’kufadi,
Ponyengedwa n’kanyama kotchedwa chitukuko?
Ananu, mtheradi khuzumukani, m’salalamuke.
Mudziwa utsi ukalowa kudzenje,
Make mbewa naye amafa nawo.
Chidzuwa chikukomola tonsefe.
Monga kupha nyani tsono, chidzuwachi
Sichikuyang’ana nkhope, ata!
Tidanyengedwa kudyadi gaga makolofe;
Poti mphuno salota, maso kumbuyo kulibe.
M'liyenda tidakaonamo agalu amichombo
Adatiuzako, ‘katsekuleni minda, kameteni mapiri;
Katipuleni madambo, kagwetseni misinyika.
Page 2 of 9
EXAMINATION NUMBER: ________________________________________________
Mukakolola phwamwamwa, chaka chikamakatsendera.
M’satinamize makolo, poti chala m’daluma dala,
Kuti anafe phala la kwa Mphambe tisamwe.’
Tizizunzika m’mbonaona za zivomerezi, napolo
Kutentha udyo kwa dzuwa; kung’aluka kwa nthaka.
Zonsezi n’kukhala nkhuyu zomwe mudadya tisanabadwe,
Zikutipota anafe, mwa udzu wofa njovu zikamayambana.
Tsopano yankhani mafunso otsatirawa.
a. Kodi oyankhula mu ndime ziwiri zoyambazo ndani?
......................................................................................................................
.................................................................................................(Malikisi 1)
b. Ndi chiyani chimene chakhudza kwambiri oyankhula mu ndime ziwiri
zoyambazo?
......................................................................................................................
......................................................................................................................
..................................................................................................(Malikisi 2)
c. Tsimikizani kuti kuyankhula kwa oyambawo kukusonyeza mtafu.
......................................................................................................................
......................................................................................................................
..................................................................................................(Malikisi 2)
d. Nanga oyankhulidwawa akusonyeza bwanji kuti zomwe adachitazo
gwero lake n’kusazindikira?
......................................................................................................................
......................................................................................................................
..................................................................................................(Malikisi 2)
e. Perekani zitsanzo ziwiriziwiri zopezeka m’ndakatuloyi za zipangizo
zotsatirazi:
Page 3 of 9
EXAMINATION NUMBER: ________________________________________________
i. Faniziro:
1.........................................................................................................
2. ........................................................................................................
ii. mkuluwiko:
1. ....................................................................................................
2.........................................................................................................
(Malikisi 4)
f. Fotokozani kamvekedwe ka ndakatuloyi.
………………………………………………………………......................
.................................................................................................(Malikisi 1)
g. Pezani chitsanzo cha mvekero mu ndakatuloyi.
..................................................................................................(Malikisi 1)
h. Perekani phunziro lalikulu lopezeka m’ndakatuloyi.
......................................................................................................................
......................................................................................................................
......................................................................................................................
................................................................................................. (Malikisi 2)
2. Werengani nkhani ili m’munsiyi mosamala ndipo muyankhe mafunso
otsatirawo.
KUCHOKA SI KOMA UKU (I D ZABULONI)
“Ndithudi, achikhala ana onse amachoka chotere pasukulu, tikadamati uphunzitsi ndi ntchito
yolemekezeka. Sindiko kutsanzika nanga uku? Eti pochoka kumangotaya phunzo, zipangizo
za sukulu zikulira mayomayo ndi nkhalwe za apuludzu ena akamaliza mayeso? Matsano
waperekadi phunziro losaiwalika kwa tonsefe kuti pamsasa saipitsa.” Adanena mawuwa ndi
aphunzitsi a Kavungu akusetekera m’manja momwe mudali noninoni ndi nyama yabakha.
Amavomerezana ndi amayi Kamzingeni, aphunzitsi amene amayang’anira ana ogonera
pasukulu pomwepo.
Page 4 of 9
EXAMINATION NUMBER: ________________________________________________
Kutangotsala masiku owerengeka kuti mayeso a JC ayambike, Matsano adalawira kuti
akatenge tinan’tina kunyumba.Chilolezo adachipeza koma sadaululire aliyense kuti amapita
kukakonzekera phwando loti akatsanzikire anzake a Fomu 2 ndi aphunzitsi ake omwe.
Atafika kumudzi makolo ake adawolowa manja pokhala amlerankhungwa, namupatsa zonse
iye adazipempha. Padali zogalikagalika, zokukuta, zokulumunya komanso nyonso ena amati
malirom’mbale. Atasonkhanitsa zonse adabwerera kusukulu.
Tsiku limene adangofika kusukulu adadzidzimutsa mutu wasukulu, aphunzitsi ake onse ndi
ophunzira anzake a Fomu 2 powaitana ku phwando lachikhadzakhadza.
Sadaiwalenso atsogoleri awo a makalasi akumtunda. Adawauza kuti m’mawa mwake
akasonkhane m’chipinda china chokulirapo (multi-purpose hall) kuti akazunzeko mano ndi
matupi awo. Adabwereka chilimba kuti chikakutumule nyimbo za m’makaseti kuti a
mafupa osagwirana akadzithyoleko.
Ahedi poyamba adanyozera namati zawana safuna. Koma popeza chokoma chifumira ku
dzira, adakwawirako. Zimene adakaziona mpaka lero sakutha kusimba. Matsano
adawadulitsa mutu wazizwa. Kudali kudya ndi kumwerera zoziziritsa kukhosi popeza
zowawa ndi apongozi asukulu.
Potsiriza Matsano adati, “Ahedi, amama wotiyang’anira, aphunzitsi nonse ndi ana anzanga.
Poti kamawa sikadziwika in ndi mmene ndidapitira kumudzi kuti mukadziwe momwe
makolo anga amakulemekezerani.Pepani ndakuvutitsani popeza zoterezi pano sizichitika ayi.
Mayeso tilembadi, koma popeza mtima wa wina ndi tsidya lina, sindidziwa kuti ndidzaoloka
nawo. Ichi ndi chifukwa chake ndingosiyako fungo lokha, mwina sim’kandionanso. Ine
koma chikhulupiriro ndicho chilipo choti ndidzakhoza koma mwina anzangawa ndiwo
akalembe pamapepala onyowa, inki ikasungunuka. Ndidzafunanso amenewa
azikandikumbukira. Aphunzitsi angawa a Chichewa ndi masamu amakonda kundichdzera
poti ndine kuseri kwa mphika. Amenewa ndiwo n’datengera bakhayu kuti apeze pena
pochedzera.” “Ahedi, zikomo kuti ndinu kudzala. Enafe tikadachoka kalekale. Kwa anzanga
Page 5 of 9
EXAMINATION NUMBER: ________________________________________________
chikhalidwe chozunza obwera kumene mumati n’kuwachenjeretsa muchepetse. Anzanu
asamakhale mwa ufulu wang’ombe womakweteza mchira.Zikomo.”Pamapeto penipeni
padali fumbi, ali m’mwana agwiritse, nyimbo zikulikitika. Aphunzitsi a Kavungu, adangoti
kwakwalala, chinyophiro cha bakha chilli m’manja.
Tsopano yankhani mafunso otsatirawa.
a. Nkhaniyi ikuchitikira kuti?
___________________________________________________________

(Malikisi 1)
b. Perekani mphendero ya nkhaniyi.
___________________________________________________________
(Malikisi 1)
c. Ndi khalidwe lotani limene makolo ake a Matsano adaonetsa kwa mwana
wawo?
___________________________________________________________
________________________________________________(Malikisi 1)
d. Tsimikizani popereka mfundo imodzi kuti Matsano adachita bwino
pokonza phwando lotsanzikana ndi anzake komanso aphunzitsi ake.
___________________________________________________________
(Malikisi 2)
e. Tsimikizani popereka mfundo imodzi kuti makolo ake a Matsano adali
ofunda m’manja.
___________________________________________________________
________________________________________________ (Malikisi 2)
f. Kuchokeram’nkhaniyi, perekani chitsanzo chimodzi cha zipangizo
zotsatirazi:
i. mvekero :____________________________________(Malikisi1)
ii. chiyerekezo___________________________________(Malikisi1)
Page 6 of 9
EXAMINATION NUMBER: ________________________________________________
iii. mkuluwiko____________________________________(Malikisi 1)
g. Perekani matanthauzo a nsinjiro za Chiyankhulo izi:
i. apuludzu _____________________________________(Malikisi1)
ii. adawadulitsa mutu wazizwa______________________(Malikisi1)
iii. ufuluwa ng’ombe omakweteza m’chira
_____________________________________________(Malikisi1)
h. Perekani phunziro lalikulu lopezeka m’nkhaniyi.
____________________________________________________________
____________________________________________________________
(Malikisi 2)
Gawo B (Malikisi 40)
Langizo: Yankhani mafunso awiri okha m’gawoli m’ndime zofotokozedwa
bwino.
NTHONDO (S J Nthala)
a. Tsimikizani kuti “Mvula ikakuona litsiro siikata” popereka mfundo zinayi
malingana ndi zomwe zidamuchitikira Nthondo pa maulendo ake.
(Malikisi 20)
KAPENA
b. Fotokozani mfundo zinayi zomveka bwino sonyezani kuti m’bukuli muli
mgwirizano pochita zinthu. (Malikisi 20)
_________________________________________________________________________

Page 7 of 9

CHAMDOTHE NDI ZISUDZO ZINA (W Nkhoma, S Likongwe)
CHAMDOTHE
a. Tsimikizani popereka mfundo zinayi kuti atengambali ena ali ndi chikondi
m’chisudzochi. (Malikisi 20)
KAPENA
ZIKANI
b. Fotokozani mfundo zinayi zosonyeza makhalidwe a bwino a Zikani.
(Malikisi 20)
Page 8 of 9

MAFUNSO ATHERA PANO!
NB: Pepala ili lili ndi masamba osindikizidwa khumi.
Page 9 of 9